Uthengawu ulinso mu Chingerezi


betPawa Malawi – Mfundo Zokhudza Chinsinsi (Privacy Policy)


Pano ku Kuwina Limited, omwe ali ndi chilolezo cha dzina la betPawa ku Malawi ("Kampani" "ife", "ifeso", "yathu") timasamala za chinsinsi chanu kwambiri kamba koti ndizofunikira kwa ife. Ndiye tikamagwiritsa ntchito zambiri zanu, timasatila malamulo omwe anaikidwa osamalira ndikuyendesa zinsinsi zanu.(Data Protection Laws).


Mogwirizana ndi mgwirizano wa layisensi ya betPawa, kampani ya SoftPawa Limited (“SoftPawa”), yomwe ili ku C/O Freeths LLP, Routeco Office Park Davy Avenue, Knowlhill, Milton Keynes, England, MK5 8HJ, ndiye Woyang’anira Zambiri (Data Controller), ndipo ndondomeko iyi ikusonyeza mmene timagwiritsira ntchito ndi kukonza zambiri zanu mukamagwiritsa ntchito tsamba la betPawa (monga tafotokozera pansipa).


Bungwe loyenerera loyang’anira zachinsinsi ndi Malawi Data Protection Authority (“Bungwe la Chitetezo cha Zambiri”).


Ndondomeko iyi ya Zachinsinsi ndi gawo la Malamulo ndi Zikhalidwe (“Terms”) zomwe zilipo patsamba lawebusayiti yathuyi.


Chiyambi

Ife ndiwozipeleka kwamphumphu posamala ndi kuteteza zinsinsi za inu makasitomala (client) athu, monga inu ogwiritsa ntchito tsamba lathu.


Choncho tapanga ndondomeko zotetezela zinsinsi zanu(Privacy Policy), zomwe zimathandiza chitetezo cha zambiri zanu, kuphatikizapo mmene timasonkhanitsira, kugwiritsa ntchito, kufalitsa, ndi kuteteza zambiri zanu, komanso ufulu umene muli nawo okhudza zambiri ndi zinsinsi zanu.


Pogwiritsa ntchito zambiri zanu, cholinga chathu ndi kukonza momwe mumakumana ndiku gwiritsa ntchito tsamba lathu, mapulogalamu athu, ndi ntchito zathu. Kuteteza zambiri zanu ndi chinthu chofunika kwambiri kwa ife; ndiye tinaika njira ndi ndondomeko zotetezela zinsinsi ndi zambiri zanu. Cholinga chathu ndi kusabisa mmene timasonkhanitsira ndi kugwiritsa ntchito zambiri zanu. Timavomerezanso ndikulemekeza zisankho ndi ufulu wanu wokhudza zambiri zanu.


Ndondomeko iyi iyenera kuwerengedwa ndi kugwiritsidwa ntchito limodzi ndi Ndondomeko ya Ma Cookies komanso Malamulo ndi Zikhalidwe (Terms) zomwe zikupezeka patsamba lathuli. Tili ndi ufulu wosintha Ndondomeko iyi nthawi ndi nthawi, ndipo tidzakudziwitsani zosinthazo mwa kuyika mtundu watsopano patsamba lathu kapena kudzera munjira zina zoyenera. Tikukulimbikitsani kuti muzitsatira pafupipafupi kuti muwone ngati pali zosintha.


Timapereka masewera a mwayi (games of chance), kuphatikizapo ndi magemu apa intaneti (Casiono games), osangokhala kubetcha pa masewera (sports betting) monga momwe zafotokozedwera mu “Ntchito (Services)” m’Malamulo.


Timapereka Ntchito zathu kudzera m’njira zosiyanasiyana (zotchedwa “Website” mu Malamulo athu (terms)), monga:

  • Tsamba ili la intaneti, kuphatikizapo ma tsamba ena osaima paokha (subdomain) ndi matsamba ena ogwirizana (affiliated websites);

  • Ma pologaramu athu (Applications), omwe amatheka kutsitsidwa (downloadable) ndikugawana kuzela pama phone anu ammanja komaso ma Computer. Mutha kutsitsa (download) kuzela pa tsamba la Apple store, ngati mukugwiritsa ntchito foni yantundu wa iphone komaso kuzela patsamba lathu lomweri ngati mukugwiritsa ntchito Foni ya Android.

  • Mapulogalamu apaintaneti osatsitsidwa (Non-downloadable online applications) monga flash apps, HTML5 apps, ndi ena.


Ndondomeko (Policy) iyi imagwira ntchito kwa makasitomala (clients) athu onse, kuphatikizapo osewera, alendo a tsamba lathu, ndi anthu amene amagwirizana ndi masewera athu kapena ntchito zokhudzana ndizobeta.


Tikukulimbikitsani kuti muwerenge mosamala Ndondomeko ya Zachinsinsi (privacy policy) musanayambe kugwiritsa ntchito kapena kubeta pa tsamba lathuli, kuti muzitha kusankha mwanzeru.


Poyendera komaso kugwiritsa ntchito tsamba lathu, kapena mukasegula akaunti kudzera pa tsamba lathu, mukutsimikizira kuti mwawerenga ndi kumvetsa Ndondomeko iyi ya Zachinsinsi(privacy policy).


Mfundo Zokhudza Chinsinsi

Kampani yathu imatsatira malamulo a Chitetezo cha Zambiri (Data Protection Laws). Izi zikutanthauza kuti nthawi zonse tikamagwiritsa ntchito zambiri zanu, timatsatira mfundo zomwe zimachokera mu Malamulo a Chitetezo cha Zambiri (Data Protection Laws):


1. Kutsatira malamulo, chilungamo, ndi kuwonekera (Lawfulness, fairness and transparency):

Zambiri zonse zimachitidwa motsatira malamulo, molungama, komanso momveka bwino.


2. Kugwiritsa ntchito molingana ndi cholinga chake (Purpose limitation):

Zambiri zonse zimasonkhanitsidwa chifukwa cha zolinga zomwe zanenedwa bwino, zomveka, komanso zovomerezeka, ndipo sizigwiritsidwa ntchito pa zinthu zina zosagwirizana ndi zolinga zake.


