Uthengawu ulinso mu Chingerezi


Malamulo onse a beti yamasewera

Malamulo Onse

Kampani ili ndi ufulu wokonza zolakwika zomveka bwino zomwe zachitika panthawi yomwe mwabeta mitengo kapena pakuwunika zotsatira za kubeta ngakhale zitachitika magemu aja akatha, kapena kulengeza kuti mabeti omwe akhudzidwa ndi opanda ntchito (void). Ndi udindo wa kasitomala kuonetsetsa kuti wayika bet yake moyenera.


Nthawi zambiri, kubeta kumatsekedwa nthawi yomwe ma gemu omwe mwabetela akakhala kuti ayamba. Nthawi zina mipira kapena mipira imayamba msanga kuposa nthawi yomwe inasankhidwa poyamba, kampani isanadziwe, kapena kampani ikakhala ndi nthawi yolakwika yoyambira. Mabets onse omwe alandilidwa pambuyo poti chochitikacho chayamba, adzathetsedwa.


Malamulo a kampani okhudza ndalama zochepa ndi zazikulu zomwe zimaloledwa kubeta angapezeke kuchokera ku section 11 on T&C page


Ngati wogwiritsa ntchito atayika mabeti ambiri ofanana (kuphatikiza a payekha kapena osakanizidwa) omwe kupambana kwake kudzaposa malire a ndalama zomwe kampani imalola pa betslip imodzi, kampani ili ndi ufulu wochepetsa betyo kuti igwirizane ndi malire omwe ali.


betPawa ili ndi ufulu wosunga malipiro komanso kulengeza mabeti a pa chochitika kukhala opanda ntchito (void) kapena kuthesa ngati tili ndi umboni wakuti izi zachitika: (i) kukhulupirika kwa chochitikacho kwatsutsidwa;

(ii) mitengo kapena ndalama zogwiritsidwa ntchito zasokonezedwa; kapena (iii) ngati zosatila zampira zachita kukonzedwa (match fixing). Umboni wa izi ungachokere pa kuchuluka, kuchuluka kwa ndalama, kapena mawonekedwe a mabeti omwe adayikidwa ndi betPawa m’njira iliyonse ya mabeti omwe alipo. Ngati pali chisankho chomwe chaperekedwa ndi bungwe loyang’anira masewera okhudzidwa (if any), chisankhocho chidzakhala chomaliza. Ngati kasitomala ali ndi ngongole ku betPawa pachifukwa chilichonse, kampani ili ndi ufulu woti ichite kuwerengera ngongoleyo isanapereke ndalama kwa kasitomala ameneyo.


Ngati chochitika china chikachitika chomwe sichili bwino kapena sichikuphatikizidwa mu malamulo awa, kampani ili ndi ufulu woti isankhe zomwe zichitike pa chochitika chilichonse potengera momwe zinthu zilili.


Mitundu ya Mabeti

Kampani imavomereza kubeta gemu imodzi pa tiketi yanu (single bets) komanso kubeta kwa magemu angapo (multiple bets) mpaka mutha kusankha magemu 60 (makumi asanu ndi limodzi).


Mukabeta tiketi yomwe ilindi magemu awiri imatchedwa kuti 2-leg multibet kapena double. Tiketi yomwe ili ndi zosankha zitatu zogwirizana kumatchedwa 3-leg multibet kapena treble, ndi zina zotero.


Kusintha kwa Malo a Masewera

Ngati masewerawo sachitika pamalo omwe adakonzedweratu, kapena ngati gulu limodzi silikugwirizana ndi magulu omwe adatchulidwa poyamba pamasewera amenewo, Kampani ili ndi ufulu wochotsa kapena kuletsa kubetcha konse komwe kumakhudzana ndi masewera amenewo.


Kubeta Kogwirizana

Kubeta kwa tiketi yosakaniza (multibet) sikuvomerezeka ngati kuli kugwirizana pakati pa zosankha (dependency), pokhapokha ngati kampani yapereka mitengo yapadera (special prices) pa kuphatikizana kumeneku.


Ngati kubeta kogwirizana kwayikidwa mwangozi — chifukwa cha zolakwa za munthu kapena za ukadaulo — Kampani ili ndi ufulu wochotsa kapena kuletsa beti yamtundu umenewu.


“Kugwirizana” kumatanthauza kuti zotsatira za kubetcha kumodzi zimakhudza kapena zimakhudzidwa ndi zotsatira za kubetcha kwina. Chitsanzo cha kubeta kogwirizana: Manchester United kuti apambane gawo loyamba & Manchester United kuti apambane masewerawo onse. Zotsatira za masewera onse zimadalira zomwe zachitika pa gawo loyamba, choncho izi zimawerengedwa ngati kubeta kogwirizana.


Kuwonetsa Masewera

Gulu loyamba lomwe likuwonetsedwa limawerengedwa ngati gulu lomwe likusewera pakwao (home team), ndipo gulu lachiwiri limawerengedwa ngati gulu loyenda (away team).


Ngati masewerawo achitika pamalo oti siatimu ina iliyonse (neutral venue), chizindikiro cha (n) chidzawonetsedwa pambuyo pa dzina la masewerawo.


betPawa imaperekanso mwayi obeta masewera a mpira wa achinyamata (youth football). Ngati masewera ndi a gulu la achinyamata, zimasonyezedwa mu kufotokozera kwa masewera ngati U19, U23, ndi zina zotero.


Chonde samalani mukamabeta, chifukwa England–Germany U19 imatha kusokonezedwa ndi England–Germany (senior match). Choncho, onetsetsani kuti mwatsimikiza mtundu wa masewerawo musanayike pabeti yanu.


Kubeta Magemu oti alimkati mosewera

Zambiri Zonse (General): Mukamabeta mipira yoti ikuseweledwa (In-Play), mitengo imasinthasintha nthawi zonse ndipo msika (markets) ya kubeta imatha kuoneka kapena kusowa mwadzidzidzi. Kubeta koti mmasewera alimkati kumakhala kosangalatsa komanso kosangalatsa kwambiri, ndipo kumatha kuwonjezera chisangalalo mukamawonera masewera. Kubeta kwamasewera oti alinkati (live betting) kungakhale kubeta kwagemu imodzi (single bet) kapena kubeta kwa magemu ochuluka (multibet).


Mitundu ya mabeti (Bet Types): Mitundu ya masewera ndi mitengo yomwe imaperekedwa imadalira chisankho cha Kampani. Sititsimikizira kuti mtundu uliwonse wa beti udzakhala ukupezeka nthawi zonse pa masewera. Mwachitsanzo: ngati timu ikutsogola 3–0 pambuyo pa mphindi 82, kubeta kwa 1X2 sikukhalanso kogwira ntchito, koma kubeta pa over/under 3.5 goals kumakhalabe kofunikira. Kampani ili ndi ufulu wosiyitsa (suspend) kubeta kulikonse kapena msika wonse nthawi iliyonse popanda chidziwitso choyambirira.


Zambiri Zowonetsedwa & Scoreboard (Information Displayed & Scoreboard): Timayesetsa kuonetsetsa kuti zambiri zonse zomwe zikuwonetsedwa panthawi yomwe ikuseweredwa (Live) ndizolondola. Komabe, zambiri zomwe zikuwonetsedwa monga zotsatira kapena nthawi yomwe masewerawo aseweredwa, zimangoperekedwa ngati chitsogozo chokha, ndipo Kampani silinavomereze udindo uliwonse ngati zambiri zomwe zikuwonetsedwa sizolondola.


Kuchedwa Pokonza beti (Bet Processing Delays): Pachitetezo, kubeta kulikonse komwe kumayikidwa pa masewera oti akumenyedwa kumachedwetsedwa mwachindunji. Osewera omwe akubeta angakumane ndi kuchedwa kwa mpaka masekondi 10, kutengera mtundu wa masewera, malo omwe masewerawo akuchitikira, ndi liwiro la intaneti yanu.


Kuwona Pamoyo (Live Vision): Chonde dziwani kuti mawu oti live omwe amagwiritsidwa ntchito ndi ena mwa otsatsa ma TV kapena oonera sitanthauza nthawi yeniyeni nthawi zonse. Mutha kuwona zomwe zikuoneka ngati masewera oti alinkati pomwe kwenikweni zachedwa. Choncho, samalani mukamabeta potengera zomwe mukuwona pa TV kapena pa intaneti.


Kubeta Kwayikidwa Itatha (Past-post): Ngati Kampani itatsimikiza kuti kubeta kwina kwachitika masewerawo atatha kapena mutangopita patsogolo mwazotsatira (monga chigori), kubeta konse komwe kukukhudzidwa kudzachotsedwa kapena kuletsedwa (cancelled).


Zotsatira (Results): Timayesetsa kuwonetsetsa kuti mabeti onse atsimikizika (resulted) mwachangu masewerawo akangotha. Komabe, dongosolo lathu limafunika kutsimikizira zotsatira kuchokera m’magwero awiri odalirika kuti tikhazikitse molondola. Izi zitha kutenga mphindi zochepa. Ngati zotsatira sizingatsimikizidwe nthawi yomweyo, timadikira mpaka chitsimikizo chenicheni chapezeke. M’masewera otsika monga mpira wa m’magulu otsika kapena tennis, zingafunike kuleza mtima pang’ono.


Zotsatira Zovomerezeka

Zotsatira za mabeti zimadalira zomwe zachitika pamasewera pa ground. Zigamulo kapena zisankho zomwe zikuchitika pambuyo pa masewera kuchokera ku mayiko a malamulo, mabungwe a masewera, kapena mabungwe olamulira zomwe zimakhudza kapena kusintha zotsatira za pamunda sizidzaloledwa pamabeti anu.


Ngati timu yosewera pakwawo (home team) lisankha kusewera pamalo ena osati malo ake, malowo azawelengedwabe ngati apanyumba(home ground), ndipo chizindikiro cha (n) sichigwiritsidwa ntchito.


Kuphulira kolakwika

Mabeti omwe aphulilidwa (Cashed Out) ndi kasitomala, ngati ndalama zomwe zidaperekedwa si zolondola chifukwa cha zolakwa pamitengo (odds), zidzayesedwa kachiwiri ndikukonzedwa ndi ndalama zolondola. Kukonzedwa uku kungachitike magemu akayamba kumene, kapena ikakhala kuti ikuseweredwa (In-Play), kapena pambuyo pa masewera.


Kuwonetsa Nthawi

Masiku ndi nthawi zonse zomwe zikuwonetsedwa zili mu Greenwich Mean Time (GMT+3).


Malamulo a Mabeti a Mpira (Football/Soccer Betting Rules)

Nthawi ya Masewera

Ngati masewera akakonzedwa kuseweredwa m’njira ina kuposa nthawi ya mwachikhalidwe ya 2x45 minutes kuphatikizapo nthawi yolipira zolakwika (injury time), mabeti onse a mtundu umenewu amachosedwa (voided).


Titha kulora (Exception): Masewera a ubwenzi (friendly matches) akhoza kukhala osiyana. Pa masewera amenewa, mabeti onse amasankhidwa malingana ndi zotsatira zenizeni za masewerawo, ngakhale 90 minutes ya nthawi yokhazikika yasiyidwa kapena kusakhazikika.


Masewera oimisidwa

Masewera oimisidwawa (abandoned) ndi omwe amayamba koma osafika mpaka pamapeto ake mwachikhalidwe mkati mwa maola 24.


Gemu ikaimisidwa (abandon), timadikila maola 24 kuti iseweledweso kapena ayi. Zikakhala kuti maola 24 atha ndipo gemuyo sinaseweledweso, ngati pa betslip yanu panali game imodzi ndekuti timakubwenzelani ndalama yomwe munabetela (stake) koma ngati panali ma game angapo ndekuti timachotsapo game imeneyo ndi ma odds ake ndikukupatsani ndalama zama game otsalawo. Ma beti onse omwe zotsatira zake zasankhidwa kale (mwachitsanzo zosatila zapa halftime kapena first team to score) tizawelengela.


Ngati masewerawo aletsedwa ndipo abwezeretsedwanso mkati mwa maola 24, koma amasewera kuyambira mphindi yoyamba (minute 1), kubetcha konse kudzayesedwa kachiwiri malinga ndi zotsatira zatsopano.


Bonus yomwe ili pa betslip idzakonzedwanso ngati masewera aletsedwa asabwezeretsedwanso mkati mwa maola 24.


Kuchinya Zigoli

Timu imawerengedwa kuti yachinya chigori ngakhale ngati chigoli chachinyidwa ndi timu yomwe akusewera nayo (own goal) kapena lapangidwa kudzera pa penalty kick pa nthawi ya masewera wamba kapena injury time.


Ngati masewerawo atayamba koma asanathe (final whistle/buzzer), kubeta komwe kutha kutsimikizidwa pa nthawi yolepheretsa masewerawo kudzapitilira (stand). Kubeta konse komwe sikungatsimikizidwe panthawiyo, kuphatikizapo kubeta pa zotsatira zonse za masewerawo (game outcome), kudzachotsedwa (voided). Mabeti omwe alindi gemu imodzi (single bets) zidzabwezedwa ndalama zake (bet stake refunded). Magemu oti pali magemu ochuluka zidzakhalabe valid, koma masewerawo adzachotsedwa pa betslip.


Malo osewerera opanda mwini

Ngati masewerawo achitika pamalo osalowerera mwini (neutral venue), gulu loyamba lomwe likuwonetsedwa patsamba lathu lidzawerengedwa ngati gulu la pakhomo (home team), ndipo gulu lachiwiri lidzawerengedwa ngati gulu la yoyenda (away team). Masewera amtunduwu adzasonyezedwa ndi chizindikiro cha (n) kuti chizindikitse kuti akuchitika pamalo osalowerera ndale.


Masewera Osinthidwa Nthawi

Masewera amatchedwa postponed ngati sanayambe pa nthawi yomwe anakonzedwa poyamba, ndipo kuyamba kwake kwasinthidwa kupita pa nthawi kapena tsiku lina.


Ngati nthawi yoyambira (kickoff) yasinthidwa koma masewerawo ayambiranso mkati mwa maola 24 kuchokera pa nthawi yoyamba yomwe anakonzedwa, kubetcha konse kudzapitilira (all bets stand).


