Uthengawu ulinso mu Chingerezi


betpawa Malawi - Cookies Policy


Chiyambi

Mukamafuna kulowa, kapena mukalowa pa tsamba la betPawa kudzera pa intaneti kapena pulogalamu yathu ya foni ya m’manja (app) yomwe imagwiritsidwa ntchito ndi Kuwina Limited, omwe ali ndi chilolezo choyendetsa betPawa ku Malawi, kapena mukachita nawo zinthu kapena kugwiritsa ntchito zomwe timapeleka, timagwiritsa ntchito (ndiponso timalora ena kugwiritsa nawo ntchito) mawebusayiti oyang’anira ma cookies, ma pixel tags, ma script, ma tag, ma API ndi ukadaulo wina (Ukadaulo wofufuza zochitika, Tracking Technologies).


Ukadaulo wofufuza zochitikawu umatilola kuti tizisonkhanitsa zambiri zokhudza inu ndi momwe mumachitira pa intaneti, komanso chipangizo chanu (mwachitsanzo kompyuta yanu kapena foni yam'manja), kuti tikuthandizeni kugwiritsa bwino ntchito tsamba lathu la webusayiti komanso pa pulogalamu (App) yathu, kusintha momwe webusayiti ndi pulogalamu (App) yathu zimagwirira ntchito, komanso kukonza zomwe mumakumana nazo pa webusayiti ndi pulogamu (App) yathu kuti zigwirizane ndi zomwe mumakonda. Timagwiritsanso ntchito uthengawu kuti tisonkhanitse ziwere2sasgero (statistics) zokhudza momwe webusayiti ndi pulogalamu (App) yathu zikugwiritsidwra ntchito, kuchita kafukufuku, kupereka zomwe zikugwirizana ndi zomwe mumakonda, komanso kuyang'anira ntchito zomwe timapereka kwa ogwiritsa ntchito athu, otsatsa malonda (advertisers), ofalitsa (publishers), makasitomala ndi anzathu othandizana nawo kugwira ntchito.


Timathandizanso ena (mabungwe kapena anthu) kuti asonkhanitse zambiri zokhudza inu pogwiritsa ntchito ukadaulo wofufuza zochitika zanuwu.


Kuti mudziwe zambiri za momwe timasonkhanitsira komanso momwe timagwiritsira ntchito uthenga wanu waumwini/wachidziwitso (personal data), chonde werengani ndondomeko yathu yachinsinsi (privacy policy).


Kodi ma cookies ndi chiyani?

Ma cookies ndi zolembedwa (files) zazing’ono zingo’no zomwe zimasungidwa (omwe amakhala ndi zilembo ndi manambala okha) omwe seva ya pa intaneti imasunga pa kompyuta yanu kapena foni yanu mukamachezera tsamba lawebusayiti. Mukamagwiritsidwa ntchito, cookie imathandiza kupanga tsamba lathu lawebusayiti ndi pulogalamu (App) kukhala yosavuta kugwiritsa ntchito, mwa chitsanzo, posunga zomwe mumakonda monga chilankhulo kapena makonda anu ena. Mutha kupeza zambiri zokhudza ma cookies pa tsamba ili www.allaboutcookies.org.


Ma cookies amagwiritsidwa ntchito kwambiri kuti masamba a intaneti azigwira ntchito bwino. Kugwiritsa ntchito ma cookies kumathandiza kusonkhanitsa zambiri zokhudzana ndi momwe mukugwiritsira ntchito tsamba, kuti muzitha kuyenda pakati pa masamba mosavuta. Ma cookies amasunga zambiri monga dzina la browser yomwe mukugwiritsa ntchito, dzina la domain, adiresi ya IP, zambiri za dongosolo la kompyuta (operating system), tsiku ndi nthawi yomwe munachezera, masamba omwe munawona, komanso zambiri zofanana ndi izi. Zonsezi zimathandiza kuti tsamba lizikumbukira zomwe mumakonda, ndikupangitsa kugwiritsa ntchito tsamba lathu ndi App kukhala kosavuta komanso kogwira bwino ntchito.


Ma cookies amagwiritsidwanso ntchito kutsimikizira kuti ma advertisement kapena malonda omwe mumawona pa intaneti akugwirizana ndi zomwe mumakonda komanso zomwe mumakonda kufufuza.



