Uthengawu ulinso mu Chingerezi

Responsible Gambling

Timakhulupilira mu kusewela beti moyenera ndipo timafuna kuti nthawi zonse muzisangalala ndi kusewera nafe koma mukukhalabe olamulira maseweledwe anu ndikungo betela zomwe mungakwanitse. Ngati mukuona kuti kusewela beti kwakhala vuto, tiuzeni ndipo tidzalumikizana kuti tikuthandizeni.


Mukuda nkhawa ndimene mumasewelela beti?

Tiyeni tikambirane kuti tione momwe tingakuthandizireni.


Pemphani kuyimbilidwa foni mwaulere

+265
Enter your phone number without the country code (e.g., 123456789).
Expect a call in:
0-5 minutes
Log in or Join now to experience more

Kapena imbani ku Harmony Mental Wellness kuti mulandile thandizo moyenelela.

Ngati mungafune kulankhula ndi akatswiri odziyimira pawokha, timalimbikitsa Harmony Mental Wellness.

Lumikizanani ndi mlangizi wodziwa zambiri nthawi iliyonse maola 24 patsiku masiku 7 pa sabata, Lolemba mpaka Lamulungu kudzera poimba foni pa nambala iyi +265 880 011 119 kapena WhatsApp pa nambala iyi: +265 888 200 222.


Chonde ingoyimbirani manambala omwe ali pamwambapa ngati mukufuna upangiri. Kuti muthandizidwe zokhudzana ndi akaunti yanu ya betPawa, lumikizanani nafe podina https://www.betpawa.mw/help#contact-us kuti mulakhule ndi a gulu lathu.


Kusunga ulamulilo

Tikufuna kuti musangalale ndi nthawi yomwe mumasewela beti ndi ife. Nawa malangizo angapo owonetsetsa kuti mukutelo:

  • Ganizirani kusewela beti ngati mtundu wina obwelesa chisangalatso, osati njira yopezela ndalama.

  • Vomelezani kuti beti ndi masewera amwayi popanda njira zotsimikizira kupambana

  • Musalole masewela a beti kusokoneza zochita zanu za tsiku ndi tsiku ndi udindo wanu wabanja

  • Pewani kusewela beti mukamamwa mowa kapena mukapsinjika maganizo

  • Khazikitsani milingo yotsika mtengo yopangila dipoziti ndalama yatsiku/sabata/mwezi ndikukhala okhazikika pamalile amenewa.

  • Musapitilize kusewela beti pamene simukupambana kapenanso kuigwiritsa ntchito ngati njira yobwenzela ngongole.

  • Pumulani pafupipafupi ndikulondoloza ndalama zomwe mumasewelera.

Yang'anirani kabetedwe kanu

Mudziyang’anila malipoti a akaunti yanu pafupipafupi kuti muwongolere kabetedwe kanu, ndalama zomwe mukuika komanso zomwe mukuchotsa. Lowani ku akaunti kwanu ndikudina pamene palembedwa kuti STATEMENT pamene mumapapeza mukadina polemba akaunti.

Ngati simukukondwela ndi zomwe mukuwona, ganizirani kutenga imodzi mwazinthu zothandizira zomwe zaperekedwa patsamba lino.


Zizindikiro za chiopsezo

Ngati mukusewera masewero a beti koma zikuonetsa kuti ndichiphinjo ndipo mukulephela kusiya, zikusonyeza kuti pali vuto. Izi ndi zizindikiro zina zofunika kuziyang'anira, ngakhale pangakhale zina.

Ngati muzindikira zingapo, tikulimbikitsa kuti mufufuze thandizo:

  • Mumawona beti ngati njira yopezera ndalama

  • Kusewela beti kumasokoneza moyo wanu watsiku ndi tsiku komanso udindo wabanja

  • Mukumanyalanyaza zofunika zamoyo wanu monga chakudya ndi kugona chifukwa cha beti

  • Mukubetela kuposa momwe mungathere

  • Mumaba kapena kubweleka ndalama kuti mubwenzeretse zomwe mwaonongapo chifukwa cha beti

  • Mumasewera bet chifukwa cha kukhumudwa kapena malingaliro ena oipa.