Gemu ikapangidwa postpone, timadikila maola 24 kuti iseweledweso kapena ayi. Zikakhala kuti maola 24 atha ndipo gemuyo sinaseweledweso, ngati pa betslip yanu panali game imodzi ndekuti timakubwenzelani ndalama yomwe munabetera (stake) koma ngati panali ma game angapo ndekuti timachotsapo game imeneyo ndi ma odds ake ndikukupatsani ndalama zama game otsalawo.


Bonus yomwe ili pa betslip idzakonzedwanso ngati masewera aletsedwa asabwezeretsedwanso mkati mwa maola 24.


Kutsimikiza Zotsatira za Masewera

Zotsatira za mabeti a masewera a mpira (football/soccer) zimadalira nthawi yokonzedweratu ya masewera kuphatikizapo injury time yomwe yawonjezedwa ndi referee. Nthawi imeneyi imatchedwanso kuti “Regular Time” kapena “90 minutes”.

Pokhapokha ngati zatchulidwa mwapadera pa mtundu wina wa beti, nthawi yoonjezera akafanana mphamvu (overtime) komanso mapenate sizikhudza zotsatira za beti.


Msika wa Makhadi

Khadi lachikasu (Yellow Card) limawerengedwa ngati khadi limodzi (1). Khadi lofiira (Straight Red) kapena khadi lachikasu-lofiira (Yellow-Red) limawerengedwa ngati makhadi awiri (2). lachiwiri lachikasu lomwe limapangitsa kuti wosewera apatsidwe yellow-red card silionjezeredwa, choncho wosewera m'modzi sangathe kupeza makhadi oposa atatu


Zotsatira za beti zimatsimikizidwa malinga ndi umboni wonse womwe ulipo wa makhadi omwe aperekedwa pa nthawi ya masewera 90 minutes zokhazikika kuphatikizapo nthawi yoonjezera (injury time).


Makhadi operekedwa musanayambe kapena mutatha masewera sitiwerengera. Makhadi operekedwa pa nthawi ya half-time break adzawerengedwa ngati operekedwa mu chigawo chachiwiri (2nd half).


Makhadi operekedwa kwa anthu osasewera pa ground monga osewera omwe asinthidwa kale, ma coach, kapena osewera omwe ali pa bench sitiwerengera.


Msika wa Ma Corner

Ma corner omwe aperekedwa koma sanatengedwe (awarded but not taken) sitizawerengera pa mabeti. Ma corner onse amawerengedwa pa nthawi yokhazikika yokha (Regular Time – 90 minutes) kuphatikizapo injury time. Nthawi yowonjezera akafanana mphamvu (overtime) sikuphatikizidwa pa msika uwu.


Zochitika Zosakhazikika Kwambiri

Ngati pakachitika vuto lalikulu kapena chochitika chosakhazikika chomwe chimakhudza mwachindunji zotsatira za masewera a beti, monga: timu kusewera ndi gulu la achinyamata chifukwa cha ndale, kupsinjika, kusagwirizana, matenda, kapena zinthu zina zofanana Kampani ili ndi ufulu wochotsa (cancel) kubetcha konse komwe kwavomerezedwa kapena kulengeza kuti masewerawo ndi osagwira ntchito (void).


Mitundu ya Masewero a Mpira ndi matanthauzo a Zotsatira

1 X 2- Nthawi Ya Thunthu (1X2-Full Time)

1X2 Yomwe imadziwikanso kuti zothatira za masewera kapena 3-Way ndi ndi ntundu odziwika kwambiri pa kubetcha mpira. Cholinga chake ndikunenelatu kapena kulosera zotsatira za masewero pokutha nthawi ya thunthu(osaphatikiza nthawi ya chiwonongeko(Extra Time).


Zosankha (Selections)

1- Gulu la Pakhomo kapena gulu lolembedwa ku manzere(Home Team)

X- Zofana Mpavu (Draw)

2- Gulu lobwera/Alendo kapena gulu lolembedwa ku manja (Away Team)


Chitsanzo (Example)

Real Madrid v Barcelona

Ngati masewerowa atha ndi zotsatira 1-2 kupamba kukhala pa 2. Chifukwa Barcelona ya pambano masewero.


1X2 - Chigawo choyamba (First Half)

Kulosera gulu lomwe lidzapambane chigawo choyamba cha masewera.


Zosankha (Selections)

1- Gulu la Pakhomo kapena gulu lolembedwa ku manzere(Home Team)

X- Zofana Mpavu (Draw)

2- Gulu lobwera/Alendo kapena gulu lolembedwa ku manja (Away Team)


1X2 - Chigawo Chachiwiri (Second Half)

Kulosera gulu lomwe lidzapambane chigawo chachiri cha masewera.


Zosankha (Selections)

1- Gulu la Pakhomo kapena gulu lolembedwa ku manzere(Home Team)

X- Zofana Mpavu (Draw)

2- Gulu lobwera/Alendo kapena gulu lolembedwa ku manja (Away Team)


Over/Under - Nthawi ya thunthu

Kulosera ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa pa nthawi ya thunthu.


Zosankha (Selections)

Over x.5- Pazakhala zigoli zambiri kuposa malire azigoli zopelekedwa.

Under x.5- Pazakhala zigoli zochepera malire azigoli zopelekedwa.


Chitsanzo (Example)

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira za nthawi ya thunthu zinali 1-2, zosankha zinali 2.5 zikhala Over chifukwa zigoli zitatu zagoletsedwa ndipo 3 ndi zambiri kuposa 2.5.


Over/Under - Chigawo choyamba (First Half)

Kulosera ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa mu chigawo choyamba.


Zosankha (Selections)

Over x.5- Pazakhala zigoli zambiri kuposa malire azigoli zopelekedwa.

Under x.5- Pazakhala zigoli zochepera malire azigoli zopelekedwa.


Msika umenewu umapezekanso mu chigawo chachiwiri(Second Half).


Over/Under - Yapakhomo nthawi yathunthu (HOME - Full Time)

Kulosera ngati gulo lapakhomo lizapeze zigoli zochuluka kapena zochepela malire opelekedwa pakutha nthawi ya thunthu.


Zosankha (Selections)

Over x.5- Pazakhala zigoli zambiri kuposa malire azigoli zopelekedwa.

Under x.5- Pazakhala zigoli zochepera malire azigoli zopelekedwa.


Over/Under - Yobwera nthawi yathunthu (Away - Full Time)

Kulosera ngati gulu lobwera lizapeze zigoli zochuluka kapena zochepela malire opelekedwa pokutha nthawi ya thunthu.


Zosankha (Selections)

Over x.5- Pazakhala zigoli zambiri kuposa malire azigoli zopelekedwa.

Under x.5- Pazakhala zigoli zochepera malire azigoli zopelekedwa.



Double Chance- Nthawi yathunthu- (Full Time)

Uwu ndi msika wa kubetcha womwe umachulukitsa mwayi wopamba, m’malo mosankha zotsatira zimodzi zokha (monga mu 1X2) apa mumasankha zotsatira ziwiri, zomwe zimachepetsa chiopsezo poyerekeza ndi ku betcha kwa 1X2.

Zosankha (Selections)

1X- Gulu la Pakhomo kupambana kapena kufananiza mphamvu (Draw).

X2- Gulu lobwera lipambane kapena kufananiza mphamvu (Draw).

12- Papezeke gulo loti lipambane pakati pa gulu lobwera/alendo kapena gulu la pakhomo.


Chitsanzo (Example)

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira za nthawi ya thunthu zinali 1-2, njira zomwe zingapambane ndi X2 ndi 12,chifukwa Barcelona ndi yomwe yapambana. Ngati masewera anathera 1-1, njira zopambana ndi 1X ndi X2, chifukwa masewera athera kufanana mphavu(draw).


Double Chance - Gawo loyamba-(First Half)

Uwu ndi msika wa kubetcha womwe umachulukitsa mwayi wopamba, m’malo mosankha zotsatira zimodzi zokha (monga mu 1X2) apa mumasankha zotsatira ziwiri, zomwe zimachepetsa chiopsezo poyerekeza ndi ku betcha kwa 1X2. Mugawo loyamba.


Zosankha (Selections)

1X- Gulu la Pakhomo kupambana kapena kufananiza mphamvu (Draw).

X2- Gulu lobwera lipambane kapena kufananiza mphamvu (Draw).

12- Papezeke gulo loti lipambane pakati pa gulu lobwera/alendo kapena gulu la pakhomo.

Double Chance - Gawo lachiwiri-(Second Half)

Uwu ndi msika wa kubetcha womwe umachulukitsa mwayi wopamba, m’malo mosankha zotsatira zimodzi zokha (monga mu 1X2) apa mumasankha zotsatira ziwiri, zomwe zimachepetsa chiopsezo poyerekeza ndi ku betcha kwa 1X2. Mugawo loyamba.


Zosankha (Selections)

1X- Gulu la Pakhomo kupambana kapena kufananiza mphamvu (Draw).

X2- Gulu lobwera lipambane kapena kufananiza mphamvu (Draw).

12- Papezeke gulo loti lipambane pakati pa gulu lobwera/alendo kapena gulu la pakhomo.


Both Teams To Score - Nthawi ya Ntunthu (Full Time)

Both teams to score FT (BTTS, Golo/Golo) ndi msika umene mumalosera kuti ma gulu onse awiri achinyana zigori mu nthawi yathunthu.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Magulu onse awiri achinyana zigori pa nthawi yopelekedwa, monga 1-1.

Ayi(No)- Magulo onse awiri sakwanitsa kuchinyana zigoli Kapena imodzi mwa maguluwa ikwaninitse kugoletsa inzake pa nthawi yopelekedwa monga 0-0.


Chitsanzo (Example)

Real Madrid v Barcelona

Ngati zosankha za masewera zathera 1-2, kusankha komwe kungatheke ndi Inde, chifukwa ma gulu onse awiri akwanilitsa kuchinya zigiri.


Both Teams To Score - Gawo loyamba(First Half)

Both teams to score FT (BTTS, Golo/Golo) ndi msika umene mumalosera kuti ma gulu onse awiri agoletsana zigori mu gawo loyamba.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Magulu onse awiri agoletsana zigori mugawo loyamba monga 1-1

Ayi(No)- Magulo onse awiri sakwanitsa kugoletsana zigoli Kapena imodzi mwa maguluwa ikwaninitse kugoletsa inzake mugawo loyamba monga 0-0.


Both Teams To Score - Gawo lachiwiri (Second Half)

Both teams to score FT (BTTS, Golo/Golo) ndi msika umene mumalosera kuti ma gulu onse awiri agoletsana zigori mu gawo lachiwiri.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Magulu onse awiri agoletsana zigori mugawo lochiwiri monga 1-1

Ayi(No)- Magulo onse awiri sakwanitsa kuchinyana zigoli Kapena imodzi mwa maguluwa ikwaninitse kugoletsa inzake mugawo lachiwiri monga 0-0.


2-Way Handicap - Nthawi ya thunthu (Full Time)

2- Way Handicap ndi msika umene mungalosere kuti ndi gulu liti lidzawine masewero pomaliza nthawi ya thunthu. Nthawi yowonjezera ndi mapenati siziwerengeredwa.


Chitsanzo (Example)

1 1.56 Barcelona ili pa -0.5

2 2.65 Real Madrid ili pa +0.5

Mongo yerekeza kuti masewero athera 2-2 kuti afanana mphamvu. Ngati muna betcha Real Madrid pa 2.65 ndi +0.5(ndi kuwonjezera chigoli) ndekuti ku betcha kwanu kwatheka.


Msika umenewu umapezekaso pa gawo yoyamba ndi gawo lachiwiri.


3-Way Handicap - Nthawi ya thunthu (Full Time)

3 way handicap, yotchedwanso European handicap, ndi msika umene mungalosere kuti ndi gulu liti lidzawine masewero pomaliza nthawi ya thunthu pamene handicap yagwiritsidwa ntchito. Nthawi yowonjezera ndi mapenati siziwerengeradwa.


Chitsanzo:

1 2.25 Barcelona ili pa -1.0

X 3.60 Draw ili pa-1.0

2 2.65 Real Madrid ili pa +1.0


Chitsanzo #1:

Mongo yerekeza kuti masewero athera 2-2 kuti afanana mphamvu. Ngati muna betcha Real Madrid pa 2.65 ndi +0.5(ndi kuwonjezera chigoli) ndekuti ku betcha kwanu kwatheka.


Chitsanzo #2:

Mongo yerekeza kut masewero athera 2-2 kuti afanana mphamvu. Ngati munabetcha kuti afanana mphavu ili pa 3.60, i -1.0(kuchotsa chigoli chimodzi) pa Barcelona ndekuti ku betcha kwanu kwakanika.


Msika umenewu umapezekaso pa gawo yoyamba ndi gawo lachiwiri.


Clean Sheet - Yapakhomo (HOME Team)

Mutha kulosere ngati gulu la pakhomo silidzalola kumwetsedwa zigoli kapena kulola gulu linalo kuyesera kubeletsa.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Gulu lapakhomo silidzalola gulu la alendo kuchinya zigoli ziri zonse.

Ayi(No)- Kutanthauza kuti gulu la pakhomo silinakwanitse kusunga clean sheet, kutanthauza kuti lilola gulu la alendo kugoletsa zigoli zosachepela chimodzi.


Clean Sheet - Yobwera (AWAY Team)

Mutha kulosere ngati gulu lobwera silidzalola kumwetsedwa zigoli kapena kulola gulu linalo kuyesera kuchinya.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Gulu lobwera silidzalola gulu la linalo kuchinya zigoli ziri zonse.

Ayi(No)- Kutanthauza kuti gulu lobwera silinakwanitse kusunga clean sheet, kutanthauza kuti lilola gulu lapakhomo kugoletsa zigoli zosachepela chimodzi.


Chitsanzo (Example)

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira zomaliza ndi 1-2, zosankha zopambana zingakhale ndi Ayi, chifukwa Barcelona sinathe kusunga clean sheet chifukwa Real Madrid yagoletsa chigoli chimodzi.


Clean Sheet - Gawo loyamba (First Half)

Muthakulosera ngati gulu lapakhomo kapena lobwera silidzalola zigoli zili zonse mugawo loyamba.


Zosankha (Selections)

Inde(Yes)- Gulu lapakhomo silidzalola gulu la linalo kugoletsa zigoli ziri zonse.