3. Kuchepetsa kuchuluka kwa zambiri zomwe zikusonkhanitsidwa (Data minimisation):

Zambiri zomwe timasonkhanitsa zimakhala zokwanira, zofunika, komanso zochepa malinga ndi zomwe zikufunika kuti zitheke kugwiritsidwa ntchito pa cholinga chomwe chinakonzedwa.


4. Kulondola kwa zambiri (Accuracy):

Timatsimikizira kuti zambiri zomwe tili nazo ndi zolondola komanso zimasinthidwa nthawi zonse, ndipo tikapeza zolakwika timazikonza mwachangu.


5. Nthawi yosungira zambiri (Storage limitation):

Timatsimikizira kuti zambiri sizimasungidwa kwa nthawi yaitali kuposa momwe zikufunika, ndipo zimangokhalira kusungidwa nthawi yomwe ili yoyenera malinga ndi cholinga chomwe zidasonkhanitsidwa.


6. Chitetezo ndi chinsinsi (Integrity and confidentiality):

Timatsimikizira kuti zambiri zanu zikuchitidwa m’njira yotetezeka, pogwiritsa ntchito njira zaukadaulo ndi za bungwe zoteteza kuti zisagwiritsidwe ntchito mopanda chilolezo, kapena kuti zisatayike, kuwonongeka, kapena kuchotsedwa mwangozi.


7. Udindo ndi kutsatira malamulo (Accountability):

Timatsatira malamulo onse okhudzana ndi chitetezo cha zambiri mwa kukhazikitsa njira zoyenera zaukadaulo ndi za bungwe loteteza zambiri zanu, kusunga mbiri ya momwe zimagwiritsidwira ntchito, komanso kugwirizana ndi mabungwe oyang’anira kuti tiwonetse kutsatira mfundo za chitetezo cha zambiri.


Chifukwa Chomwe Timasonkhanitsira Zambiri Zaumwini

Timagwirtitsa ntchito zambiri zanu (personal data), ndicholinga choti tikupaseni ntchito zathu (our services). Potsatira mfundo ya kuchepetsa kuchuluka kwa zambiri (data minimization), timasonkhanitsa zambiri zofunika zokha, ndipo timazigwiritsa ntchito pokhapokha pa zolinga zovomerezeka ndi zomwe zanenedwa bwino. Sitimagulitsa zambiri zanu kwa munthu kapena kampani ina iliyonse.


Timafunikira zambiri zanu kuti:

  • Tikupatseni Ntchito zathu(our services);

  • Titsatire zofunikira za malamulo kapena malamulo oyendetsera ntchito;

  • Titeteze zofuna zanu, zathu, za anthu onse kapena za anthu ena okhudzidwa;

  • Nthawi zina, kugwiritsa ntchito zambiri zanu pazifukwa zina zomwe mwavomereza momveka bwino.

Timagwiritsa ntchito zambiri zanu pa ntchito monga:

  • Kuyeza momwe tsamba lathu likugwiritsidwira ntchito;

  • Kulembetsa ndi kutsimikizira akaunti yanu;

  • Kusamalira malipiro ndi kupereka ntchito;

  • Kuchita ntchito zokhudzana ndi kasitomala (customer support);

  • Kutsatsa ndi kulimbikitsa ntchito (marketing initiatives);

  • Kupewa chinyengo (fraud prevention);

  • Kulimbikitsa kubetcha kotetezeka (safe gambling practices);

  • Kasamalidwe ka chiwopsezo (risk management);

  • Kuzindikira ndi kupewa ndalama zonyamulidwa mwachinyengo kapena zopangidwa ndi zigawenga (anti-money laundering and counter-trafficking financing);

  • Ndiponso kusintha momwe mumakumana ndi tsamba lathu kapena pulogalamu yathu kuti ikhale yogwirizana ndi inu (personalised experience).


Ndizambiri zake ziti zomwe timafuna?

4.1 Zambiri Zokhudza Munthu (Personal Information)


Mtundu woyamba wa zambiri ndi zomwe zingadziwitse kapena zingathe kuzindikira munthu payekha (“Zambiri Zokhudza Munthu”). Zambiri izi zitha kusonkhanitsidwa ndipo zingaphatikize zinthu izi:

  • Zambiri za Kulembetsa (Registration details): Mukamapanga akaunti ndi kulembetsa kuti mugwiritse ntchito Tsamba ndi Ntchito zathu, mungapemphedwe kuti mupereke zambiri zokhudza inu monga: dzina loyamba ndi labambo, zambiri yakomwe mmakhala(address), Kusiyanitsa pakati pa maina kuti ndinu aamuna kapena aakazi (Gender), tsiku lobadwa, nambala ya chiphatso chanu (ID number), nambala ya foni, ntchito yomwe mumagwira, ndi zina zotero.
    Kuphatikizapo, titha kusonkhanitsa zambiri ndi zikalata monga momwe zimafunikira ndi malamulo a Kudziwitsa Kasitomala (KYC) ndi Kuletsa Kuchita Zolakwa pa Ndalama (AML), monga gwero la ndalama zanu ndi njira zomwe mumapezera chuma.

    Mwantchito zina zomwe timatengera zambiri zanu, zimatithandizira ife kuti titsatire malamulo ndi zofunikira zomwe tili nazo monga kampani yazobeta (gambling company), kuphatikizapo zofunikira za chilorezo, chamalamulo azobeta moyenera, ndi malamulo a AML.


  • ID yochokera ku boma (Government-issued ID): Mogwirizana ndi zofunikira za KYC(Know your Customer) ndi AML (anti Money Laundering), mungapemphedwe kuti mupereke fanizo la ID yanu, monga Chiphaso chanu chaunzika, kapena china chilichonse chovomerezeka ndi boma kuti titsimikizire kuti ndinu amene mukugwiritsa ntchito akaunti yanu, potengela chilorezo cha mmene mungagwiritsile ntchito pa tsamba lathu.


  • Zambiri zokhudza kubeta (Gaming information): Kuti ifeyo tibwerese zochita(services) pa tsamba lathu, timasunga zambiri zokhuza account yanu pogwiritsa ntchto zintchito zathu (services) , monga ndondomeko za ndalama (transactions), ndalama zomwe mumayika (deposits), mabeti anu, kuchotsa ndalama (withdraws), ma bonasi ndi zopambana, komanso kutenga nawo mbali pa mpikisano.