Kusungidwa kwa njira zamakono zotsatira (Storing Tracking Technologies)


Timakhala ndi ukadaulo otsatira (Tracking Technologies) nthawi yomwe mumayendera kapena kugwiritsa ntchito Tsamba lathu lawebusayiti kapena App — matekinoloje awa amatchedwa “First Party Tracking Technologies.” Kuphatikizapo, pali maukadaulo ena omwe amasungidwa ndi magulu ena akunja (monga omwe amapereka mautumiki a kusanthula deta, anzathu abizinesi, ndi otsatsa malonda) omwe amaika zomwe zimayendetsedwa pa Tsamba lathu ndi App — ndipo awa amatchedwa “Third Party Tracking Technologies.”


Mitundu yonse iwiri ya matekinoloje awa imatha kusungidwa nthawi yonse yomwe mukuyendera tsambalo kapena nthawi yomwe mumabwerera mobwerezabwereza pa Tsamba lathu kapena pa App.



Mitundu ya njira zamakono zotsatila momwe timagwiritsa ntchito ndi iti? (What types of Tracking Technologies do we use?)


  • Njira Zamakono zotsatila zinthu zofunika Kwambiri (Strictly Necessary Tracking Technologies)
    Ukadaulowu ndi ofunika kwambiri kuti mukhale ndi mwayi wolowa mu akaunti yanu, kuyenda mosavuta pa Tsamba lathu kapena App, komanso kugwiritsa ntchito zinthu zake. Amathandizanso kupereka ntchito zomwe mwapempha, monga kusunga dzina lanu lolowera. Komanso, amagwiritsidwa ntchito pachitetezo ndi kukhulupirika, mwachitsanzo kuzindikira kuphwanya malamulo athu kapena kuthandiza pa chitetezo cha tsambalo.


  • Njira zamakono zotsatila Ntchito (Functionality Tracking Technologies)
    Ukadaulowu umagwiritsidwa ntchito kuzindikira inu mukabwerera ku Tsamba lathu kapena App. Amathandiza kumbukira zomwe mumasankha, monga chilankhulo chomwe mumakonda, ndikupereka zinthu zosinthidwa kuti zigwirizane ndi inu. Amathandizanso pa kulowa (authentication) – mwachitsanzo, kukumbukira kuti mwalowa kale – ndi kuthandiza ntchito zina pa Tsamba lathu ndi App.


  • Njira zamakono zostila za Magwiridwe a ntchito(Performance Tracking Technologies)
    Ukadaulowu umasunga zambiri zokhudza mmene mumagwiritsira ntchito intaneti, monga nthawi yomwe mumakhala pa Tsamba kapena App. Amasonkhanitsa deta ya khalidwe lanu komanso momwe mumachitira ndi zinthu zomwe zili patsamba. Zimenezi zimagwiritsidwa ntchito pa kusanthula (analytics), kafukufuku, komanso kupanga ziwerengero kuti tithe kusintha ntchito zathu.


  • Njira zamakono zosatila za Malonda kapena Kutsatsa (Marketing or Advertising Tracking Technologies)
    Ukadaulowu umagwiritsidwa ntchito kukupatsani zotsatsa ndi zotsogoza zomwe zikugwirizana ndi zomwe mumakonda. Amathandizanso kuchititsa kampeni za kutsatsa kudzera pa imelo, komanso kuchepetsa nthawi yomwe mumawonetsedwa chotsatsa chimodzi. Amathandiza kudziwa momwe kampeni yotsatsa ikuyendera ndipo nthawi zambiri amaikidwa ndi otsatsa athu (monga ma network otsatsa).


  • Njira zamakono zolondoleza za ma tsamba a mchezo (Social Media Tracking Technologies)
    Tsamba lathu ndi App zimakhala ndi zizindikiro za ma social media, monga mabatani a Facebook “Like” kapena “Share.” Zinthu izi zimatha kukhala zoyendetsedwa ndi gulu lachitatu kapena mwachindunji patsamba lathu. Zomwe mumachita ndi zinthu izi zimatsatiridwa malinga ndi ndondomeko yathu ya zachinsinsi (Privacy Policy).