Ayi(No)- Kutanthauza kuti gulu lapakhomoli silizakwanitsa kusunga clean sheet ndipo liza mwetsedwa zigoli zochepa.


Zosankha (Selections)

nde(Yes)- Gulu lobwela silidzalola gulu lapakhomo kugoletsa zigoli ziri zonse.

Ayi(No)- Kutanthauza kuti gulu lobwelali silizakwanitsa kusunga clean sheet ndipo liza mwetsedwa zigoli zochepa


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira za half yoyamba ndi 1-2 zosankha zopambana zingakhale Ayi pa gulu lobwera chifukwa Barcelona siinathe kusunga clean sheet. Chifukwa Barcelona yagoletsa chigoli chimodzi.


Msika umenewu umapezekanso mugawo lachiwiri.


Correct Score - Nthawi yathunthu (Full Time)

Pa msika uwu mumaloserera molondola chiwerengero cha zigoli zomwe zikhalepo pamapeto pa masewero osawerengera ndime yachipulura. Zoloserazi zima lembedwa kuchokera pa gulu la pakhomo kupita ku ku gulu lobwera. Mwachitsanzo, “1-0” zikutanthauza kuti gulu la pakhomo lapambana 1-0.


Zosankha zina zimakhala “Other” zomwe zimatanthauza zotsatira zonse zomwe sizina phatikizidwe pa mndandanda wina monga “0-0, 0-1, 1-0”.


Chitsanzo

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira zatha 1-2 ndiye kuti chipambano ndi 1-2.


Correct Score - Gawo loyamba (First Half)

Apa mumaloserera molondola chiwerengero cha zigoli mu theka loyamba. Zotsatira zimawonetsa zomwe zathera mutheka loyamba. .Mwachitsanzo “1-0” zikutanthauza kuti gulu la pakhomo lapambana mu theka loyamba 1-0.


Chitsanzo

Real Madrid vs Barcelona

Ngati zotsatira zamasewero pakutha nthawi yathunthu ndi 1-2, ndipo gawo loyamba latha 0-0, ddipo gawo lachichiri latha 1-2, zopambana ndi 1-2.


Msika umenewu umapezekanso mu gawo lachiwiri.(2nd Half)


Chigawo choyamba/Nthawi yathunthu (Half Time/Full Time)

Kulosera zotsatira za mu gawo loyamba komanso za masewero onse ndi chisankho chimodzi.


Zosankha (Selections)

1/1 Ya pakhomo/Ya pakhomo (Home/Home)

1/X Ya pakhomo/Kufanana mphamvu (Home/Draw)

1/2 Ya pakhomo/Yobwera(Home/Away)

X/1 Kufanana mphamvu/Ya pakhomo(Draw/Home)

X/X Kufanana mphamvu/Kufanana mphamvu(Draw/Draw)

X/2 Kufanana mphamvu/Yobwera(Draw/Away)

2/1 Yobwera/Ya pakho(Away/Home)

2/X Yobwera/Kufanana(Away/Draw)

2/2 Yobwera/Yobwera(Away/Away)


Chitsanzo

Real Madrid v Barcelona

HT 0-0

FT 1-2


Apa chisankho chopambana ndi X/2 chifukwa choti gawo loyamba lathera mofanana mphamvu ndipo Barcelona yapambana.


Team to Score (4-Way) - Full Time

Apa muma losera amene adzagoletse pa masewero pa kutha nthawi ya thunthu kaya ndi gulu la obwera, onse awiri kapena palibe adza goletse (0-0).


Zosankha (Selections)

Popanda chigoli(No Goal)- Apa mumalosera kuti palibe zigoli zomwe zingagoletsedwe.

Ya pakhomo(Home)- Gulu la pakhomo lokha ndi lomwe lizagoretse zigoli.

Yo bwera(Away)- Gulu lobwera lokha ndi lomwe lizagoretse zigoli.

Onse(Both)- Magulu adza kwanitsa ku chinya zigoli.


1X2 and Over/Under - Nthawi yathunthu (Full Time)

Kulosera zotsatira ndi mulingo wa zigoli zomwe zinga goletsedwe.


Chitsanzo

Real Madrid - Barcelona

Nthawi ya thunthu (FT) score is 2-2

Kubetcha kwanu kwatheka ngati munasankha X-Over(2.5) chifukwa masewerowo athera mofanana mphamvu komanso zigoli zinayi (4) zagoletsedwa.


Msika umenewu umapezekanso mu zigawo zonse gawo loyamba (1st Half) ndi gawo lachiwiri (2nd Half).


Draw No Bet - Nthawi yathunthu (Full Time)

Msika uwu umatanthauza kuti ngati masewero athera mofanana mphavu (draw), ndalama zanu zizabwerera kapena kubwezedwa.


Zosankha (Selections)

1 - Gulu la pakhomo(Home) ku wina

2 - Gulo lobwera ku wina


Chitsanzo

Real Madrid - Barcelona

Ngati zotsatira za masewero ndi 2-2 kubetcha kulikonse kuma bwezedwa.

Ngati Real Madrid yapambana, kubetcha pa “1’ kuma pambana.

Ngati Barcelona ya pambana kubetcha pa “2” kwa pambana.


Home/Away No Bet - Nthawi ya thunthu (Full Time)

Apa mumalosera gulu lomwe lidzapambane, koma ngati masewera atha ndi draw (zofanana), ndalama zanu zimabwezedwa.


Zosankha (Selections):

Home (Pakhomo) – Mumatenga gulu la pakhomo kuti lipambane. Ngati masewerawo atha ndi draw, ndalama zanu zimabwezedwa.

Away (Alendo) – Mumatenga gulu la alendo kuti lipambane. Ngati masewerawo atha ndi draw, ndalama zanu zimabwezedwa.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati masewerowo atha 2–2, kubetcha kulikonse kumabwezeredwa (palibe amene wapambana).

Ngati Real Madrid yapambana, bet ya Home imapambana.

Ngati Barcelona yapambana, bet ya Away imapambana.


Odd/Even – Nthawi Ya thunthu (Full Time)

Apa mumalosera ngati chiwerengero cha zigoli pokutha pamasewerawo chidzakhala chiwerengero chosalingana (odd) kapena chiwerengero chofanana (even).


Kumbukirani kuti 0 (ziro) imawerengedwa ngati even, choncho ngati masewerawo atha 0–0, kusankha kopambana kudzakhala even.


Zosankha:

Odd (Chosalingana) – Pakhale zigoli zokhala ndi chiwerengero chosalingana mu masewera onse.

Even (Chofanana) – Pakhale zigoli zokhala ndi chiwerengero chofanana mu masewera onse.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati masewerawo atha 1–2, kusankha kopambana kudzakhala Odd, chifukwa zigoli onse ndi 3, ndipo 3 ndi chiwerengero chosalingana.


Odd/Even – Gawo Loyamba (First Half)

Apa mumalosera ngati chiwerengero cha zigoli zomwe zidzagoletsedwe mu chigawo choymba cha masewerawo chidzakhala chiwerengero chosalingana (odd) kapena chofanana (even).

Kumbukirani kuti 0 (ziro) amawerengedwa ngati even, choncho ngati chigawo choyamba chatha 0–0, kusankha kopambana kudzakhala even.


Zosankha:

Odd (Chosalingana) – Pakhale zigoli zokhala ndi chiwerengero chosalingana mu chigawo choyamba.

Even (Chofanana) – Pakhale zigoli zokhala ndi chiwerengero chofanana mu chigawo choyamba.

Msika uwu umapezekanso pa chigawo chachiwiri (2nd Half).


Gulu logoletsa chigoli chotsiriza (Team To Score Last) – 3 Way

Apa mumalosera kuti ndi gulu liti lomwe lidzagoletse chigoli chomaliza, kapena ngati palibe chigoli chomwe chidzagoletsedwe.

Zigoli zozigoletsa okha(own goals) zimawerengedwa mu msika uwu.


Zosankha:

1 – Gulu la pakhomo (Home) idzagoletsa chigoli chomaliza.

2 – Gulu la alendo (Away) idzagoletsa chigoli chomsliza

No Goal – Palibe chigoli chomwe chidzagoletsedwe mu masewerawo.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Zotsatira zomaliza: 1–2

Tiyeni tiganize kuti zigoli zinabwera motere: 1–0; 1–1; 1–2.

Pamenepa, kusankha kopambana kudzakhala 2 (Away) chifukwa Barcelona idagoletsa chigoli chomaliza.


Total Goals Exact - Nthawi ya thunthu (Full Time)

Uwu ndi msika womwe mumalosera chiwerengero chenicheni cha zigoli zomwe zidzachitike mpaka masewerowo atatha nthawi yathunthu. 10+ zigoli kutanthauza kuti zigoli zitha kukhala kapena kudusa pa 10.


Zosankha (Selections):

0 goals – Palibe chigoli chidzapezeke (0)

1 goal – Masewerowo adzatha ndi chigoli chimodzi chokha

2 goals – Masewerowo adzatha ndi zigoli ziwiri

3 goals – Masewerowo adzatha ndi zigoli zitatu

4 goals –Masewerowo adzatha ndi zigoli zinayi

5-.....

10+- Masewerowo adzatha nidi zigoli zigoli khumi

kapena kuposerapo.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati masewerowo atha ndi zotsatira za 2-1, ndiye kuti zolosera zonse ndi 3, kotero kusankha kopambana kuli pa 3 goals. Zitati zigoli zinali 6-5 apa owina ndi amene anasankha zigoli 10+


Msika wa “Total Goals Exact” ukupezekanso pa 1st Half (chigawo loyamba) ndi 2nd Half (chigawo chachiwiri).

Komanso msika wa Total Goals Exact Full Time ukupezekanso pa gulu lapakhomo (Home) ndi ya alendo (Away) payekha.


Ogoletsa Chigori Choyamba ( First Goalscorer )

Msika uwu umakupemphani kuti muloseleretu wosewera amene adzapeze chigoli choyamba pa masewero.


Masewero ngati atha 0-0 (palibe chigoli), mabeti onse amakhala opanda ntchito (void). Chigawo cha ndime yachipulula sikuwerengeredwa.(Extra Time)


Ngati wosewerayo sanayambe kusewera kapena walowa gulu lake litagoletsa kale chigoli, beti limenelo limakhala void..

Ngati wosewerayo wasinthidwa kapena watulutsidwa asanagoletse chigoli choyamba, beti limenelo limakhala losaloledwa. Ikakhala beti ya masewero amodzi sitaki imabwezedwa pamene beti ya masewero ambiri imapitilira koma guli limeneri limachosedwa pa tiketi yanu.

Chonde dziwani Ma own goals (chigoli chozidzigoletsa okha) sichimalembedwa pa msika uwu.


Ogoletsa chigori panthawi ina iliyonse (Anytime Goalscorer)

Msika uwu mumalosere wosewera amene adzagoletse chigoli nthawi iliyonse pa masewero.

Ngati masewerowo atha 0-0 (palibe chigoli), mabeti onse amakhala opanda ntchito (void). Chigawo cha ndime yachipulula sikuwerengeredwa.(Extra Time)


Ngati wosewerayo wasinthidwa kapena watulutsidwa asanagoletse chigoli, beti limenelo limakhala losapambana.


Ma own goals (chigoli chodzigoletsa okha) sizimaloledwa.


Ogoletsa chigori Chomaliza ( Last Goalscorer )

Msika uwu mumalosere wosewera amene adzagoletse chigoli chomaliza pa masewero.

Masewero ngati atha 0-0 (palibe chigoli), mabeti onse amakhala osawerengedwa. Chigawo cha ndime yachipulula sikuwerengeredwa.(Extra Time)


Ngati wosewerayo sanasewere masewerowo, siteki pa ku betcha kwa masewero amodzi imabwezedwa pamene ku betcha kwa masewelo ambiri kumapitilira koma gulu lobetcheleredwa limachotsedwapo.

Wosewerayo ngati wasinthidwa kapena watulutsidwa asanagoletse chigoli chomaliza chisana goletsedwe, ku betcha kwake sikunapambane..


Ma own goals (zogoli zozigoletsa okha) sizimawerengeredwa pa msika uwu.


Ogoletsa zigori ziwiri ( Brace Goalscorer )

Msika uwu mumalosere wosewera amene adzagoletse zigoli ziwiri (2) kapena kuposera apa pa masewero. Masewero ngati atha 0-0 (palibe chigoli), mabeti onse amakhala osawerengedwa (voided). Chigawo cha ndime yachipulula sikuwerengeredwa(Extra Time) komanso, wosewerayo ngati watuluka asanagoletse zigoli ziwiri kapena kuposerapo, Ku betcha paiye ndekuti nkosapambana. Wosewera ngati sanatengepo mbali pamasewero, ku mubetchera pa msika uwu kumakhala kosaloledwa(void).


Ogoletsa zigori zitatu ( Hat-trick Goalscorer )

Msika uwu mumalosere wosewera amene adzagoletse zigoli zitatu(3) kapena kuposera apa pa masewero. Masewero ngati atha 0-0 (palibe chigoli), mabeti onse amakhala osawerengedwa (voided). Chigawo cha ndime yachipulula sikuwerengeredwa(Extra Time)

komanso, wosewerayo ngati watuluka asanagoletse zigoli zitatu kapena kuposerapo, Ku betcha paiye ndekuti nkosapambana.Wosewerayo ngati wasinthidwa kapena watulutsidwa asanagoletse chigoli chomaliza chisana goletsedwe, ku betcha kwake sikunapambane ngatinso wosewera sanatengepo mbali pamasewero, ku mubetchera pa msika uwu kumakhala kosaloledwa(void).


Chigawo chomwe chikhale zigori zochuluka (Half with more goals)

Msika uwu mumalosera kuti chigawo chiti chamasewero chidzakhale ndi zigoli zambiri.

Ngati mukuganiza kuti zidzakhala zofanana (zigoli zofanana mu chigawo chilichonse), mutha kubetcha pa "Equal".

Msika uwu umapezekanso pa nthawi zonse (Full Time) komanso pa gulu lililonse.


Zosankha (Selections):

First Half (chigawo choyamba) – Zigoli zambiri zidzapezeka muchigawo choyamba kuposa chigawo chachiwiri.