  • Zambiri za Malipiro (Payment information): Kuti mupitilize kusangalala ndi zintchito(services) zathu, (monga kubeta, kapena kugula), timasonkhanitsa zambiri zokhudza malipiro anu, monga ndalama zomwe mumagwiritsa ntchito kapena zambiri zokhudza Payment Service Provider (PSP) wanu.


  • Zambiri zomwe mumapereka mwaufulu (Voluntary information): Timasonkhanitsanso zambiri zanu zomwe mumasankha kutipatsa. Chitsanzo, Izi zitha kukhala mukamayankha mauthenga athu, kutitumizira imelo (email), kapena kugawana zambiri za inu kudzera mu Ntchito monga pa chat kapena pamasewera(games).

    Izi zimaphatikizapo zambiri zomwe mukufuna kugawana nafe kuti tithe kukonza ubale wathu ndi inu komanso kuonetsetsa kuti mukusangalala ndi Ntchito zathu.


  • Zambiri za Chipangizo (Device information): Timasonkhanitsa zambiri zokhudza chipangizo chimene mumagwiritsa ntchito monga Foni, pulogalamu, kapena zida zomwe zingakuzindikireni, monga UDID, IMEI, MAC address, IP address, ndi geo-location data ngati zikugwirizana.


  • Mafoni (Telephone calls): Titha kulemba kapena kuyang’anira zomwe tayankhulana pafoni pazifukwa izi:

    • Kuthetsa mikangano kapena kutsimikizira maumboni azamalamulo;

    • Zantchito zothandiza makasitomala athu (monga kuwunika khalidwe la ntchito, kuonetsetsa kuti kasamalidwe kakuyenda bwino, komanso kukhutitsidwa kwa makasitomala);

    • Kuonetsetsa kuti tikutsatira malamulo;

    • Maphunziro a ogwira ntchito;

    • Kuzindikira ndi kupewa chinyengo kapena ntchito zolakwika.

      Pa nthawi iliyonse, mudzadziwitsidwa kumayambiriro kwa foni kuti kuyankhulana kukujambulidwa.


  • Zochitika (Events): Pa nthawi ya zochitika zathu, timatha kuchita zinthu monga kuyankhula ndi alendo, olankhula, othandizira, kapena owonetsera, komanso kutenga zithunzi kapena makanema.

    Tidzapempha chilolezo chanu musanatengedwe chithunzi kapena kanema komwe muli, komanso musanagwiritse ntchito zithunzizo pa kutsatsa.

    Mudzapemphedwanso chilolezo musanayambe kugwiritsa ntchito zomwe mwalankhula pa kutsatsa.

    Mukamagwiritsa ntchito Ntchito zathu, mutha kuitana bwenzi kuchokera pa netiweki yanu kuti lijoyine Ntchito. Akavomera, titha kusonkhanitsa zambiri zawo monga dzina, imelo, nambala ya foni, ndi tsiku lobadwa, ndipo izi zidzagwiritsidwira ntchito molingana ndi Ndondomeko iyi ya Zachinsinsi.

    Kuti pakhale chilungamo, mawu ofotokoza mu zotsatsa za zochitika azikhudza momwe zithunzi kapena makanema angagwiritsidwire ntchito.



  • Zambiri zomwe timapeza kuchokera kwa anthu ena (Information from third parties): Timapezanso zambiri kuchokera kwa omwe timagwirizana nawo (third party) monga opereka ntchito za netiweki yanu, Airtel ndi TNM, komaso mabungwe ena azachuma (Banks), komanso kuchokera kuzinthu zomwe zingathandize kutsimikizira kuti ndinu amene mukuti muli kapena kupewa ntchito zachinyengo.


  • Zambiri zaukadaulo ndi zolumikizana (Technical, device and connection information): Mukatsitsa (download) tsamba lathu pa chipangizo chanu, titha kutolera zambiri kuchokera pa chipangizo chomwe mukugwiritsa ntchito, pofuna kupeleka chitetezo ndi kupewa chinyengo komanso kupewa zina zambiri. Mwachitsanzo, titha kusonkhanitsa zambiri zokhudzana ndi mapulogalamu ena omwe akugwira ntchito nthawi imodzi ndi Webusayiti kuti azindikire ngati mukugwiritsa ntchito mapulogalamu omwe amagwirizana ndi tsamba lathuli mwachinyengo (mwachitsanzo maloboti, pulogalamu yaumbanda, ndi zina zotero) kapena kuyang'ana ngati kulumikizana komwe mukugwiritsa ntchito kuli kodzera pa VPN kapena proxy.

    Kuti tikweze ntchito za Tsamba lathu ndi kukonza momwe zimagwirira ntchito, timasonkhanitsa zambiri zaukadaulo zomwe zimatumizidwa ndi chipangizo chanu, monga mtundu wa msakatuli (browser), dongosolo la kompyuta (operating system), chilankhulo chomwe chipangizo chimagwiritsa ntchito, nthawi yolowera, ndi tsamba limene mudachokera.


  • ZaZambiri za kusanthula (Analytics information): Timasonkhanitsa zambiri zokhudza momwe mumagwiritsa ntchito Ntchito zathu, monga kugwiritsa ntchito mapulogalamu, ndondomeko yomwe mwapandila log(log files), zochita za ogwiritsa ntchito (monga masamba omwe mumaonera, nthawi yomwe mumakhala patsamba, zomwe mumadina, ndi zina), nthawi yolowera, ndi ma alarm. Zambiri izi zimagwiritsidwa ntchito kuti tikonze zolakwa, kufufuza zolakwika, komanso kusanthula momwe Ntchito zikugwiritsidwira ntchito.

  • Zambiri zosazindikirika (Anonymous information): Titha kuchotsa zizindikiro pa zambiri zomwe tasonkhanitsa kuti zisazindikire munthu aliyense payekha.

    Zambiri zotere sizimayendetsedwa ndi malamulo a Ndondomeko iyi, ndipo titha kugawana nazo ena pa zolinga zilizonse monga kutsatsa kapena kafukufuku.