  • Mukuyesa kubisa kuti mumasewera kapena zotsatila zomwe masewerowo akukubweretserani.

  • Mwalephera mobwerenzabwerenza kuyesa kuwongolera mmene mumasewelera masewero a bet

  • Ena amati muli ndi chizolowezi chosewela bet

Kudzipatula Nokha

Ngati mukukhulupirira kuti mungakhale ndi vuto la beti, chonde ganizirani kudzipatula.

Kodi kudzipatula ndi chiyani?

Kudzipatula ndipamene timatseka akaunti yanu mwa pempho lanu. Pali njira ziwiri: zosakhalitsa komanso zokhazikika. Kupatula kwakanthawi kumapangitsa akaunti yanu kukhala yosafikirika mpaka mutakonzeka kubwereranso. Kudziletsa kosatha sikusinthika, kutanthauza kuti simudzatha kugwiritsanso ntchito akaunti yanu nthawi iliyonse mtsogolo.

Nthawi zonse kasitomala akadzipatula, timachita chilichonse chomwe tingathe kuti izi zilemekezedwe. Chonde musayese kulambalala njira zathu kuti muyambenso kubeta chifukwa sitikhala ndi udindo ngati izi zichitika.

Mukufuna kudzipatula?

Mutha kutseka akaunti yanu podina https://www.betpawa.mw/self-exclusion kapena kupempha foni yaulere pansipa ngati mukufuna thandizo kuti zichitike.


Pemphani kuyimbilidwa foni mwaulere

+265
Enter your phone number without the country code (e.g., 123456789).
Expect a call in:
0-5 minutes
Log in or Join now to experience more

Chifukwa chiyani kudzipatula?

Ndi njira yotsimikizika yothandizira kuthana ndi mavuto a beti. Akaunti yanu ikatsekedwa, timalangiza kuti tibwerere ku zochitika za tsiku ndi tsiku zomwe zimakhudzidwa ndi kubeta, ndi kufunafuna thandizo lina ngati kuli kofunikira.


Kuletsa ana osavomerezeka kusewera beti

Polembetsa ndi kubeta ndi betPawa, mumatsimikizira kuti muli ndi zaka zosachepera 18. Tili ndi ufulu wotsimikizira zaka zanu ndipo titha kukulepheretsani kugwiritsa ntchito akaunti yanu ngati pali kukaikira za zaka zanu. Ngati mwapezeka kuti ndinu achichepere, zopambana zanu zonse zidzalandidwa ndipo akaunti yanu idzatsekedwa. Makasitomala onse omwe amagwiritsa ntchito beti ya Kampaniyi omwe amadziwika kuti ndi wocheperako adzalandidwa zopambana zonse ndipo akaunti yake ya beti idzayimitsidwa.


Malire a Deposit

Ku betPawa, tikufuna kuti osewera onse azikhala ndi ulamuliro pa masewera awo komanso kubetcha mwanzeru.

N’chifukwa chake tayambitsa malire pama Deposit anu, iyi njira yokuthandizani kuwongolera ndalama zimene mumagwiritsa ntchito.

Mungakhazikitse nokha malire a deposit pamwezi, kutsatira momwe mukusewelela, ndiponso kulandira uthenga mukafika pa malirewo.

Zonsezi zili m’manja mwanu. Mungasinthe, kuchotsa, kapena kusinthanso malire anu nthawi iliyonse.

Malire anu azidzikonzanso okha mwezi uliwonse, kuti muyambe mwezi uliwonse mwatsopano.

Iyi ndi imodzi mwa njira zimene timagwiritsa ntchito kukuthandizani kukhala ndi ulamuliro komanso kubetcha mwanzeru.

Dziwani zambiri


Back to top
Not logged in-Join NoworLogin