Second Half (chigaowo chachiwiri goli zambiri zidzapezeka mu chigawo l chachiwiri kuposa choyamba

Equal (Zofanana) – Zigoli zidzakhala zofanana mu tchigawo choyamba ndi chachiwiri


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati chigawo choyamba chatha 0-0 ndipo masewerowo atha 1-2, ndiye kuti zogoli zonse zitatu zidachitika mu chigawo chachiwiri, kotero kusankha kopambana ndi “Second Half.”



Timu yapakhomo iwina zigawo zonse (HOME win both halves)

Msika uwu mumalosera ngati timu yapakhomo (Home team) idzawine magawo onse awiri a mphindi 45 (chigawo choyamba ndi chigawo chachiŵiri).


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu yapakhomo idzawina pa chigawo choyamba ndiponso pa chigawo chachiwiri

No (Ayi) – Timu yapakhomo sidzawina magawo onse awiri a masewero.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

HT (chigawo choyamba): 1-0

FT (Nthawi yathunthu): 1-0

Kusankha kopambana ndi No, chifukwa Real Madrid sinawine chigawo chachiŵiri (0-0 mu chigawo chachiŵiri).


Timu yoyenda (away) iwina zigawo zonse (AWAY win both halves)

Msika uwu mumalosera ngati timu ya alendo (Away team) idzawina magawo onse awiri a mphindi 45 (chigawo choyamba ndi chigawo chachiŵiri).


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu ya alendo idzawina pa chigawo choyamba ndiponso pa chigawo chachiŵiri.

No (Ayi) – Timu ya alendo sidzawina magawo onse awiri a masewero.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

HT (chigawo choyamba): 1-2

FT (Nthawi Yathunthu): 1-3

Kusankha kopambana ndi Yes, chifukwa Barcelona idaposa Real Madrid mu theka lililonse — adawina 1-2 mu loyamba ndi 0-1 mu lachiŵiri, choncho adawina magawo onse awiri.


Timu yapakhomo iwina chigawo chinachake (HOME win either half)

Msika uwu mumalosera ngati timu yapakhomo (Home team) idzagoletse zigoli zambiri kuposa gulu la alendo pa chigawo chimodzi (kapena pa magawo onse awiri).


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu yapakhomo idzawina chigawo choyamba, chigawo chachiŵiri, kapena onse awiri.

No (Ayi) – Timu yapakhomo sidzawina chigawo chiilichonse cha masewero.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

HT (chigawo choyamba): 1-1

FT (Nthawi yathunthu): 2-2

Kusankha kopambana ndi No, chifukwa matimu onse adapeza chigoli chimodzi pa chigawo chilichonse, choncho Real Madrid sinali ndi chigawo chomwe yawina.


Timu yoyenda (away) iwina chigawo chinachake (AWAY win either half)

Msika uwu mumalosera ngati timu ya alendo (Away team) idzapeze zigoli zambiri kuposa timu yapakhomo pa chigawo (kapena pa magawo onse awiri).


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu ya alendo idzawina chigawo choyamba, chigawo chachiŵiri, kapena onse awiri.

No (Ayi) – Timu ya alendo sidzawina chigawo chili chonse cha masewero.


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

HT (chigawo Loyamba): 1-1

FT (Nthawi yathunthu): 2-3

Kusankha kopambana ndi Yes, chifukwa Barcelona idawina chigawo chachiŵiri pogoletsa zigoli ziwiri pamene Real Madrid idagoletsa chigoli chimodzi chokha.


Timu yapakhomo igoletsa mzigawo zonse (HOME score in both halves)

Msika uwu mumalosera ngati timu yapakhomo (Home team) idzapeze chigoli pa chigawo choyamba ndi chigawo chachiŵiri cha masewero.


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu yapakhomo idzapeza chigoli pa chigawo choyamba komanso chachiŵiri.

No (Ayi) – Timu yapakhomo sichidzapeza zigoli pa magawo onse awiri (mwina pa chigawo chimodzi chokha kapena ayi).


Timu yoyenda (away) igoletsa mzigawo zonse (AWAY score in both halves)

Msika uwu mumalosera ngati timu ya alendo (Away team) idzapeze chigoli pa chigawo choyamba ndi chachiŵiri pa masewerowo.


Zosankha (Selections):

Yes (Inde) – Timu ya alendo idzapeza chigoli pa chigawo choyamba komanso chachiŵiri.

No (Ayi) – Timu ya alendo sichidzapeza zigoli pa magawo onse awiri (mwina pa chigawo chimodzi chokha kapena ayi).


Timu yapakhomo iwina koma timu inayo sigoletsa-nthawi yonse yamasewero (HOME team win to nil - Full Time)

Loselani ngati timu yapakhomo (Home Team) ingapambane masewerawo osagoletsedwa chigoli. Msikawu umapezeka nthawi yonse yamasewero (Full Time) komanso theka loyamba (1st half).


Zosankha (selections):

Inde (Yes) - Timu yapakhomo (Home Team) ipambana masewerawa ndipo siigoletsedwa chigoli (imasunga clean sheet)

Ayi (No) - Timu yapakhomo siipambana kapena ipambana masewerawo koma igoletsedwa chigoli


Chitsanzo (Example):

Real Madrid - Barcelona

Zotsatira zomaliza: 1-0.

Kulosera kopambana kudzakhala Inde (Yes), chifukwa Real Madrid adapambana masewerowo ndipo siinalole kuti igoletsedwe chigoli. (sanavomereze cholinga).


Timu yobwera iwina koma timu inayo sigoletsa-nthawi yonse yamasewero (AWAY team win to nil )- Full Time

Loselani ngati timu yobwera (Away Team) ingapambane masewerawo osagoletsedwa chigoli. Msikawu umapezeka nthawi yonse yamasewero (Full Time) komanso theka loyamba (1st half).


Zosankha (selections):

Inde (Yes) - Timu yobwera (Away Team) ipambana masewerawa ndipo siigoletsedwa chigoli (imasunga clean sheet)

Ayi (No) - Timu yobwera siipambana kapena ipambana masewerawo koma igoletsedwa chigoli


Chitsanzo (Example):

Real Madrid - Barcelona

Zotsatira zomaliza 1-2. Kusankha kopambana kungakhale Ayi (No) chifukwa ngakhale Barcelona idapambana masewerowa, siidakwanitse kuteteza golo lawo"]


Chiwerengero chama Kona - Nthawi yonse yamasewero (Corner Count 1X2) - Full Time

Loserani kuti ndi timu iti imene itapedze ma corner ambiri pakutha kwa masewero.


Zosankha (Selections):

1 - Timu yapakhomo idzapeza ma corner ambiri

X - Timu zonse ziwiri zidzapeza ma corner ofanana

2 - Timu yobwera idzapeza ma corner ambiri


Msika uwu ukuperekedwanso pa gawo loyamba la masewero (1st Half).


Kona yoyamba (First Corner)

Loserani kuti ndi timu iti imene itatasewere corner yoyamba. Msika uwu umapezeka wa kutha kwa masero (FT) komanso kutha kwa gawo loyamba (1H). Chonde dziwani kuti ma corner operekedwa koma osaseweredwa, sangawerengedwe pa malipiro.


Zosankha (Selections):

1 - Timu yapakhomo (Home Team)

2 - Timu yobwera (Away Team)

Palibe Corner (No Corner) - Sipaseweredwa ma corner


Kona Yomaliza (Last Corner)

Loserani kuti ndi timu iti imene itasewere corner yomaliza. Msikawu umapezeka wa kutha kwa masewero (FT) komanso kutha kwa chigawo choyamba (1H). Chonde dziwani kuti ma corner operekedwa koma osaseweredwa, sangawerengedwe pa malipiro.


Zosankha (Selections):

1 - Timu yapakhomo (Home Team)

2 - Timu yobwera (Away Team)

Palibe Corner (No corner) - Sipaseweredwa ma corner


Msikawu umapezekanso pa kulosera kutha kwa chigawo choyamba (1st Half).


Nambala Yama Kona ngati angagawidwe ndi 2 osasala kanthu kapena ayi - Nthawi yonse yamasewero (Corner Count Odd/Even) - Full Time

Loserani ngati patapezeke nambala ya ma corner amene angagawidwe ndi 2 opanda chotsalira (even) kapena papezeka chotsalira (odd) panthawi yamasewerowa. Chonde dziwani kuti 0 (zero) imatengedwa ngati nambala imene ingagawidwe ndi 2 opanda chotsalira (even), kotero ngati palibe corner zomwe zidatengedwa, kusankha kolondola ndi "even".


Zosankha (Selections):

Odd - Padzakhala nambala yama corner imene ikagawidwa ndi 2 padzakhala chotsalira. (Mwachitsanzo 1, 3, 7, 9, 11 ndi manambala ena).

Even - Padzakhala nambala yama corner imene ikagawidwa ndi 2 sipakhala chotsalira. (Mwachitsanzo 2, 4, 6, 8, 10 ndi manambala ena).


Msikawu umapezekanso kwa chigawo choyamba chamasewero (1st Half).



Chiwerengero chama Kona kupitilira/Kuchepera - Nthawi yonse yamasewero (Total Corners Over/Under) - Full Time

Loserani kuti padzakhala ma corner angati panthawi yamasewero. Chonde dziwani kuti ma corner operekedwa koma omwe sanaseweredwe, sazawerengedwa pakuweruza zotsatira.


Zosankha (Selections):

Kupitilira (Over) x.5 - Padzakhala ma corner ambiri kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa

Kuchepera (Under) x.5 - Padzakhala ma corner ochepa kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa


Chiwerengero chama Kona kupitilira/Kuchepera - Muchigawo choyamba chamasewero (Total Corners Over/Under) - First Half

Loserani kuti padzakhala ma corner angati mu chigawo choyamba cha masewero. Chonde dziwani kuti ma corner operekedwa koma omwe sanaseweredwe, sazawerengedwa pakuweruza zotsatira.


Zosankha (Selections):

Kupitilira (Over) x.5 - Padzakhala ma corner ambiri kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa

Kuchepera (Under) x.5 - Padzakhala ma corner ochepa kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa


Chiwerengero chama Kona onse - Nthawi yonse yamasewero (Total Corners) - Full Time

Loserani kuchuluka kwa ma corner omwe adzapezeke pamasewero. Chonde dziwani kuti ma corner operekedwa koma omwe sanaseweredwe, sazawerengedwa pakuweruza zotsatira.


Zosankha (Selections):

Ma corner 0-8 - Padzakhala ma corner ziro mpaka asanu ndi atatu pamasewero.

Ma corner 9-11 - Padzakhala ma corner asanu ndi anayi mpaka khumi ndi chimodzi pamasewerowa.

Ma corner 12+ - Padzakhala ma corner osachepera 12 kapena kupitilira apo pamasewerowa.


Msikawu umapezekanso kwa chigawo choyamba chamasewero (1st Half).


Chiwerengero chama Kona tikawelengerapo Handicap - Nthawi yonse yamasewero (Corners 2-Way Handicap) - Full Time

2-way Corner handicap ndi msika womwe mungathe kulosera kuti ndi timu iti imene idzapambane masewero tikawerenga chiwerengero chomaliza cha ma corner kumapeto kwa masewerowa tikawerengerapo Handicap. Nthawi yowonjezera siizawerengedwa (Extra Time).


Chitsanzo (Example)

1 1.56 Barcelona ndi -0.5

2 2.65 Real Madrid ndi +0.5


Tiyerekeze kuti masewerowa atha 5-5 pachiwerengero chama corner. Ngati munasankha Real Madrid pa (@) 2.65 ndiye kuti +0.5 (kuphatikiza theka la corner) idzawonjezeredwa pamakona a Real Madrid ndipo kulosera kwanu ndikopambana.


Msika wa Corners 2-Way Handicap uliponso kwa chigawo choyamba chamasewero (1st Half).


Timu Imene Idzalandire ma makhadi achikasu/Ofira ambiri - Nthawi yonse yamasewero (Team with most Bookings) - Full Time

Loserani kuti ndi timu iti imene idzalandire ma khadi achikasu olo Ofira (yellow/red cards) (bookings) ambiri pamasewero.


Zosankha (Selections):

1 – Timu yapakhomo (Home)

X – Zofanana (Timu zonse ziwiri zilandira ma khadi yellow/red ofanana)

2 – Timu yobwera (Away)


Chitsanzo (Example):

Real Madrid - Barcelona

Ngati ma bookings pa mapeto a masewero (FT) ndi 3–3, ndiye kuti X ndi kusankha kopambana, chifukwa timuzo zili ndi ma yellow/red card ofanana.


Kuchuluka/Kuchepera kwa ma khidi achikasu/Ofira (bookings) - Nthawi yonse yamasewero (Total Bookings Over/Under) - Full Time

Loserani kuchuluka kwa kwama khadi a yellow/red (yellow/red card) pakutha kwa masewerawo. Khadi lachikasu (yellow card) limawerengedwa ngati 1 booking ndipo khadi lofiira (red card) kapena achikasu awiri (2 yellow cards) ngati 2 bookings. Khadi lachikasu lachiwiri (second yellow card) kwa wosewera m'modzi limene liimatsogolera ku khadi lofiira (red card) silimawerengeredwa. Zotsatira zake, wosewera m'modzi sangathe kukhala ndima bookings opitilira atatu. Khadi lofiira (red card) loperekedwa pakamodzi imawerengedwa ngati 2 bookings. Chonde dziwani kuti ma booking amene adzapelekedwe kwa omwe si osewera (osewera omwe adalowetsedwa kale, mamanejala, osewera amene sadalowetsedwe) sikuganiziridwa.


Khadi la chikasu (yellow card) = 1 booking


Khadi lofiira lopelekedwa pakamodzi (straight red card) = 2 bookings


Khadi lachiwiri la Yellow lomwe limatsogolera ku khadi lofiira (Red card) limawerengedwa ngati 2 bookings, osati 3.


Zosankha (Selections):

Kupitilira (Over) x.5 - Padzakhala ma booking ochulukirapo kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa

Kuchepera (Under) x.5 - Padzakhala ma booking ochepa kuposa omwe ali pa mzere waperekedwa


Msikawu uliponso kwa chigawo choyamba chamasewero (1st Half).


Chiwerengero chama khadi achikasu/Ofira - Nthawi yonse yamasewero (Total Bookings) - Full Time

Loserani kuchuluka kwenikweni kwa ma booking pakutha kwa pamasewero.