4.2 Zambiri Zosazindikirika (Non-Personal Information):


Mtundu wachiwiri wa zambiri ndi zomwe sizingazindikiridwe kapena sizikudziwika za munthu payekha (“Non-Personal Information”).


Zambiri izi zimaphatikiza zambiri zaukadaulo komanso momwe ogwiritsa ntchito amagwiritsira ntchito Ntchito, monga:

  • Dongosolo lomwe kasitomala amagwiritsa ntchito,

  • Mtundu wa msakatuli(browser),

  • Kusamutsidwa kwa chophimba (screen resolution),

  • Chilankhulo cha msakatuli ndi kiyibodi,

  • Zochita za kasitomala pa Tsamba (monga zomwe amadina),

  • Nthawi yomwe adakhala akugwiritsa ntchito Ntchito, ndi zina zotero.


Ngati nthawi iliyonse zambiri zosazindikirika zimalumikizidwa ndi Zambiri Zokhudza Munthu, ndiye kuti zimakhala ngati Zambiri Zokhudza Munthu mpaka kulumikizanako kutha.


Ndondomeko Ya kagwilitsidwe ka ntchito ka Uthenga wa Chidziwitso

Titha kugwiltsa ntchito chidziwitso chanu pamene pali chimodzi mwa zokhuza za malamulo ndi ku phatikizaponso izi:


  • Kukwaniritsa kwa mgwirizano, motsatira malamulo: (Fulfilment of a contract, compliance with a legal obligation): Ndikofunikira kuti tikonze zidziwitso zanu zomwe zili zofunika kuti mgwirizano ugwire ntchito kapena kuti titsatire maudindo athu osiyanasiyana azamalamulo, kapena owongolera, komanso osangotsatira zomwe zili ndi ziphaso zathu zotchova njuga ndiponso kutsatira malamulo aliwonse okhudza kupewa kuba ndalama (AML) komanso odziwa katsitomala (KYC).


  • Zokonda zovomerezeka(Legitimate interests):Timakonzanso zambiri za zidziwitso zanu pomwe tikuona kuti kukonza koteroko kuli m'zokonda zathu zovomerezeka (kapena zokonda zovomerezeka za ma bungwe ena omwe datayi imepelekedwa kwaiwo) malinga ngati kukonza koteroko sikungasokoneze ufulu wa zokonda zanu. Chitsanzo cha momwe timakonzera chidziwitso mogwilizana ndi zokonda zovomerezeka ndi izi:

    • Pamene tipereka chidziwitso chaumwini kwa makampani athu angapo wogwira nawo ntchito kapena ang'onoang'ono kutsatira kusintha kwa kampani kapena pa zifukwa zoyang'anira ntchito za mkati, ndipo anthu oterewa adzakhalanso okamizidwa ndi zofunikira za chinsinsi zomwe zimatsatidwa ndi Malamulo Oteteza Chidziwitso;

    • kuzindikira ndi kusunga chidziwitso chokhudza anthu amene ali ndi mavuto osewela njuga mosamala;

    • kukonza chidziwitso ndi cholinga chotsimikizira chitetezo cha intaneti ndi chidziwitso, kuphatikizapo kuletsa anthu osaloledwa kulowa mu njira zathu zolumikizirana za netiwoki;

    • kuteteza kukhulupirika kwa ntchito zathu polimbana, kupereka malipoti, ndi kugawana chidziwitso chokhudza njira zoyikira ndalama zokayikitsa kapena zachinyengo;

    • kutsatira malamulo ndi zofunikira za boma;

    • kupanga ndondomeko ya mphoto yapadera kwa osewera ndi kugawana chidziwitso chaumwini ndi alangizi athu komanso opereka chithandizo cha ukadaulo (monga owerengera ndalama) kuti tiwonetsetse kuti tikutsatira malamulo oyenera woyendetsera ntchito komanso njira zabwino za makampani.

  • Chilolezo(Consent): Makonzedwe athu a Chidziwitso chanu chaumwini adzakhala ofunikira kwambiri kuti tikupatseni ntchito zathu. Nthawi zina, tikhoza kupempha chilolezo chanu kuti tikonze Chidziwitso chaumwini. Zikatero, Chidziwitso chanu chaumwini chidzakonzedwa motsatira chilolezocho ndipo mudzatha kuchotsa chilolezochi polemba kalata nthawi iliyonse.


  • Zofunidwa ndi a zamalamuro (Requirement by law): Titha kukonza Chidziwitso chanu chaumwini popanda chilolezo chanu chodziwikiratu pamene talamulidwa kutero ndi lamulo. Izi zikuphatikizapo nthawi pamene malamulo ofunikira amatikakamiza kusonkhanitsa ndi kukonza chidziwitso chaumwini kuti tikwaniritse zofunikira zathu zamalamulo kapena kutsatira malangizo a boma. Zoterezi zitha kuchitika, mwachitsanzo, popereka malipoti a msonkho, pofufuza milandu, m'milandu ya m'khoti, komanso pa nkhani za chitetezo cha dziko. Komabe, tadzipereka kuonetsetsa kuti kukonza kulikonse komwe kukuchitika pansi pa zoterezi kukuchitidwa motsatira malamulo oyenerera, ndikuganiziranso za kuteteza zinsinsi ndi ufulu wanu.


  • Zofunikala pa Umoyo: Titha kukonza Chidziwitso chanu chaumwini ngati kuli kofunikira kuteteza zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu kapena moyo wa munthu wina, monga kupewa kuvulazidwa kapena ziwopsezo zomwe zingaike chiopsyezo moyo wa munthu.


  • Udindo wa Anthu: Nthawi zina, titha kukonza kapena kuwulula Chidziwitso chanu chaumwini ngati kuli kofunikira kuti tigwire ntchito yofunika kwa anthu onse kapena pogwiritsa ntchito mphamvu za boma; mwa chitsanzo, ngati tapemphedwa ndi wogwira ntchito m'boma woyenerera kufufuza za umbanda kuti tithandizire pa kafukufuku yemwe akuchitika, kapena pamene tiganiza zopereka chidziwitso ku gulu lachitatu lomwe lili ndi ulamuliro wotero (monga apolisi).