Pansipa pali chiseweredzo cha mitundu yosiyanasiyana ya njira zamakono zolondoleza (tracking technologies). Chimaphatikizapo cholinga chake komanso ngati amasonkhanitsa zambiri zokhudza munthu payekha. Chiseweredzo ichi chimapangidwa kuti chikupatseni kumvetsetsa bwino mmene timagwiritsira ntchito makono olondoleza.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Ma Cookies a Analytics

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Kampani Yokha (First Party Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kuchita bwino (Performance Tracking Technologies)

      Njira zamakonozi zimagwiritsidwa ntchito kusonkhanitsa zambiri zokhudza momwe mumachitira ndi zomwe zili patsamba lathu ndi pa App yathu, monga ma URL omwe mumachokera (referral links) ndi zina zotero. Timagwiritsa ntchito zambiri zimenezi kuti tipange malipoti, tiwerenge ndalama zomwe timayenera kulandira, komanso kuti tikonzere bwino tsamba lathu ndi App ndikupatsani zogulitsa ndi zomwe zili zogwirizana ndi zomwe mumakonda.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Google AdWords

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Kampani Yokha (First Party Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Malonda kapena Kutsatsa (Marketing or Advertising Tracking Technologies)

      Timagwiritsa ntchito Google AdWords, yomwe imagwiritsa ntchito ma cookies kuti itithandize kudziwa chiwerengero cha anthu omwe amadina pa malonda athu a Google ndiyeno kulumikizana nafe kudzera pa tsamba lathu. Cookie iyi imayikidwa pa browser yanu kokha mukadina pa chotsatsa cha Google, ndipo imatithandiza kuwonjezera momwe tsamba lathu limagwirira ntchito bwino kwa alendo athu. http://www.google.co.uk/intl/en/analytics/privacyoverview.html


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Google Tag Manager

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu (Third Party Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe (Performance Tracking Technologies)

      Cookie iyi imakhudzana ndi Google Tag Manager, yomwe timagwiritsa ntchito kutsitsa (download) kapena kuyika ma script pa masamba a tsamba lathu kuti zithandize kugwira ntchito bwino ndi moyenera. http://www.google.co.uk/intl/en/analytics/privacyoverview.html


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Google Analytics

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu (Third Party Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe (Performance Tracking Technologies)

      Cookie iyi imagwiritsidwa ntchito kusonkhanitsa zambiri zokhudza momwe alendo amagwiritsira ntchito Tsamba lathu ndi App yathu. Timagwiritsa ntchito zambiri zimenezi kuti tipange malipoti komanso tikonzere bwino Tsamba ndi App. Ma cookie awa amasonkhanitsa zambiri monga chiwerengero cha alendo, kumene alendo abwera kuchokera, masamba omwe awawona, ndi zina zofunika zokhudza kugwiritsa ntchito kwao tsambalo. http://www.google.co.uk/intl/en/analytics/privacyoverview.html


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Hotjar

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe

      Hotjar ndi chida chomwe chimasonkhanitsa zambiri zokhudza momwe alendo amagwiritsira ntchito Tsamba lathu ndi App. Hotjar imagwiritsa ntchito ma cookie kusonkhanitsa zambiri zosakhudza umwini wa munthu. Zitsanzo za zomwe zimasonkhanitsidwa zikuphatikizapo masamba omwe awonedwa, momwe masamba amagwiritsidwira ntchito, mtundu wa chipangizo ndi msakatuli womwe wagwiritsidwa ntchito, komanso dziko limene muli. https://www.hotjar.com/privacy


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Xtremepush

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe, Kutsatsa kapena Zamalonda

      Xtremepush ndi nsanja ya kutsatsa ndi kusanthula yomwe timagwiritsa ntchito pa kusanthula kwa deta, kukwaniritsa mafomu a pa intaneti, kutumiza ma push notifications, komanso pazifukwa zokhudzana ndi kutsatsa. Xtremepush Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Iovation

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira Wofunika Kwambiri

      Iovation imagwiritsidwa ntchito poletsa ndi kuzindikira zipangizo zokhudzana ndi chinyengo kapena ntchito zoipa, ndipo imapereka ntchito zodziwitsa zipangizo komanso zodzitetezera ku zachinyengo. Iovation Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): TrustPilot

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe

      Ma cookie awa amagwiritsidwa ntchito kuwonetsa ndemanga kuchokera ku TrustPilot ndikukupatsani mwayi woti mutipatse ndemanga, komanso pazifukwa zosanthula. Trustpilot's Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Pingdom

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kachitidwe

      Ma Tracking Technologies awa amagwiritsidwa ntchito kuyang’anira nthawi yomwe tsamba limatseguka, momwe ntchito zikuyendera, komanso kulemba zambiri zokhudza momwe tsamba ndi App zikuyendera. Timagwiritsa ntchito Pingdom kuti tiwonetsetse kuti ogwiritsa ntchito akusangalala komanso ntchito zikuyenda bwino. Pingdom Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Bing