Khadi lachikasu (yellow card) = 1 booking

Khadi lofiira lomwe laperekedwa pakamodzi (straight red card) = ma booking awiri (2)

Khadi lachikasu lachachiwiri (second yellow card) lomwe limatsogolera ku khadi lofiira (red card) limawerengedwa ngati ma booking awiri (2), osati atatu (3).


Chifukwa chakuti, wosewera m'modzi sangathe kulandira ma booking oposa atatu (3).


Msika uwu ukuperekedwanso pa kutha kwa chigawo choyamba (1st Half).

Khadi lachikasu/lofira loyamba - Nthawi yonse yamasewero (First Booking) - Full Time

Loserani kuti ndi timu iti imene italandire booking yoyamba pa masewero (khadi lachikasu “yellow card” kapena khadi lofiira “red card”).


1X2 komanso ma timu awiri onse agoletsa - Nthawi yonse yamasewero (1X2 and Both Teams To Score) - Full Time

Loserani zotsatira za masewero komanso ngati ma timu awiri onse adzapeze chigoli (osachepera) limodzi.


Zosankha (Selections) :

1-Yes (Inde) – Timu yapakhomo ipambana komanso matimu awiri onse apeza chigoli

2-Yes (Inde) – Timu yobwera ipambana komanso matimu awiri onse apeza chigoli

X-Yes (Inde) – Matiwa afanana mphamvu (draw) komanso matimu awiri onse apeza chigoli

X-No (Ayi) – Matiwa afanana mphamvu (draw) komanso matimu awiri onse sakwanitsa kupeza chigoli

1-No (Ayi) – Timu yapakhomo ipambana koma timu imodzi yokha ndiyomwe itapeze chigoli

2-No (Ayi) – Timu yobwera ipambana koma timu imodzi yokha ndiyomwe itapeze chigoli



Chitsanzo (Example):

Real Madrid - Barcelona

Zotsatira zomaliza (Full Time): 1-2

Zosankha zopambana (winning selection) ndi: 2-Yes, chifukwa Barcelona idapambana ndipo matimu awiri onse adapeza chigoli.


Penate iperekedwa (Penalty Awarded)

Loserani ngati pataperekedwe penate (penalty) kapena ayi pamasewero.

Kulosera kwanu kumawerengedwa pazochitika za mkati mwa nthawi yokhazikika ya masewero.

Izi zikuphatikiza nthawi monga yovulala/yoyimitsidwa yowonjezeredwa ndi woyang'anira masewero kumapeto kwa nthawi yokhazikika.

Nthawi yowonjezera siiwerengedwa pokhapokha itanenedwa mwanjira ina.

Ngati palibe penate (penalty) yoperekedwa, kusankha kopambana pamsika uno kudzakhala ayi (No).


Zosankha (Selections):

Inde (Yes) - Padzakhala penate (Penalty) yoperekedwa pantha yokhazikika yamasewero.

Ayi (No) - Sipadzakhala penate (Penalty) yoperekedwa pantha yokhazikika yamasewero.


Osewera adzachotsedwa pamasewero - Nthawi yonse yamasewero (Player Sent Off) - Full Time

Loserani ngati padzakhala khadi lofiira (red card) lomwe lidzaperekedwe pa masewero.


Khadi lomwe laperekedwa pa nthawi yopuma (HT) kapena pambuyo pa masewero silidzawerengedwa. Komanso, makhadi operekedwa kwa osewera omwe ali pa benchi sadzawerengedwa.


Zosankha (Selections):

Inde (Yes) – Wosewera adzachotsedwa pa masewero panthawi yokhadzikika ya masewero.

Ayi (No) – Palibe wosewera amene adzachotsedwe pa masewero panthawi yokhadzikika ya masewero.


Msika uwu umapezekanso pawokha kwa timu yapakhomo (Home Team) ndi timu yobwera (Away Team).


Timu Idzapitira ku ndime Ina (To Qualify)

Loserani kuti ndi timu iti yomwe idzapite ku gawo lotsatira la mpikisano.

Kumbukirani kuti ngati masewerowo ali omaliza (monga Final ya World Cup), msika uwu umayimira msika wa timu yomwe idzapambane chikho.


Opambana zotsatira zama penate (Penalty Shootout Winner)

Loserani kuti ndi timu iti yomwe idzapambane pa zotsatira za mapenate (Penalty Shootout).

Msika wa zotsatira za mapenate (pernalty shootout) umachitika ngati zotsatira zikadali zofanana ngakhale mutasewera mphindi 30 za nthawi yowonjezera (Extra Time).


1X2 Nthawi Yowonjezera (1X2 Extra Time)

Loserani kuti ndi timu iti yomwe idzapambane pa nthawi yowonjezera (Extra Time).

Zotsatira za mapetane (Penalty Shootout) sizidzawerengedwa pa kuweruza zotsatira zomaliza.


1X2 Nthawi Yowonjezera Chigawo Choyamba (1X2 Extra Time 1H)

Loserani kuti ndi timu iti yomwe idzapambane chigawo choyamba mu nthawi yowonjezera (mphindi 15 zoyambirira kuphatikiza nthawi yowonjezeredwa).


Kuchuluka/Kuchepera kwa zigoli - Mu Nthawi Yowonjezera (Total Score Over/Under) - Extra Time

Loserani ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa kuposa zimene zili pa mzere womwe waperekedwa pa nthawi yowonjezera (Extra Time).

Zotsatira za mapenate (Penalty Shootout) sizidzawerengedwa pa kuweruza zotsatira zomaliza.


Kuchuluka/Kuchepera kwa zigoli mu Nthawi Yowonjezera - Mu Chigawo Choyamba (Total Score Over/Under) - (Extra Time) - 1H

Loserani ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa kuposa zimene zili pa mzere womwe waperekedwa mu chigawo choyamba cha nthawi yowonjezera “Exra Time” (mphindi 15 zoyambirira zamu nthawi yowonjezeredwa “Extra Time”).


Chitsankho choyimira zotsatira ziwiri - Mu Nthawi Yowonjezera (Double Chance) - Extra Time

Msika umene chisankho chimodzi chimakulorani kulosera zotsatira ziwiri, zomwe zimapangitsa kuti pakhale malipiro ochepa kuposa msika wamba wa 1X2.

Loserani chimodzi mwa zotsatira ziwiri zimene zili pa Double Chance pa nthawi yowonjezera (Extra Time).


Chitsankho choyimira zotsatira ziwiri - Mu Nthawi Yowonjezera - Mu Chigawo Choyamba (Double Chance) - (Extra Time) - 1H

Msika umene chisankho chimodzi chimakulorani kulosera zotsatira ziwiri, zomwe zimapangitsa kuti pakhale malipiro ochepa kuposa msika wamba wa 1X2.

Loserani chimodzi mwa zotsatira ziwiri zapawiri (Double Chance) pa chigawo choyamba cha nthawi yowonjezera (mphindi 15 zoyambirira kuphatikiza nthawi yowonjezeredwa ngati ilipo).


Chitsankho choyimira zotsatira ziwiri komanso ma timu awiri onse agoletsa - Nthawi yonse yamasewero (Double Chance and Both Teams To Score) - FT

Loserani zotsatira ziwiri mwa zitatu zomwe zingachitike pa zotsatira zomaliza za masewerawo, komanso ngati matimu onse awiri atakwanitse kupeza chigoli kapena ayi.


Msika uwu umapezekanso pa chigawo choyamba (1st Half) ndi chigawo chachiwiri (2nd Half).


Chitsankho Choyimira Zotsatira Ziwiri Komanso ma Timu Awiri Onse Agoletsa mu Chigawo Choyamba (Double Chance and 1st Half Both Teams To Score)

Loserani zotsatira ziwiri mwa zitatu zomwe zingachitike pa gawo loyamba la masewerawo, komanso ngati matimu onse awiri atakwanitse kupeza chigoli kapena ayi mu chigawo choyamba.


Chitsankho Choyimira Zotsatira Ziwiri Komanso Ma Timu Awiri Onse Agoletsa Mu Chigawo Chawiri (Double Chance and 2nd Half Both Teams To Score)

Loserani zotsatira ziwiri mwa zitatu zomwe zingachitike mu chigawo chachiwiri cha masewerawo, komanso ngati matimu onse awiri atakwanitse kupeza chigoli kapena ayi mu chigawo chachiwirichi.


Chitsankho Choyimira Zotsatira Ziwiri Komanso Kuchuluka/Kuchepera kwa Zigoli - Nthawi yonse yamasewero (Double Chance and Over/Under) - Full Time

Loserani zotsatira ziwiri mwa zitatu zomwe zingachitike pa nthawi yoyikika (regular time) ya masewerawo, komanso ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa kuposa zimene zili pa mzere womwe waperekedwa.


Kuchuluka/Kuchepera kwa Zigoli Komanso Ma Timu Awiri Onse Agoletsa - Nthawi yonse Yamasewero (Over/Under and Both Teams To Score) - Full Time

Loserani ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa kuposa zimene zili pa mzere womwe waperekedwa, komanso ngati matimu awiri onse adzakwanitsa kupeza chigoli kapena ayi mu nthawi yoyikika yamasewero (regular time).


Zotsatira zingapo zamasewero - Nthawi yonse yamasewero (Multiscores) - Full Time

Loserani chisankho chomwe chili ndi zotsatira zowona za masewerawo pa nthawi yokhazikika ya masewerowa (regular time).


Sankhani pakati pa zigoli zamitundu yosiyanasiyana ya zotsatira zomaliza zamasewero zomwe zikuphatikizidwa mu chisankho chimodzi.


Zitsanzo (example):

“1:0, 2:0 kapena 3:0” — ngati mwasankha izi ndipo zotsatira zomaliza ndi 1:0, 2:0 kapena 3:0, mwayi wanu wadutsa.

“Other Home Win / Other Away Win” — msika uwu umatanthauza kupambana kwa timu ya payakhomo kapena timu yobwera ndi zotsatira zilizonse zomwe sizinatchulidwe m’mizere yomwe yalembedwa.


Chiwero cha zigoli - Mu Nthawi Yonse Yamasewero (Multigoals) - Full Time

Loserani kuchuluka kwa zigoli zomwe zidzalowe pa nthawi yoyikika yamasewero (regular time).


Zosankha (selections):

1–2 Zigoli (Goals) – Padzakhala zigoli kuchokera pa chimodzi kufika pa ziwiri pa nthawi yokhazikika ya masewero.

1–3 Zigoli (Goals)– Padzakhala zigoli kuchokera pa chimodzi kufika pa zitatu pa nthawi yokhazikika ya masewero.

7+ Zigoli (Goals) – Padzakhala zigoli zisanu ndi ziwiri kapena kuposerapo pa nthawi yokhazikika ya masewero.

Palibe chigoli (No Goal) – Sipadzakhala chigoli chilichonse pa nthawi yokhazikika yamaswero.


Msika uwu umapezekanso pa chigawo choyamba (1st Half) ndi chigawo chachiwiri (2nd Half).

Timu Yapakhomo Ipambana kapena Timu iliyonse mwa awiriwa siigoletsedwa chigoli - Nthawi Yonse Yamasewero (Home or Any Clean Sheet) - Full Time

Loserani ngati timu yapakhomo ipambana kapena ngati timu iliyonse mwa awiriwa siigoretsedwa chigoli.


Zosankha (Selections):

'Inde' (Yes) - Timu yapakhomo ipambana kapena timu iliyonse siigoretsedwa chigoli.

'Ayi' (No) - Timu yapakhomo sidzapambana ndipo matimu onse azigoletsa zigoli munthawi yake.


Kufanana Mphamvu kapena Timu iliyonse mwa awiriwa siigoletsedwa - Nthawi Yonse Yamasewero (Draw or Any Clean Sheet) - Full Time

Loserani ngati masewerawo atathe mofanana mphamvu kapena ngati timu iliyonse siigoretsedwa chigoli.


Zosankha:

'Inde' (Yes) - Masewero atha ndi kufanana mphamvu kapena timu iliyonse siigoretsedwa chigoli.

'Ayi' (No) - Masewero siatha mofanana mphamvu ndipo matimu onse azigoletsa chigoli munthawi yake.


Timu Yobwera Kapena Timu iliyonse mwa awiriwa siigoletsedwa chigoli (Away or Any Clean Sheet) - Full Time

Loserani ngati timu yobwera ipambana kapena ngati timu iliyonse siigoretsedwa chigoli.


Zosankha:

'Inde' (Yes) - Timu yobwera ipambana kapena timu iliyonse siigoretsedwa chigoli.

'Ayi' (No) - Timu yobwera sidzapambana ndipo matimu onse azigoletsa zigoli munthawi yake.


Kuchuluka/Kuchepera kwa zigoli mu Zigawo zonse Ziwiri (Both Halves Over/Under)

Loserani ngati chiwerengero cha zigoli zomwe zidzalowe m'magawo onse awiri a masewerawo chidzakhala chopitirira kapena chochepera zimene zili pa mzere womwe waperekedwa, kapena ayi.


Timu Yapakhomo kapena Kuchepera/Kuchepera kwa zigoli - Nthawi yonse yamasewero (Home or Over/Under) - Full Time

Loserani ngati timu yapakhomo idzapambane kapena ngati chiwerengero cha zigoli pa nthawi yokhazikika yamasewero (regular time) chidzakhala chopitirira kapena chochepera zimene zili pa mzere womwe waperekedwa.


Mwayi uwu udzawerengedwa ngati wopambana ngati chimodzi mwa zotsatira ziwirizi zatsimikizika.


Kufanana Mphamvu kapena Kuchuluka/Kuchepera kwa zigoli - Nthawi Yonse Yamasewero (Draw or Over/Under) - Full Time

Loserani ngati masewerawo adzatha mofanana mphamvu (draw) kapena ngati chiwerengero cha zigoli pa nthawi yokhazikika ya masewero (regular time) chidzakhala chopitirira kapena chochepera zimene zili pa mzere womwe waperekedwa.


Mwayi uwu udzawerengedwa ngati wopambana ngati chimodzi mwa zotsatira ziwirizi zatsimikizika.


Chiwelengelo Cha zigoli ndikupambana kwa Timu yobwela (Away or Over/Under - Full Time)

Loserani ngati timu yobwera idzapambane kapena ngati chiwerengero cha zigoli pa nthawi yokhazikika yamasewero (regular time) chidzakhala chopitirira kapena chochepera zimene zili pa mzere womwe waperekedwa.