Pa zochitika zina zonse, Chidziwitso chanu chaumwini chidzakonzedwa ndi chilolezo chanu ndipo mudzatha kuchotsa chilolezochi polemba kalata nthawi iliyonse.


Anthu a Chichepere:

Timagwila ntchito zathu ndi anthu okhawo amene ali ndi zaka 18 kapena kupyolera apo. Ngati simunakwanitse zaka zimenezi, simuli ovomelezedwa kugwilitsa ntchitozi kapena kutipatsa chidziwitso chanu chaumwini.


Tili ndi ufulu wopeza ndi kutsimikizira chidziwitso chanu chaumwina chili chonse chomwe tasonkhanitsa kuchokera kwa inu. Zikapezeka kuti tadziwa kuti Kasitomala yemwe ndi wachichepele wagawana nafe chidziwitso, titha kuimitsa akaunti kuti isathe kugwilitsidwa ntchito. Ngati muli ndi umboni kuti mwana wachichepere wagawana nafe chidziwitso chilichonse, chonde tilankhuleni pa[data.protection@betpawa.com].


Kodi Timagwiritsa Ntchito Bwanji Chidziwitso Chanu?

Timagwiritsa ntchito chidziwitso chanu cha umwini pa zifukwa zomwe zatchulidwa pansipa:

  • kukhazikitsa, kuyang'anira ndi kusintha akaunti yanu;

  • kupereka ndi kuyendetsa ntchito (monga kubeta, masewera a pa intaneti ndi kukonza zolipira);

  • kulankhulana nanu ndikukudziwitsani zakusintha kwathu kwaposachedwa pa Ntchito zathu ndi zotsatsa zapadera;

  • kutsatsa Ntchito zathu (onani zambiri pansipa pansi pa "Kutsatsa"), komanso kukupatsani zotsatsa, zinthu zopangidwira inu panokha kuphatikizapo zotsatsa zozikidwa pa khalidwe lanu;

  • kuchita kafukufuku wozama, wa ziwerengero ndi wofufuza, pofuna kukonza ndi kusintha Ntchito zathu kuti zigwirizane ndi zosowa ndi zokonda zanu (monga popanga malipoti ophatikizana okhudza kagwiritsidwe ntchito ka mbali zina za Ntchito zathu).

  • Pa zifukwa zoyendetsera ubale ndi makasitomala, komanso kuthandiza ndi kukonza mavuto a Ntchitozi ndi kuyankha mafunso anu, kuphatikizapo zopempha zanu zoti mugwiritse ntchito ufulu wanu;

  • kutithandiza kupititsa patsogolo, kusintha ndi kukonza Ntchito zathu mogwirizana ndi zomwe ogwiritsa ntchito amakonda komanso momwe amagwiritsira ntchito;

  • kuzindikira ndi kupewa zinthu zachinyengo ndi zosaloledwa kapena mtundu wina uliwonse wa zochitika zomwe zingaike pachiswe kapena kukhudza moyipa kukhulupirika kwa Ntchito zathu, kuphatikizapo pozindikira zoopsa zogwirizana ndi zomwe mukuchita pa Ntchito yathu;

  • kutithandiza kukwaniritsa zofunikira za malamulo otilamulira kapena monga momwe lamulo likufunira (monga malamulo a njuga, zofunikira za malamulo a KYC ndi AML);

  • kutsatira malamulo ndi udindo wathu wovomerezeka

  • pa zifukwa za bizinesi yathu yamkati.

  • kukhazikitsanso mawu anu achinsinsi kudzera munjira zotumizirana mauthenga: Popempha kukhazikitsanso mawu achinsinsi, mukuvomereza kulandira Mawu Achinsinsi Ogwiritsidwa Ntchito Kamodzi (OTPs) kudzera munjira yolankhulirana yomwe mwasankha, yomwe ingaphatikizepo kuyimbiridwa foni, WhatsApp, kapena Telegram, malinga ndi momwe zingakhalire.

  • Thandizo la Macheza A Pompopompo (Live Chat): Zidziwitso zanu zausiku, chidziwitso chilichonse, kapena zinthu zilizonse zomwe mwagawana pamacheza apompopompo zidzasonkhanitsidwa ndi kukonzedwa mogwirizana ndi Ndondomeko Yachinsinsiyi. Pogwiritsa ntchito macheza apompopompo, mukumvetsetsa kuti kusonkhanitsa ndi kukonza zidziwitso zanu mogwirizana ndi zomwe zafotokozedwa mu Ndondomeko Yachinsinsiyi komanso zidziwitso zomwe mwagawana pamachezawa zidzagwiritsidwa ntchito pofuna kukupatsani chithandizo, kuthetsa mavuto, kapena kuyankha mafunso ngati pakufunika.

  • pa zifukwa zina monga momwe zafotokozedwera mu Ndondomeko Yachinsinsiyi.


Pakutsatsa malonda:

Kampani ikhoza kugwiritsa ntchito uthenga wanu. Mutapereka chilolezo chanu, monga dzina lanu, adilesi yakunyumba, imelo, nambala yafoni, ndi zina zotero. Titha kuchita izi tokha kapena pogwiritsa ntchito makampani ena amene amatithandiza, ndi cholinga chokupatsirani zinthu zotsatsa zokhudzana ndi ntchito zathu, komanso zinthu zina, ntchito zina, mawebusayiti ndi mapulogalamu amene ali a mabwenzi athu abizinesi ndi oyanjana nawo (onse pamodzi: “Oyanjana Nawo pa Zotsatsa”), zimene timakhulupirira kuti zingakusangalatseni.


Titha kugawana ndi kuulula Zambiri Zanu Panokha ndi Oyanjana Nawo pa Zotsatsa ndi cholinga chokupatsirani zotsatsa zosiyanasiyana, zimene ife, kapena Oyanjana Nawo pa Zotsatsa, timakhulupirira kuti n'zofunika kwa inu. Oyanjana Nawo pa Zotsatsa athu angagwiritse ntchito Zambiri Zanu Panokhazi m'njira zosiyanasiyana zotsatsira, monga kutumiza imelo mwachindunji, makalata, mauthenga a pa foni (SMS) ndi kukuyimbirani foni.