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kutsatsa kapena Zamalonda

      Timagwiritsa ntchito Bing Ads kuti tikuwonetseni malonda apadera okhudzana ndi zomwe mumakonda. Ma cookie awa amayendera momwe mumafufuzira komanso momwe mumagwiritsa ntchito tsamba, ndipo amathandiza kumvetsetsa momwe makampeni athu a Bing akuyendera. Microsoft Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Income Access

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira wa Kutsatsa kapena Zamalonda

      Timagwiritsa ntchito Income Access, ntchito ya affiliate marketing, kuti titsatire momwe ntchito za ogwirizana zikuyendera. Income Access imatha kulemba zizindikiro zapadera za chipangizo chanu kuti itsatire zomwe mumachita pa Tsamba lathu kapena App. Zambiri zimenezi zimagwiritsidwa ntchito kusanthula, kukonza tsamba, komanso kuyeza momwe makampeni a kutsatsa akuyendera. Income Access Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Incapsula

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira Wofunika Kwambiri

      Cookie iyi imagwiritsidwa ntchito kulimbikitsa chitetezo cha Tsamba ndi App, monga kuteteza ku ma Denial of Service (DDoS) attacks. Incapsula Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Sentry

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu (Error Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira Wofunika Kwambiri

      Cookie iyi imagwiritsidwa ntchito kuyang’anira ndi kulemba zolakwika zomwe zimachitika pamene wogwiritsa ntchito ali patsamba. Imathandiza kuzindikira ndi kukonza mavuto aukadaulo, motero kukonza bata ndi magwiridwe a tsamba. Sentry Privacy Policy.


  • Zamakono zotsatira (tracking technology): Cloudflare

    • Mtundu: Ukadaulo Wotsatira wa Gulu Lachitatu (Performance Tracking Technology)

    • Cholinga: Ukadaulo Wotsatira Wofunika Kwambiri

      Cookie iyi imagwiritsidwa ntchito kuzindikira magalimoto odalirika pa intaneti, kulimbikitsa chitetezo cha tsamba, komanso kukonza magwiridwe ake, monga kulimbitsa load balancing ndi kuteteza ku ntchito zoipa. Cloudflare Privacy Policy.


Chonde dziwani kuti sitimazindikira kapena kuyankha zizindikiro zokha za msakatuli zokhudza Ukadaulo Wotsatira, kuphatikizapo zofuna za 'Do Not Track. Komabe, pali njira zosiyanasiyana zomwe mungagwiritse ntchito poyang'anira ndi kusamalira makonda a ma cookie anu. Chonde kumbukirani kuti pochotsa kapena kutseka ma cookie, zina mwa ntchito za Tsamba la pa Intaneti ndi Pulogalamu zingalephereke kugwira ntchito bwino kapena kugwira mogwira mtima.


  • Kutseka ma cookie kudzera mu msakatuli wanu wa pa intaneti
    Masakatuli ambiri a pa intaneti amapereka zambiri zoyambirira zokhudza ma cookie, ndikukulolani kuona ma cookie omwe asungidwa pa chipangizo chanu, kuchotsa onse kapena chimodzichimodzi, komanso kutseka kapena kulola ma cookie pa masamba onse kapena pa masamba omwe mwasankha. Mukhozanso kuzimitsa ma cookie a anthu ena padera. Chonde dziwani kuti zokonda zoperekedwa ndi msakatuli kapena chipangizo nthawi zambiri zimangogwira ntchito pa msakatuli kapena chipangizocho.




  • Kumene maulalo amaperekedwa pa Webusaiti ndi App ku mawebusaiti a anthu ena ndikofunika kukumbukira kuti mawebusaitiwa adzakhala ndi ma cookie awo ndi ndondomeko zachinsinsi zomwe zidzayang'anire chidziwitso chilichonse chomwe mungatumize. Ngati mwaganiza zogwiritsa ntchito masamba aliwonse olumikizidwa ndi anthu ena chonde werengani ma cookie awo ndi mfundo zachinsinsi musanatero


Kusintha pa ndondomeko yama cookies

Tili ndi ufulu wosintha Ndondomeko ya Ma Cookies nthawi iliyonse, chonde mudzipita patsamba lino pafupipafupi. Tidzapereka chidziwitso cha kusintha kwa Ndondomeko ya Ma Cookies iyi potumiza mawu osinthidwa pa Webusaiti yathu ndi App. Popitiriza kugwiritsa ntchito Webusaiti yathu ndi App, tidzalingalira kuti mukuvomereza zosinthazi.


Back to top
Not logged in-Join NoworLogin