Mwayi uwu udzawerengedwa ngati wopambana ngati chimodzi mwa zotsatira ziwirizi zatsimikizika.


Opambana Mu Mphindi 15 (1X2 - Interval 15 minutes)

Loserani zotsatira za masewero za msika wa 1X2 potengera nthawi ya mphindi 15 za masewero. Zigoli zomwe zidzalowe mkati mwa nthawi imeneyo zokha ndi zomwe zidzawerengedwe.


Chitsanzo (Example): Pakati pa mphindi 1 mpaka 15 (00:01–14:59), kapena pakati pa mphindi 16 mpaka 30 (15:00–29:59), ndi zina zotero.


Opambana Mumphindi 10 (1X2 - Interval 10 minutes)

Loserani zotsatira za masewero za msika wa 1X2 potengera nthawi ya mphindi 10 za masewero. Zigoli zomwe zidzalowe mkati mwa nthawi imeneyo zokha ndi zomwe zidzawerengedwe.


Chitsanzo: Pakati pa mphindi 1 mpaka 10 (00:01–09:59), kapena pakati pa mphindi 11 mpaka 20 (10:00–19:59), ndi zina zotero.


Chiwelengelo cha Zigoli Mumphindi 15 (Over/Under - Interval 15 minutes)

Loserani ngati chiwerengero cha zigoli zomwe zidzalowe mkati mwa nthawi ya mphindi 15 chidzakhala chopitirira kapena chochepera zimene zili pa mzere womwe waperekedwa. Zigoli zomwe zidzalowe mkati mwa nthawi yosankhidwayo zokha ndi zomwe zidzawerengedwe.


Chitsanzo: Ngati musankha Over 0.5 (00:01–14:59) ndipo goli limodzi lalowa pa mphindi ya 8, chisankho chanu chapambana.


Ngati palibe chigoli chomwe chalowa mkati mwa nthawi imeneyo, chisankhocho chagonja.


Njira Yopambanila (Winning Method)

Loserani kuti ndi timu iti yomwe idzapambane komanso njira yomwe idzapambanire. Msika uwu umapezekanso pa kutsimikizira ndime ya mpikisano (deciding leg of a tie) wokha, ndipo wopambana adzadziwika potengera zotsatira zonse za mpikisanowo wonse (entire tie).


Kupambana Kwambili (Winning Margin)

Loserani kuchuluka kwa zigoli zomwe timu yopambana idzawonjezere kuti ipambane masewerawo. Mwachitsanzo 3-1 ndie kuti timu yapambana ndi zigoli ziwiri.


Mtundu wa kubeta kwa basketball ndi malamulo otsatila (Basketball bet type and resulting rules)

Kutalika kwa masewelawa (Match length)

Masewela a Basketball amakhala ndimakota 4, ndipo kota lililonse limatenga mphindi 10. Nthawi yonse tikaphatikiza imakhala mphindi 40. Komabe, pali zosiyana kutengera mpikisano kapena mulingo wa masewero -

NBA - 4 x 12 minutes

NCAA - 2 x 20 minutes

CBA (Chinese Basketball League) - 4 x 12 minutes

PBA (Philippine Basketball League) - 4 x 12 minutes

Masewela oti asiyidwa panjira / Masewela oti asintha nthawi yoyambila (Abandoned / Postponed Matches)

Masewela oti aimitsidwa panjira kapena asintha nthawi yoyambila samawelengedwa pokhapokha ngati ayambilanso ndipo aseweredwa mkati mwa maola 24 kuchokera nthawi yomwe anayenera kuyamba.

Ngati nthawi yoyambila masewela asinthidwa kufikila ndendende maola 24 kuchokolela panthawi imene masewelawo amayenela kuyamba, ndiye kuti beti imeneyo izawelengesedwa.


Kubeta kuti wapambana ndani - Mu nthawi yonse yoseweledwa kuphatikizapo nthawi yowonjezela (Moneyline - Full Time incl. Over Time)

Loselani timu yomwe ingapambane masewero. Chonde dziwani kuti msika uwu umaphatikizapo nthawi yowonjezera.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tiyelekeze kuti tinalosela kuti Utah Jazz ipambana masewero. Iwo apeza mapointi 120 kuposela Lakers omwe apeza 100. Beti yathu ndiyekuti yapambana.


Opambana mu theka loyamba (Moneyline - First Half)

Loselani kuti ndi timu iti idzatsogolera pa theka loyamba. Theka loyamba mu basketball ndi kota loyamba ndi lachiwiri (quarter 1 ndi quarter 2). Ngati zotsatira zili zofanana (draw) pambuyo pa theka loyamba, mabeti onse sadzawelengetsedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tinali ndi beti pa Utah Jazz kuti ipambane theka loyamba.

Tiyeni tiwone zotsatira za theka loyamba. Zinali 47 - 69 (Timaphatikiza mapointi a kota yoyambilila ndi kota yachiwili). Izi zikusonyeza kuta Utah Jazz inali ndi mapointi aambili itatha theka loyamba motelo beti yathu inachita bwino.


Kubeta kuti wapambana ndani - Mu Kota yoyamba (Moneyline - First Quarter)

Loselani kuti ndi timu iti imene ipambane mu kota yoyamba. Nkutheka zigoli zizakhala zofanana pakutha pa kota yoyamba ma bet onse sazawelengetsedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

LA Lakers inali ndi mapointi awili kuposela Utah Jazz mu kota yoyamba ndipo ngati munasankha kuti apambana mu kota yoyambayo ndiyekuti beti imeneyo mwapambana.


1X2 - Mu Theka loyamba ( 1X2 First Half)

Loselani kuti ndi timu iti idzatsogolera pa theka loyamba. Msika uwu uli ndi mwayi wobetanso kuti mapointi atha kukhala olingana (draw).


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Ngati munalosela pa beti kuti Utah jazz ipambana mu theka loyamba, Munapambana chifukwa iwo anali ndi mapointi 69 pamene Lakers inali ndi mapointi 47 ndipo anawina mu theka loyamba yamasewelowo.


1X2 Mu Kota yoyamba (1X2 First Quarter)

Loselani kuti ndi timu ipambane mu kota yoyamba. Msika umenewu ulinso ndikuthekela kosankha kuti mapointi akhala olingana (draw).


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

LA Lakers inali ndimaponti awili kuposa Utah Jazz mu kota yoyamba ndipo ngati munasankha kuti kuti a LA Lakers apambana mukota yoyamba ndiyekuti mwapambana pa beti imeneyo.


Msika umenewu umapezekanso pama kota ena


kubeta pa chiwerengero cha mapointi onse (a magulu onse awiri) pamapeto a masewera — kuphatikizapo nthawi yowonjezera (Over/Under - Full Time incl. Over Time)

Loselani ngati padzakhala mapointi ambiri kapena ochepa omwe adzapezeke pamasewera onse kuposa pamointi womwe aperekedwa. Msika uwu umaphatikizapo nthawi yowonjezera.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tiyeni tiyelekeze kuti tili ndi beti pa “ma pointi Under 225.5.”

Ngati titaphatikiza mapointi onse (100 + 120) timapeza 220.

Izi zikutanthauza kuti kubeta kwathu kwapambana, chifukwa tinaneneratu kuti padzakhala mapointi ochepera 225.5, ndipo zinali zoona.


kubeta pa chiwerengero cha mapointi onse omwe adzapezeke mu theka loyamba la masewera (Over/Under – First Half)

Loselani ngati padzakhala mapointi ambiri kapena ochepa omwe adzapezeke mu theka loyamba la masewerawo kuposa mapointi omwe apelekedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tabeta kuti tikhala ndima points oposela 110.5 patheka loyamba yamasewela. tikaphatikiza zotsatira za theka loyamba, tapeza 47 + 69 = 116, Izi zikutanthauza kuti kubeta kwathu kwapambana, chifukwa tinaneneratu kuti padzakhala mapointi oposa 110.5 mu theka loyamba, ndipo zakhala choncho.


kubeta pa chiwerengero cha mapointi onse omwe adzapezeke mu kota loyamba la masewera (Over/Under – First Quarter)

Loselani ngati padzakhala mapointi ambiri kapena ochepa omwe adzapezeke mu kota yoyamba ya masewerawo kuposa mapointi omwe apelekedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Beti inaikidwa kuti mapointi achepela 60.5 mu kota yoyamba. Tikaona mapointi a kota yoyamba 28+26=54. Zikutanthauza kuti beti yathu yapambana, chifukwa zomwe tinalosela zinali zochepela 60.5 zomwe zinagolesedwa mu kota yoyamba.


Msika umenewu umapezekanso pama kota ena.


kubeta pa chiwerengero cha mapointi onse a timu yapakhomo omwe adzapezeke mu kota yoyamba la masewera (Over/Under – 1Q Home Team)

Loselani ngati timu yapakhomo ikhale ndi mapointi ambiri kapena ochepa omwe adzapezeke mu kota yoyamba ya masewerawo kuposa mapointi omwe apelekedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tili ndi beti ya timu yapakhomo kuti ikhala ndimapointi oposela 25.5 mu kota yoyamba. Iwo agoletsa ndimapointi 28 zomwe zikutanthauza kuti beti imeneyi yapambana chifukwa timangofunikila mapointi 26 kuchokela kwaiwo.


kubeta pa chiwerengero cha mapointi onse a timu yobwela omwe adzapezeke mu kota yoyamba ya masewera (Over/Under – 1Q Away Team)

Loselani ngati timu yobwela ikhale ndi mapointi ambiri kapena ochepa omwe adzapezeke mu kota yoyamba ya masewerawo kuposa mapointi omwe apelekedwa.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Timu yobwela inali ndima pointi 26 mu kota yoyamba. Ngati munabeta kuti timu yobwela ikhala ndimapointi ochepela 26.5 mu kota yoyamba ndiye kuti mwapambana pa beti imeneyi.


Wopambana pa masewero ndi chiwerengero cha mapointi - nthawi yonse kuphatikiza nthawi yowonjezela.

Kulosela kuti ndi timu iti itapambane komanso mapointi onse omwe adagoletsa mu kusankha kumodzi.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Bet idayikidwa pa kusankha “2 – Under 225.5”, zomwe zikutanthauza kuti tinasankha kuti Utah Jazz ipambana masewelawo ndipo padzakhala mapointi osakwana 225.5. Titayang'ana zotsatira zomaliza, tikuwona kuti beti yathu inapambana, Utah Jazz idapambana masewerawo ndipo mapointi 220 okha ndi omwe adagoletsa.


2-Way Handicap - Full Time incl. Over Time

2-way handicap (omwe umadziwikanso kuti mapointi ogawa) ndi msika umene mumakwanitsa kubeta pa zotsatila zamasewela pamene timu imodzi imapatsidwa pointi yoyambila. Ma bet amawelengetsedwa tikaphatikizapo handicap.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Titabeta pa “1(+24.5)” zomwe zikutanthauza kuti, taipatsa LA Lakers mwayi wa mapointi 24.5. Titayang'ana zotsatira zomaliza, tikuwona kuti bet yathu yapambana, chifukwa ma points ataonjezeledwa LA Lakers ili ndi mapointic124.5 mosiyana ndi mapoint a Utah amene ali 120.


2-Way Handicap (Mugawo loyamba) 2-Way Handicap - First Half

Kulosela kuti ndi timu iti yomwe ipeza mapointi ambiri mu theka loyamba pamene taonjezela handicap.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Beti idayikidwa pa “2(-10.5)mutheka loyamba” zomwe zikutanthauza kuti timachotsa mapointi 10.5 kuchokera ku timu yobwela pama pointi amu theka loyamba. Chifukwa chake tifufuze mapointi amutheka loyamba - 47-69. Ngati tichotsa mapointi 10.5 kuchokera pa 69 tili ndi mapointi 58.5 omwe akadali apamwamba kuposa timu yobwela iwo ali ndi 47. Beti yathu yapambana.


Msikawu umapezekanso mu gawo lachiwili.


2-Way Handicap mukota yoyamba (2-Way Handicap - First Quarter)

Kulosela kuti ndi timu iti yomwe ipeza mapointi ambiri mu kota yoyamba pamene taonjezela handicap.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tili ndi kubetai pa “1(-1.5) mu kota yoyamba” zomwe zikutanthauza kuti tikuchotsa mapointi 1.5 ku timu yapakhomo mu kota yoyamba. Tikachotsa ma pointi amenewa, tili ndi zotsatira za kota yoyamba za 26.5-26. LA Lakers akadali ndi mapointi ambiri kuposa Utah Jazz, choncho beti yathu yapambana.


Odd/Even - Munthawi yonse yamasewelo kuphatikizapo nthawi yoonjezela. (Odd/Even - FT incl. OT)

Loselani ngati kuchuluka kwa mapointi onse omwe apeza pamasewerawa adzakhala oti nambala yake itha kugawika ndi 2 (Even) kapena ayi (Odd). Msika umenewu umaphatikizapo nthawi yowonjezera.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tili ndi beti pa “Even(nambala yogawika ndi 2) – Munthawi yonse yamasewelo kuphatikiza nthawi yowonjezera”. Tiyeni tiwone zotsatira zomaliza – 100-120. Pazonse pali mapointi 220, yomwe ndi nambala ya Even, choncho beti yathu yapambana.


Odd/Even - Mugawo loyamba (Odd/Even - First Half)

Loselani ngati kuchuluka kwa mapointi onse omwe apeke mu gawo loyamba pamasewerawa adzakhala Odd kapena Even.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tina beta kuti ikhala “Even – mugawo loyamba”. Tione maponti a gawo loyamba

– 47-69. Tikaphatikiza onse akukwana 116, Zomwe zikutanthauza kuti ndi nambala ya Even, beti yathu yapambana pamenepo.


Odd/Even - Kota yoyamba (Odd/Even - First Quarter)

Loselani ngati kuchuluka kwa mapointi onse omwe apeke mu kota yoyamba pamasewerawa adzakhala Odd kapena Even.