Tidzagwiritsa ntchito Zambiri Zanu Panokha ndi cholinga chokupatsirani zinthu zotsatsa pokhapokha ngati tili ndi chifukwa chomveka chovomerezeka chochitira zimenezo, kapena pamene tapeza chilolezo chanu kuti tichite zimenezo.


Muli ndi ufulu wopempha Woyang'anira Zambiri (Data Controller) kuti asiye kugwiritsa ntchito zambiri zanu panokha ngati zikugwiritsidwa ntchito potsatsa mwachindunji, kuphatikizapo kusanthula zambiri zanu zokhudzana ndi kutsatsako. Mutha kukana nthawi iliyonse kulandiranso zotsatsa zina kuchokera kwa ife kapena kwa Oyanjana Nawo pa Zotsatsa potilankhula pa imelo yomwe yaperekedwa kapena podzichotsa pamndandanda wolandira zotsatsa potsatira malangizo omwe ali pa mauthenga otsatsa (monga kukanikiza batani la “Dzichotseni” kapena “Unsubscribe”).


Chonde dziwani kuti kudzichotsa pamndandanda wathu wolandira zotsatsa sikutanthauza kuti simungalandire mauthenga okhudza ntchito zathu omwe si otsatsa, monga zosintha ndi zidziwitso zofunika.


Ngati mutsitsa (download) pulogalamu iliyonse ya pa foni yam'manja kuchokera ku Apple AppStore™ kapena Google Play™ kupita ku chipangizo chanu, njira yokhayo yoletsera kulandira zidziwitso ndiyo kusintha makonzedwe (settings) a pa chipangizo chanu chomwecho.


Timagwiritsa ntchito ukadaulo wotsatsa wa makampani ena kuti tionetse zotsatsa pamene mukugwiritsa ntchito Ntchito zathu. Mutha kudzichotsa m'magulu ambiri otsatsa a makampani ena, kuphatikizapo aja omwe amayendetsedwa ndi mamembala a Network Advertising Initiative ("NAI") ndi Digital Advertising Alliance ("DAA").


Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene mamembala a NAI ndi DAA amagwiritsira ntchito zambirizi, komanso zosankha zanu zokhudza kugwiritsidwa ntchito kwa zambirizi ndi makampaniwa, kuphatikizapo mmene mungadzichotsere m'magulu awo otsatsa, chonde pitani pa mawebusayiti awo:

www.networkadvertising.org/optout_nonppii.asp and www.aboutads.info/choices.


Timagawana Uthenga ndi ndani?

Sitimapereka kapena kugulitsa zinsinsi zanu kwa ena. Titha kugawana uthenga wanu wachiinsinsi/chidziwitso ndi ena (“Olandira” Recipient) monga tafotokozera mu ndondomeko yachinsinsi iyi. Uthenga wanu chidziwitso (personal data) udzawululidwa kwa olandira (recipient) okha malinga ndi momwe zikufunikira pa cholinga chenicheni, monga tanena mu ndondomeko yathu ya chinsinsi (privacy policy).


Timagawana uthenga wanu wachidziwitso ndi ena mwa olandira awa:

  • Opereka masewera;

  • Ogwirizana nawo pantchito komanso omwe amapereka ntchito kuchokera kunja, komanso omwe amagwira nawo ntchito, monga (koma osangokhala okhawo) makampani opereka ma cloud okhudza ma kompyuta, othandizana nawo pa kutsatsa malonda, ntchito zowunikira ndikuwona za anthu komanso kupewa chinyengo, komanso ena omwe amafufuza zowona za mauthenga ofunikira.

  • Mabungwe owunikira mbiri ya ngongole, opereka ntchito za ndalama komanso makampani opereka ntchito za KYC, kuti afufuze dzina, malo opezekela komanso zaka. Izi zikuphatikizapo:

    • Zambiri za umunthu wanu ndi uthenga wakapezekedwe kanu;

    • Zambiri zokhudza kugawana kwa malipiro anu; komanso

    • Zambiri zokhudza kupewa chinyengo.

  • PSP, omwe amayang’anira malipiro, ndi mabanki;

  • Aliyense wakunja kwa kampani amene amakupatsani mphotho yowoneka penanso amene amakonza zochitika zakunja kwa kampani kapena mipikisano m'malo mwa Kampani pena mogwirizana ndi Kampani;

  • Mabungwe othetsera kapena kuthandiza pa vuto la kudalira masewera a njuga; komanso

  • Mabungwe opereka ma layisensi, aboma komanso oyang'anira malamulo, mogwirizana ndi malamulo okhudza nkhaniyi.

Mongoonjezera pa zolinga zomwe zalembedwa mu ndondomeko yachinsinsiyi (privacy policy), timagawana uthenga wanu wa chinsinsi ndi olandirawa pa zolinga zotsatirazi:

  • Kusunga uthengawu m’malo mwathu, mwachitsanzo pogwiritsa ntchito opereka ntchito za cloud ya kompyuta;

  • Kukonza uthengawu kuti utithandizele ndi ntchito zathu za bizinesi (mwachitsanzo: kukonza zolipira ndi madipoziti anu; kutsimikizira kulowa kwanu;

  • kuwunika ntchito zathu; kuzindikira ndi kupewa chinyengo kapena zochita zosaloledwa; ndi zina zotero);

  • Kuchita kafukufuku, kuyeza ukadaulo kapena kusanthula zinthu;

  • Kulankhulana zokhudza malonda omwe akulunjika kwa inu, komanso kutsatsa malonda mogwirizana ndi ndondomeko yathu yotsatsira (onani pamwambapa, m’gawo lotchedwa "Kutsatsa"); komanso

  • Nthawi iliyonse tikakhulupirira mwachikhulupiriro chonse kuti kuwulula uthenga wanu wachidziwitso ndikofunikira kuti titeteze ufulu wathu kapena zolakwa zamalamulo, kuyanjana ndi ndondomeko zathu, kuteteza chitetezo chanu kapena cha ena, komanso kufufuza kapena kupewa chinyengo chilichonse, chifukwa cha chitetezo kapena kutithandiza ndi mavuto ena okhudzana ndiza ukadaulo.