Chitsanzo (Example)

LA Lakers v Utah Jazz 100-120 (28-26; 19-43; 31-29; 22-22)

Tina beta kuti timu yapakhomo mukota yoyamba ikhala Even. Titaona mukota yoyamba maponti ali motele – 28-26. Tikaphatikiza zonse tili ndi mapointi 54, imene ili nambala ya Even. Beti yathu yachitabwino pamenepo.


Msika umenewu umapezekanso makota onse.


Mitundu ya Beti ya Tennis ndi Malamulo Otsatira (Tennis Bet Types & Resulting Rules)

Ngati masewelo a Tennis a sithidwa nthawi kapena aimitsidwa, mabeti onse okhudzana ndi masewerawo adzakhala ovomerezeka mpaka masewerawo ayambirenso ndi kumalizidwa.

Ngati wosewera wasiyira pakati, wachotsedwa kapena wachotsedwa chifukwa cha malamulo, mabeti onse okhudzana ndi masewerawo adzachotsedwa.


Tennis Tie Break

Pali mitundu iwiri ya Tiebreak yomwe imaseweredwa mu tennis – Tiebreak wamba (Regular Tiebreak) womwe umaseweredwa kuti adziwe wopambana wa set, ndi Super Tiebreak (omwe amadziwikanso kuti Match Tiebreak) womwe umaseweredwa kuti adziwe wopambana wa masewero onse.


Regular Tiebreak

Tiebreak ya set imaseweledwa ngati ma pointi apa set ali 6-6. Ndiye kuti osewela aliyense wapambana ma gemu six. Iwo amasewela tiebreak kufikila osewela modzi akhale ndi mapointi 7, koma ngati ma pointi afika pa 6-6, wosewera amene apambana mapointi awiri motsatizana ndiye wopambana wa setiyo.

Chonde dziwani kuti zimenezi zimagwiranso ntchito ngati zili 7-6 — kusiyana kwa mapointi awiri ndikofunikira kuti upambane! (Super tiebreak nayonso muyenera kukhala ndi kusiyana kwa mapointi awiri kuti upambane.)


Masewelo a Tennis a chiwonetselo (Tennis Exhibition matches)

Chonde dziwani kuti masewera ena a tennis achiwonetselo amakhala ndi maseweledwe osiyanasiyana. Masewera amenewa adzatsimikizidwa malinga ndi zotsatira zovomerezeka.


Super Tiebreak

M’masewera a doubles (Awa ndimasewela amene amaseweledwa anthu awili mu timu imodzi), nthawi zambiri pamakhala Super Tiebreak m'malo mwa seti yachitatu kuti masewerawo athamange mwachangu. Choncho, ngati zotsatira za seti zili 6-4; 3-6, adzasewera Super Tiebreak kuti adziwike wopambana. Mu tiebreak imeneyi, gulu lomwe layamba kufikila mapointi 10 ndiye limene limalengezedwa kuti lapambana masewerawo. Koma ngati ma pointi afika pa 10-10, gulu lopambana lidzakhala lomwe lipambane mapointi awiri motsatizana.

Pofuna kupambana mu tiebreak, pafunika kusiyana kwa mapointi awiri.

Pofuna kuwerengera masewera, betPawa imawerengera Super Tiebreak ngati masewera amodzi okha (1 game).

Choncho, ngati zotsatira zomaliza zili 6-4; 4-6; 10-8, kuchuluka kwa masewera onse kumakhala 21

(6 + 4 + 4 + 6 + 1 = ma gemu 21).


Moneyline - FT

Loselani kuti ndiosewela uti amene apambane masewelawa. Masewerawa ayenera kumalizidwa kwathunthu kuti beti yathu ikhale yovomerezeka.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Ngati zotsatira za seti ndi 4-6, 6-4, 3-6, wopambana wa masewerawo ndi Djokovic, chifukwa wapambana ma seti awili pomwe Nadal wapambana seti imodzi yokha. Chonde dziwani kuti wopambana wa masewerawo adzakhala wosewera amene apambana ma seti ambiri, osati wosewera amene apambana magemu ambiri.


Msika uwu umapezekanso pa ma seti ena.


Moneyline - First Set

Loselani wosewera amene angapambane seti yoyamba.

Seti yoyamba iyenera kumalizidwa kwathunthu kuti beti yathu ikhale yovomerezeka.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Ngati zotsatira za seti yoyamba ndi 6-2, wopambana wa setiyi ndi Nadal, chifukwa wapambana masewera 6 pomwe Djokovic wapambana 2 yokha. Chonde dziwani kuti wopambana wa seti ndi wosewera amene apambana masewera ambiri kuposa mnzake mu setiyo.



Moneyline - Second Set

Loselani wosewera amene angapambane seti yachiwili.

Seti iyenera kumalizidwa kwathunthu kuti beti yathu ikhale yovomerezeka.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Ngati zotsatira za seti yachiwiri zili 6-7, wopambana wa setiyo ndi Djokovic, chifukwa wapambana masewera 7 pomwe Nadal wapambana 6.


Chonde dziwani kuti wopambana wa seti ndi wosewera amene wapambana masewera ambiri kuposa mnzake mu setiyo.


Over/Under - Full Time

Loselanii ngati paseweledwe masewera ambiri kapena ochepa kuposa momwe zatsimikiziridwa.Super Tiebreak imawerengera ngati gemu imodzi yokha mu kuwerengera kwa masewera onse.


Chitsanzo (Example 1)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Zotsatira zomaliza: 6-4, 6-2. Chiwerengero chonse cha masewera: 6 + 4 + 6 + 2 = 18.


Chitsanzo (Example 2)

Mu masewera a doubles, Super Tiebreak imawerengeredwa ngati game imodzi yokha. Choncho, ngati zotsatira zomaliza ndi 6-4, 4-6, 10-5, chiwerengero chonse cha masewera chikhala:

6 + 4 + 4 + 6 + 1 = 21.


Msika uwu umapezekanso kwa ma seti ena.


Games Over/Under - Home - FT

Loselani ngati wosewera wa timu yapakhomo adzakhala ndi magemu ambiri kapena ochepa kuposa momwe atsimikiziridwa mu masewerawo onse.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Ngati zotsatila zomaliza zinali 6-3 7-5. Ngati munapanga beti yanu kuti timu yapakhomo ikhala ndima game oposela 12.5, ndiye kuti mwapambana chifukwa Nadal anali ndi game onse 13, zomwe zimaposa 12.5. Timu ya pakhomo (Home team player) ndi dzina loyamba lomwe lili pa m’ndandanda wa masewera (fixture name) nthawi zonse.


Games Over/Under - Away - FT

Loselani ngati wosewera wa timu yobwela adzakhala ndi magemu ambiri kapena ochepa kuposa momwe atsimikiziridwa mu masewerawo onse.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Mwapanga beti yanu kuti “timu yobwela – 8.5 masewera onse”. Zotsatira zomaliza zinali 6-4 7-6. Ngakhale wosewera wobwela sanachite bwino masewerawo, mwapambana beti yanu, chifukwa Djokovic adapambana masewera 10 onse.


2-Way handicap Games - FT

Loselani kuti ndi wosewera uti yemwe wapambana masewera ambiri atagwiritsa ntchito handicup.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Zotsatira zomaliza zinali 4-6 6-4 3-6. Nadal adapambana masewera 13 ndipo Djokovic adapambana masewera 16. Kotero Djokovic adapambana masewera a 3 kuposa mdani wake. Ngati kubeta kwanu kunali “1 (+3.5)” mwapambana, Zotsatira zomaliza zinali 4-6 6-4 3-6. Nadal adapambana masewera 13 ndipo Djokovic adapambana masewera 16. Kotero Djokovic adapambana masewera a 3 kuposa mdani wake. Ngati kubetcha kwanu kunali “1 (+3.5)” mwapambana, chifukwa mudapatsa Nadal masewera 3.5 pasadakhale ndipo tsopano wapambana masewera 16.5, omwe ndi 0.5 kuposa Djokovic.


Msika uwu umapezekanso kwa ma seti ena.


Correct Score - Full Time

Loselani zigoli zolondola zamasewerawo.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Zotsatira zomaliza zinali 4-6 7-6 6-4. Nadal adapambana ma seti 2 ndipo Djokovic 1 yekha. Chifukwa chake zimapanga zotsatira zomaliza 2-1.


Total Sets Exact - FT

Loselani kuti ndi ma seti angati omwe adzaseweredwe ndendende.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Nadal adapambana masewerawa 6-4 6-4. Adasewera ndendende ma seti 2, omwe angakhale chissankho chopambana.


Odd/Even Games - FT

Loselani ngati chiwelengelo chonse cha masewelawa chidzakhala Odd (Nambala yosagawika ndi 2) Kapena Even (Nambala yogawika ndi 2).


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Zotsatira zomaliza zamasewerawa zinali 4-6 6-4 4-6. Kuchuluka kwamasewera ndi 30, yomwe ndi nambala ya Even, kotero kusankha kopambana pa beti imeneyi ndi Even.


Msika uwu umapezekanso kwa ma seti ena.


Total Sets - Over/Under - FT

Loselani ngati kuchuluka kwa ma seti omwe aseweredwa kudzakhala kochulukirapo kapena kuchepera kuposa momwe atsimikizila. Chonde dziwani kuti masewerawa akuyenera kufikira kumapeto kuti msikawu ukhazikitsidwe.


Chitsanzo (Example 1)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Ngati zotsatira zomaliza zamasewera zinali 6-4 6-4, tinali ndi ma seti a 2 okha omwe adaseweredwa ndikusankha “Under 2.5” ndiyo pambana.


Chitsanzo (Example 2)

Nadal adapambana seti yoyamba 6-4. Djokovic adapambana seti yachiwiri 6-4. Zotsatira ndi 3-3 mu seti yachitatu ndipo Nadal adaima pamasewelawa. Pamenepa tiyimitsa msikawu chifukwa masewerowa sanathe ngakhale ali kale mu seti yachitatu.

Any Set Winner Home/Away - FT

Loselani ngati wosewera Wapakhomo kapena Obwera apambana seti iliyonse. Setiyi iyenera kumalizidwa kwathunthu kuti beti yathu ikhale kuti yatheka.


Chitsanzo (Example)

Rafael Nadal v Novak Djokovic

Tiyeni tione kuti zotsatira zomaliza zinali 6-3 5-7 3-6, Mukadakhala ndi kuti mwa beta pa seti inailiyonse - Home“ mwapambana, chifukwa Nadal adapambana seti imodzi, koma sadapambane masewera ndi 1-2. Wosewera wa timu yapakhomo nthawi zonse amakhala wosewera kapena timu yomwe imalembedwa koyamba mu dzina lamasewera.


Win to Nil Any Set - FT

Loselani ngati seti iliyonse idzatha 6:0 kapena 0:6. Setiyi iyenera kumalizidwa kwathunthu kuti beti ikhale kuti yatheka.


Tiebreak in Any Set - FT

Loselani ngati padzakhala Tiebreak pamasewerawa.


Msika uwu umapezekanso pama seti ena.


Virtual Football (Soccer) Betting Rules, Bet Types & Resulting Rules

Zotsatira zamasewera a Virtual Football zimapangidwa pogwiritsa ntchito kuwerengera kothekera kwa zotsatira zomwe zikuchitika kutengera mphamvu zamagulu a Virtual omwe akutenga nawo gawo. A Random Number Generator (RNG) imagwiritsidwa ntchito kuti adziwe zotsatira zochitika pamwambo uliwonse wamasewera. Izi zikutsimikizira kuti zotsatira zamasewera amodzi sizikhudza masewera otsatira ndipo zotsatira zake zimasiyana, ngakhale Ma Virtual Team omwewo atasewera kangapo.


Cancelled Matches

Zochitika zosayembekezereka zitha kuchititsa kuti Virtual Match yomwe inakonzedwa kuti iyambe isayambitsidwe. Izi zikachitika, kubetera konse pamasewerawo kudzathetsedwa.


1X2 - Full Time

1X2,omwe umatchedwanso zotsatira zampira kapena 3-way, ndi msika wotchuka kwambiri pakulosera mpira. Cholinga ndikulosera zotsatira za masewerowo pakatha nthawi yokhazikika.


Zosankha

1 - Team yapakhomo.

X - Fanana mphamvu

2- Team yobwera


Chitsanzo:

RMA v BAR

Ngati zotsatira zomaliza zili 1 - 2, zopambana zizakhala kusankha 2 chifukwa BAR idapambana.


Over/Under - Full Time

Loserani ngati padzakhala zigoli zochuluka kapena zochepa kusiyana ndi chiwerengero chomwe chaperekedwa m’musichipa pakatha nthawi yokhazikika.


Zosankha

Over x.5 : Zigoli zikhala zochuluka kuposa zoperekedwa.

Under x.5: zigoli zikhala zochepera kuposa zoperekedwa.


Chitsanzo:

RMA v BAR

Ngati zogoli zikhale 1 - 2, kulosera kulondola ndi Over 2.5 Chifukwa zigoli zitatu zagolesedwa ndipo ndizodusa 2.5.


Double Chance - Full Time

Msika omwe chisankho chimodzi chimakhudza zotsatira ziwiri, ndipo zimachulukitsa mwayi owina kusiyana ndi msika 1X2 pawokha. Loserani zotsatira posankha pamodzi pomwe pali zotsatira ziwiri za nthawi yokhazikika.


Zosankha

1X - Timu yapakhomo ipambana kapena matimu afanana mphamvu

X2 - Timu yobwera ipambana kapena matimu afanana mphamvu

12 - Timu yapakhomo kapena yobwera ipambana.


Chitsanzo

RMA v BAR

Tiyerekeze mpira wathera 1- 2, zisankho zolondora ndi X2 ndi 12 chifukwa BAR yapambana masewerawo. Zigoli zikakhala 1 - 1,zisankho zolondora ndi 1X komanso 2X chifukwa kufanana mphamvu (X) kukupezeka muzosankhazo.


Half Time/Full Time

Loserani zotsatira za 1x2 za theka loyamba. Loserani zotsatira za 1x2 zamasewera onse. Gwiritsani ntchito kusankha kumodzi kuti muyike kubetera komwe kumaphatikiza zolosera zonse ziwiri.


Kuti chisankhocho chikhazikitsidwe ngati wopambana maulosi onse ayenera kukhala olondola. Ngati theka loyamba kapena kulosera kwamasewera onse kuli kolakwika ndiye kuti kusankha kudzathetsedwa ngati kutayika.


Mawonekedwe ogwiritsidwa ntchito pofotokozera kuphatikiza kosankhidwa ndi HT/FT. Kusankhidwa kwa 1/X kumatanthauza kuti timu yapakhomo (1) ipambana mu theka (HT) loyamba ndipo ma timu afanana mphamvu (X) mu nthawi yonse (FT).


Zosankha:

1/1: Yapakhomo / Yapakhomo

1/X: Yapakhomo/Fanana mphamvu

1/2 : Yapakhomo/Yobwera

X/1: Draw/Yapakhomo

X/X : Fanana mphamvu / Fanana mphamvu

X/2 : Fanana mphamvu / Yobwera

2/1: Yobwera / Yapakhomo

2/X : Yobwera / Fanana mphamvu

2/2 : Yobwera / Yobwera


Chitsanzo

RMA v BAR

HT 0-0

FT 1-2


Kusankhidwa kopambana kungakhale X/2 pa chitsanzochi chifukwa theka loyamba (HT) ma timu afanana mphamvu ( Draw) ndipo mu nthawi yonse timu yobwera (2) ndiye yapambana.


Both Teams To Score - Full Time

Mu msika umenewu (BTTS, Gol/Gol) mungathe kulosera ngati matimu onsewa apeze chigoli chimodzi kapena ayi panthawi yokhazikika (FT).


Zosankha:

Yes (Inde) - Matimu onse apeza chigoli, zomwe zimafunikira kuti zigoli ziyambire 1-1

No(Ayi) - Timu imodzi ndiyomwe igoletse kapena masewera athera 0-0


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira zomaliza ndi 1-2, kusankha kopambana kungakhale Yes (Inde), chifukwa magulu onsewa adapeza chigoli chimodzi pamasewerawo.


eFootball (Soccer) Betting Rules, Bet Types & Resulting Rules

Mu dziko la masewera a pa kompyuta otchedwa virtual sports, eFootball imadziwika kuti ndi imodzi mwa magawo osangalatsa komanso akukula mofulumira kwambiri. Pa mpikisano uliwonse, osewera awiri enieni amapikisana pa masewera a pa kompyuta odziwika bwino a mpira. Nthawi zambiri ndi FIFA, kutsanzira mpira weniweni omwe ukuseweredwa nthawi yomweyo. Masewerawa amachitika mofulumira ndipo ali ndi mpikisano waukulu komanso amatsatira malamulo ndi kapangidwe kampira weniweni.


Cholinga chathu ndi kuonetsetsa kuti zinthu zonse zikuyenda mwachilungamo, momveka bwino, komanso mosavuta kuti muzisangalala ndi kubetera nthawi iliyonse.


Pokhapokha ngati atanena mosiyana, misika yonse yamasewera (match markets) imadalira zotsatira za nthawi yomalizira yosewera (regular time). Izi zikuphatikizapo nthawi iliyonse yowonjezera ya kuvulala kapena kuimitsa masewera (injury or stoppage time). Nthawi yowonjezera (Extra time), chilango cha ma penate, sizidzawerengedwa pa kukhazikitsa zotsatira za misika ya nthawi zonse (regular time markets)

Cancelled Matches

Kubetera kudzakhala kosavomerezeka ngati masewera a eFootball omwe adakonzedweratu nthawi yoseweredwa akanika kutero pazifukwa zilizonse.

Interrupted/Abandoned Matches

Ngati mpira wasokonezeka kapena kuimitsidwa panjira pa zifukwa zilizonse ndipo suyambiraso ndikumalizika mkati mwa maola 24 (24 hours), kubetera konse komwe zotsatira zadziwika kale (monga 1st half) zimavomerezeka. Mabeti okhala ndi masewera amodzi, adzakhala opanda kanthu ndipo ndalama yobetera(stake) idzabwezedwa. Ngati beti yanu ili ndimasewera ochuluka, idzakhala yovomerezeka ndipo masewera okhudziwa adzachosedwa pakubetera kwanu.

Incorrectly Listed Fixtures

Ngati masewerawa alembedwa molakwika (matimu olakwika), kubetera konse kwa masewerawo sikudzakhala kosavomerezeka.

1X2 - Full Time

1X2 amatchedwanso zotsatira za mpikisano (Match Result) kapena 3-way, ndipo ndi msika wodziwika kwambiri pakubetera kwa mpira. Cholinga chake ndikulosera zotsatira za mpikisano ikatha nthawi yosewera (regular time).


Zosankha:

1 - Timu yapakhomo (Home)

X - Fanana mphamvu (Draw)

2 - Timu yobwera (Away)


Chitsanzo:

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira zomaliza ndi 1-2, zotsatira zopambana ndi kusankha 2, chifukwa Barcelona idapambana masewerawo.


1X2 - First Half

Loserani timu yomwe idzapambane theka loyamba la masewerawa.


Zosankha:

1 - Timu yapakhomo (Home)

X - Fanana mphamvu.

2 - Timu yobwera (Away)


Over/Under - Full Time

Loserani ngati padzakhala zigoli zambiri kapena zochepa kuposa zomwe zaperekedwa panthawi yokhazikika.


Zosankha

Over x.5 (Kuposa x.5) - Padzakhala zigoli zochuluka kuposa mwayi wobetera womwe waperekedwa.

Under x.5 (kuchepera x.5) - Padzakhala zigoli zochepa kuposa mwayi wobetera womwe waperekedwa.


Chitsanzo

Real Madrid v Barcelona.

Ngati zotsatira zomaliza zinali 1 - 2 kusankha kopambana kwa zigoli ndikwa Over 2.5(Posera 2.5) chifukwa zigoli zitatu zidagolesedwa zomwe ndi zopitilira 2.5.

Over/Under - First Half

Loserani ngati padzakhale zigoli zochuluka kapena zochepa kuposa zomwe zaperekedwa mu theka loyamba (HT).


Zosankha

Over 1.5 (Kuposa X.5) : Padzakhala zigoli zoposa mwayi obetera omwe waperekedwa.

Under X.5 (Kuchepera X.5): Pazakhala zigoli zochepera mwayi omwe waperekedwa.


Msika umenewu umapezekaso pa theka loyamba (1st half).


Over/Under - HOME - Full Time

Loserani ngati timu yobwera ingagoletse zigoli zoposa kapena zochepera mwayi omwe waperekedwa panthawi yokhazikika.


Zosankha.

Over x.5 (Kuposa x.5): Padzakhala zigoli zoposa mwayi obetera omwe waperekedwa.

Under x.5 (Kuchepera x.5) - Padzakhala zigoli zochepera mwayi obetera omwe waperekedwa.


Msika umenewu umapezekaso pa theka loyamba (1st Half)


Double Chance - Full Time

Msika omwe chisankho chimodzi chimakhudza zotsatira ziwiri, ndipo zimachulukitsa mwayi owina kusiyana ndi msika 1X2 pawokha. Loserani zotsatira posankha pamodzi pomwe pali zotsatira ziwiri za nthawi yokhazikika.


Zosankha.

1X - Timu yapakhomo ipambana kapena matimu afanana mphamvu

X2 - Timu yobwera ipambana kapena matimu afanana mphamvu

12 - Timu yapakhomo kapena yobwera ipambana.


Chitsanzo.

Real Madrid v Barcelona

Ngati zotsatira zomaliza zinali 1-2, zosankha zopambana zikanakhala X2 ndi 12, chifukwa Barcelona idapambana mpikisanowo. Ndipo zigoli zikanakhala 1-1, zosankha zopambana ndi 1X ndi X2, chifukwa mwa zosankhazi mulinso kufanana mphamvu(X - draw) kwa matimu.


Miska umenewu mapezekanso pa theka loyamba (1st Half)

2-Way Handicap - Full Time

2-way handicap ndi msika wolosera timu yomwe idzapambane masewera pa nthawi yokhazizika(regular time) timu yomwe mwasankha ikaonjezeredwa kapena kuchoseredwa mwayi. Nthawi yowonjezera (Extra time) ndi mapenate siziwerengedwa.


Chitsanzo:

1 1.56 barcelona ali ndi -0.5

2 2.65 Real Madrid ali ndi +0.5


Tiyerekeze mpira wathera 2 -2 kusonyeza kuti matimu afanana mphamvu(draw). Ngati munabetera pa Real madrid @ 2.65, + 0.5 yiphatikizidwa ku zigoli za Real madrid (2 + 0.5) ndipo Real Madrid ipambana chifukwa zigoli zikhala 2 - 2.5 (2 - 3).


Msika wa 2-Way Handicap umapezekaso pa theka loyamba (1st Half ) komanso pa theka lachiwiri (2nd Half.)

3-Way Handicap - Full Time

3-way handicap omwe umatchedwaso European handicap ndi msika wobetera womwe mungalosere timu yomwe idzapambane masewera pa nthawi yokhakika(regular time), timu yomwe mwasankha ikaonjezeredwa kapena kuchoseredwa mwayi. Nthawi yowonjezera (Extra time) ndi mapenate siziwerengedwa


Chitsanzo:

1 2.25 Barcelona ali ndi -1.0

X 3.60 Fanana mphamvu -1.0

2 2.65 Real madrid ali ndi +1.0


Chitsanzo #1

Tiyerekeze mpira wathera 2 -2 kusonyeza kuti matimu afanana mphamvu(draw). Ngati munabetera pa Real madrid @ 2.65, + 1.0 yiphatikizidwa ku zigoli za Real madrid (2 + 0.5) ndipo Real Madrid ipambana chifukwa zigoli zikhala 2 - 2.5.


Chitsanzo #2.

Tiyerekeze mpira wathera 2 -2 kusonyeza kuti matimu afanana mphamvu(draw). Ngati munabetera pofanana mphamvu (draw) @ 2.65, -1.0 ichoseredwa ku zigoli za Barcelona (2-1) ndipo beti sipambana chifukwa zigoli zikhala 1 -2.


Msika umenewu umapezekaso pa theka loyamba(1st Half)


Draw No Bet - Full Time

Uwu ndi msika umene umatchedwanso 12 kapena Moneyline, momwe mungathe kulosera za opambana pamasewera popanda kusankha za kufanana mphamvu (draw). Izi zikutanthauza kuti matimu akafanana mphamvu, mudzabwezeredwa ndalama zanu zomwe munabetera. Ndipo mukazabetera masewera ochuluka pakamodzi,beti yanu izakhala yovomerezeka koma masewera okhudzidwawo azachosedwapo.


Msika uwu umapezeka pa nthawi yonse yamasewera(Full time), theka loyamba(1st half), ndipa theka lachiwiri (2nd half).


Zosankha

1 - Timu yapakhomo ipambana

2 - Timu yobwera ipambana


Chitsanzo

Real Madrid - Barcelona

Tiyerekeze mpira wathera 1 -2, ngati munasankha Barcelona ndiye kuti mwapambana. Ngati mpira wathera 1 - 1, ndalama zomwe munabetera (Stake) zimabwezedwa.

Home/Away No Bet - Full Time

Msika umenewu umatchedwanso 12 kapena moneyline ndipo mumalosera opambana popanda kusankha kufanana mphamvu(draw). Izi zikutathauza kuti matimu akafanana mphamvu mudzabwezeredwa ndalama zomwe munabetera (stake). Ngati beti yanu inali ndi masewera ambiri omwe akhudzidwa adzakhalabe ovomereka koma masewerawo azachosedwa pa pepala lanu lobetera(betslip).


Away No Bet ndi mtundu wa msika wopatula kupambana kwa timu yobwera pa misika ya mitundu itatu (1X2). Ndipo umakulorani kubetera pakufanana mphamvu (x) komanso kuti timu yapakhomo ipambana. Ngati timu yobwera yapambana, ndalama zanu zimabwezedwa.


Home No Bet - X: Zikutanthauza kuti matimu akafanana mphamvu (draw), mwapambana beti yanu. Ngati timu yapakhomo yapambana (Home), ndalama zanu zimabwezedwa ndipo ikapambana timu yobwera(Away) beti yanu imakhala yosapambana.


Home No Bet - 2: Zikutanthauza kuti timu yobwera ikapambana(Away),beti yanu yawina. Ngati timu yapakhomo yapambana (Home), ndalama zanu zimabwezedwa ndipo matimu akafanana mphamvu (X) beti yanu imakhala yosapambana.


Away No Bet - X : Zikutanthauza kuti matimu akafanana mphamvu (draw), mwapambana beti yanu. Ngati timu yobwera yapambana (Away), ndalama zanu zimabwezedwa ndipo ikapambana timu yapakhomo (Home) beti yanu imakhala yosapambana.


Away No Bet - 1: Zikutanthauza kuti timu yapakhomo ikapambana (Home), mwapambana beti yanu. Ngati timu yobwera yapambana (Away), ndalama zanu zimabwezedwa ndipo matimu akafanana mphamvu (Draw), beti yanu imakhala yosapambana.

Odd/Even - Full Time

Loserani ngati padzakhala zigoli zomwe zingatheke kugawika ndi 2 (even) kapena ayi (Odd). Chonde dziwani kuti “0” amatengedwa ngati otheka kugawidwa ndi 2 (even). Tiyerekeze mpira wathera 0 - 0 kusankha kopambana ndikwa “even”


Zosankha

Odd - Zigoli zikhala zosatheka kugawidwa ndi 2.

Even- Zigoli zikhala zotheka kugawidwa ndi 2.


Chitsanzo

Real Madrid v Barcelona.

Tiyerekeze mpira wathera 1- 2, kusankha kopambana ndikwa “odd” chifukwa tikaphatikiza zigoli zonse zikwana zitatu(3) ndipo 3 sangatheke kugawidwa ndi 2.

Total Goals Exact Home/Away - Full Time

Loserani chiwerengero cha zigoli zomwe zigoletsedwe mu mpira. Zigoli 10+ zikutanthauza kuti padzakhala zigoli 10 kapena kupitilira apo zomwe zigoletsedwa.


Zosankha

0 - Sipapezeka chigoli

1 - Papezeka chigoli chimodzi(1)

2 - Papezeka zigoli ziwiri(2)

3 - Papezeka zigoli zitatu(3)

4 - Papezeka zigoli zinayi(4)

5 - Papezeka zigoli zisanu(5)

10+ - Papezeka zigoli khumi(10) kapena kuposera apo.


Back to top
Not logged in-Join NoworLogin