Kutumiza uthenga kumayiko ena

Uthenga wachidziwitso (private data) umene timasonkhanitsa kuchokera kwa inu, timatha kuuutumiza kumayiko ena kapena kusungidwa ndi mabungwe apadziko lonse. Ungathenso kukonzedwa ndi makampani omwe amagwira ntchito m'mayiko ena, omwe amagwira ntchito m’malo mwathu kapena m'malo mwa m'modzi wa omwe amatipatsa ntchito. Mwachitsanzo, ma seva a makompyuta omwe amagwiritsidwa ntchito kusungira tsamba lawebusayiti atha kukhala m'mayiko ena – izi si zodabwitsa chifukwa intaneti ndi malo apadziko lonse.


Tidzasunga uthenga wanu wachinsinsi m'malo okhawo omwe amapereka chitetezo cha deta chofanana kapena choposa chomwe chimaperekedwa ndi malamulo a chitetezo cha uthenga. Tikudzipereka kutenga njira zonse zoyenera zotetezera uthenga wanu wachinsinsi mogwirizana ndi ndondomeko yathu yachinsinsi tikamawusamutsa motere.


Kutumiza kulikonse kwa uthenga wanu wachidziwitso mkati mwa dziko lino kapena kudutsa malire kupita kwa omwe amatipatsa ntchito, kudzachitika mogwirizana ndi malamulo oyenera achitetezo cha uthengawu.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza kutumiza uthenga wanu wachinsinsi kupita kumayiko ena, chonde tifikileni mwachindunji pa data.protection@betpawa.com.


Ukadaulo wofufuza uthenga kuchokera kuma kampani ena akunja

Mukamalowa kapena kugwiritsa ntchito maserevisi athu, timagwiritsa ntchito (ndiponso timalola ena akunja kugwiritsa ntchito) mawebusayiti okhala ndi zizindikiro ngati, ma cookies, ma pixel, ma script, ma tag ndi matekinoloje ena ("Ukadaulo wofufuza uthenga" “tracking technologies”).


Ukadaulo wofufuza uthengawu umatilola kuti tisonkhanitse zambiri zokhudza inu ndi momwe mumachitira pa intaneti, komanso chipangizo chimene mukugwiritsa ntchito (mwachitsanzo kompyuta kapena foni yam'manja), pazifukwa zosiyanasiyana monga kusintha momwe mumayendera pa tsamba lathu, kukonza magwiridwe antchito zathu, komanso kusintha zomwe mumakumana nazo mukamagwiritsa ntchito tsamba lathu.Timagwiritsanso ntchito ukadaulo wofufuza uthengawu posonkhanitsa ziwerengero zokhudza momwe ntchito zathu zikugwiritsidwira ntchito, kusanthula, kupereka zinthu zomwe zikugwirizana ndi zomwe mumakonda, komanso kuyang'anira ntchito zomwe timapereka kwa ogwiritsa ntchito athu, otsatsa, ofalitsa, makasitomala ndi othandizana nawo.


Timathandizanso anthu ena akunja kusonkhanitsa zambiri za inu pogwiritsa ntchito ukadaulo wofufuza uthengawu. Kuti mudziwe zambiri, onani Ndondomeko Yathu ya Ma Cookies.


Ntchito za ma kampani ena akunja

Mukamagwiritsa ntchito maserevise athu, mukhoza kukumana ndi ma link okupititsani kumawebusayiti ena, kapena mapulogalamu a anthu ena akunja. Chonde kumbukirani kuti ndondomeko ya uthenga wachinsinsi iyi siyikugwira ntchito pa mawebusayiti amenewa, kapena mapulogalamu a anthu ena akunja, ngakhale akupezeka, kutsitsidwa (downloadable), kapena kugawidwa kudzera ma serevisi athu.


Chonde dziwani kuti mawebusayiti, kapena mapulogalamu (App) aanthu ena akunja amenewa ndi odziyimira pawokha ndipo alibe cholowa nafe. Ife sitikutenga udindo uliwonse wokhudza nkhani za chinsinsi kapena nkhani zina zamalamulo zokhudzana ndi mawebusayiti ndi/kapena ntchito za ma kampani ena amenewa. Tikukulimbikitsani kuti muwerenge mosamala ndondomeko zawo zachinsinsi (privacy policy) komanso malamulo awo ogwiritsira ntchito, chifukwa malamulo awo – osati athu – ndi amene agwire ntchito pa mgwirizano wanu uliwonse ndi makampani ena amenewo.

Muyenera kuyang’anitsitsa mwatsatanetsatane mmene amasungira uthenga wanu wachidziwitso (personal data) musanapereke zambiri zachinsinsi chanu kwa makampani ena akunja amenewo.


Mukuvomereza mwadongosolo komanso mwakufuna kwanu zonse zomwe zingachitike chifukwa chogwiritsa ntchito mawebusayiti amenewa, kapena mapulogalamu (App) aanthu ena akunjawa. Mukuvomera kuti ife sitikhala ndi udindo uliwonse wokhudza mawebusayiti amenewo kapena kugwiritsa ntchito kwanu kwa ntchito zawo.


Kusunga zidziwitso zaumwini wa akaunti yanu

Ngati mwatsegula akaunti kudzela ku kampani yathu, tidzasunga zambiri za zaumwini wa akaunti yanu kwa nthawi yomwe akaunti yanu ikadali yogwira ntchito. Kuphatikizapo, tidzasunga zambiri zaumwini wa akaunti yanu kwa nthawi yowonjezera ya zaka 7, monga momwe ziyenera kukhalira zofunikira kuti tithe kukwaniritsa zofunikira zathu zalamulo pansi pa malamulo kapena malamulo omwe akugwiritsidwa ntchito, monga malamulo a beti, malamulo omudziwila kasitomala (KYC) ndi malamulo otetezela nchitidwe ozembesa ndalama mosayenela (AML), komanso kukwaniritsa udindo wathu wamgwirizano.


Povomereza migwirizano yathu, mukuvomereza nthawi yosungirako zambiri zaumwini monga tafotokozera mu ndondomeko yathu ya zachinsinsi.


Pakatha nthawi yosungirako akaunti yanu, tidzachotsa zambiri zaumwini wa akaunti yanu, kapena tidzachotsa zizindikiro zomwe zingakudziwitseni kuti imeneyi ndi akaunti yanu, m’njira yoti sizingatheke kubwezeretsanso munjira yomveka bwino.


Ufulu wanu

Muli ndi ufulu wotsatirawu womwe mutha kugwiritsa ntchito poyankhulana nafe nthawi iliyonse kudzera pa imelo ku data.protection@betpawa.com :

  • Kugwilitsa ntchito akaunti yanu komanso kuchotsa uthenga winaulionse wachidziwitso choti ndi akaunti yanu.

  • Kukonza kapena kusintha Zambiri zaumwini wa akaunti yanu zokukhudzani (mwachitsanzo, ngati mukukhulupirira kuti zambiri zanu zaumwini si zolondola, mutha kupempha kuti zikonzedwe kapena zichotsedwe)

  • Kuletsa kapena kuyimitsa kugwiritsidwa ntchito kwina kulikonse kwa zambiri yanu ku akaunti

  • Timapereka Zambiri zaumwini zomwe munazipereka kwa ife mwakufuna kwanu, m’njira yomwe makina angathe kuziwerenga.

  • Kuchotsa chilolezo chanu chokhudza kukonzedwa kwa Zambiri zanu zaumwini (monga pa zolinga zotsatsa pa msika);

  • Kuchotsa chilolezo chanu pa zochita zathu zokonza Zinthu (ngati zochita zimenezi zimatengera chilolezo chanu, osati ngati mbali ina ya malamulo);

  • Kukana kukhala pansi pa chisankho chochitika chokha ndi makina, kuphatikizapo kupanga mbiri ya umunthu, chomwe chingabweretse zotsatira za malamulo kapena zina zomwe zingakhudze kwambiri moyo wanu.

  • Kukana kukhala pansi pa chisankho chochitika kokha ndi makina, kuphatikizapo kupanga kafukufuku wa mbiri yanu, chomwe chingabweretse zotsatira za malamulo zokhuza inu kapena zingakukhuzeni kwambili;

  • Kupereka madandaulo ku Bungwe loona za Chitetezo cha malipoti.

Chonde dziwani kuti ma ufuluwa si okhazikika nthawi zonse, ndipo pempho lililonse limayenera kutsatira zofunikira za malamulo omwe akugwiritsidwa ntchito, kuphatikizapo malamulo okhudza beti komanso zofunikira zina zamalamulo ndi zachikhalidwe zokhudza lipoti kapena kusunga zolemba. Titha kukonza, kuwonjezera, kapena kuchotsa zambiri zomwe si zokwanira kapena ndi zolakwika, nthawi iliyonse ndi motsatira chisankho chathu, mogwirizana ndi malamulo athu amkati.


Timadzipereka posunga zambiri zanu zaumwini kwa nthawi yoikika yoyenela kuti tikwaniritse zolinga zomwe zinapangitsa kuti zisonkhanitsidwe ndi kukonzedwa, pokhapokha ngati malamulo, mgwirizano, kapena chilolezo chikufuna kapena chimalola nthawi yosiyana.


Momwe timasungira zambiri zanu motetezeka.

Timasamala kwambiri pakukhazikitsa ndi kusunga chitetezo cha Services ndi chidziwitso chanu.poyika ndi kusamalira chitetezo cha ntchito zathu komanso zambiri zanu.


Takhazikitsa njira zachitetezo zooneka ndi zamakono kuti zitithandize kupewa kulowa kwa anthu osaloledwa, kusunga chitetezo cha zambiri yanu, komanso kugwiritsa ntchito bwino malipoti amene timasonkhanitsa.


Njira zachitetezozi zimakhala zosiyana malinga ndi kufunikila kwa malipoti amene amatoleledwa komanso kusunga.


Timagwiritsa ntchito njira ndi malamulo ovomerezeka m’makampani kuti titsimikizire chitetezo cha zambiri za ogwiritsa ntchito, monga:

  • Dongosolo lotetezedwa la netiweki, lomwe limaphatikizapo njira zopewera zolowerera mwachinyengo komanso makina a kompyuta achitetezo;

  • Kulankhulana ndi kusungirako Zambiri Zaumwini m’njira yotetezedwa komanso yachinsinsi;

  • Kutsimikizira kwa ogwiritsa ntchito ndi kuwongolera mwayi wolowera;

  • Mayeso a kuwona bwino ntchito zakunja ndi zamkati mwa kampani;

  • Kukhazikitsa ndi kukonza zodzitetezera zoyenera ku zoopsa zomwe zadziwika

  • Kutsimikizira pafupipafupi kuti njira zotetezera zikugwiritsidwa ntchito moyenera.

  • Kusintha pafupipafupi njira zotetezera kuti zigwirizane ndi zoopsa kapena zofooka zodza mwatsopano.

Kuphwanya kulikonse kwa malipoti kudzayendetsedwa motsatira ndondomeko yodziwitsa za kuphwanya kwa malipoti, monga momwe zalamulidwa ndi Malamulo Oteteza malipoti.


Kusintha kwa Ndondomeko Yazinsinsi

Tili ndi ufulu wosintha Ndondomeko Yazinsinsi iyi nthawi iliyonse, chonde pitaninso patsamba lino pafupipafupi.


Tidzapereka chidziwitso chakusintha kwakukulu kwa Ndondomeko Yazinsinsiyi potumiza mawu osinthidwa patsamba lathu.


Chidziwitso cha zosintha zazikulu za Ndondomeko Yachinsinsi chikhoza kufuna kuti muwerenge ndi kuvomereza musanapitirize kugwiritsa ntchito ndikulowanso ku akaunti mwanu.


Momwe mungalumikizirane nafe

Ngati muli ndi mafunso ena okhudza Ntchito kapena zambiri zomwe timasonkhanitsa zokhudza inu komanso mmene timazigwiritsira ntchito, chonde lemberani kudzera pa imelo ku data.protection@betpawa.com.


Ngati simukukhutira ndi yankho lathu pa funso lanu, mutha kulumikizana ndi bungwe loyang’anira chitetezo cha zambiri m’dziko lanu lomwe lingakupatseni malangizo okhudza zomwe mungachite potsatira.



Back to top
Not logged in-Join NoworLogin