Uthengawu ulinso mu Chingerezi

MALONJE

1.1 Uwu ndi mgwirizano pakati pa inu monga  kasitomala wa betPawa ndi kampani ya betPawa  pa ndondomeko komanso malamulo amene azitsatidwa pa china chili chonse chokhudza andi kabetedwe ku kampani ya betPawa.  


1.2 Mgwirizanowu uzakhala m’malo ndipo uzatsatidwa nthawi zonse pamene mukubeta ndi kampani ya betPawa. Kampani ya betPawa uli ndi ufulu komanso umwini wogwilitsila zinthu monga chizindikilo cha kampani , tsamba komanso dzina la betPawa ndi zina zambiri.


1.3 Chonde welengani ndikunvetstsa mgwirizanowu komanso ndondomeko zimene zimatsatidwa  musadpitilire kutsegula akaunti ndi kampani ya betPawa.


MAWU OYENELA KUDZIWA

Kasitomala/ Inuyo munthu wina aliyense amene  anatsegulitsa komanso amagwilitsila ntchito tsamba la Kampani ya betPawa.


Kampani “ife” akuyimila kampani ya Kuwina Limited yomwe ili idalembetsedwa mkaundula wa ma kampani  m’dziko muno motsatila malamulo a dziko ma Malawi  ndipo ndiyovomelezeka ndi boma  ndi nambala ya kampani iyi COYR-A5K1EK8 and TMBRS 1011959, imene imagwilira nchito  pa address lokhazikika komanso lovomelezeka la Avalon Office Park Building, P.O Box 140,  mu Mzinda wa Blantyre, ku Malawi.


Dziko  likuyimila  dziko la Malawi


Zosayenela Kuchita zikuyimimila zonse zi mene zafotokozeledwa mu gwilizanowu mu gawo lachisanu nd chimodzi


PSP Njira Zolipilira Ndalama kudzela mwa anthu apambali ngati a Airtel kudzela ku Airtel money komanso Mpamba kudzela ku TNM 


Azamalamulo Nthambi yokhazikika ya boma yoyan’ganila za kabetedwe komanso mayele yowonetsetsa kuti ndondomeko zonse zokhudzana ndi mabetedwe komanso mayele zikutsatidwa moyenelela malingana ndi malamulo


Masewela onse a mipira komanso ma game osiyana amene ametengela mwayi kuti munthu achite mphumi amene amapezeka pa tsamba la betPawa.


Wazamasewelo aliyense amene amatengapo gawo pa masewelo antundu wina uli wonse  kapena amathandizila za masewelo anundu wina uli monga  ena ali onse aphunzitsi a mpira, oyan’ganila ma timu, oyimbila mpira wa manja komanso wa miyendo komanso wina aliyense otengapo gawo pa chilichonse chokhudzana ndi masewelo apachinzake kapena a mpikisano


Ndondomeko Zotsatidwa Izi ndi chili chonse chimene chalembadwa mu mgwirizanowu chimene kasitomala komanso ifeyo tizatsatila pogwilitsa tsamba la betPawa, zomwe zili m’mene timagwilitsilira ntchito zomwe mwagawana nafe zokhudzana ndi inu monga kasitomala, malamulo obetela mipira, malamulo a masewelo a mayele, a mipira   yoyendetsedwa nd makina a komputa komanso ndondomeko yoyendetsela mipikisana ina ili yonse ndizimene zimamanga mgwirizanowu.


Tsamba la inteneti limayimila tsamba la betPawa  kuphatikizapo lap phone la betPawa lokazikika(application) http://www.betpawa.mw/


KUSINTHA MGWIRIZANO

3.1Kampani ili ndi ufulu osintha mgwirizanowu  machinunu/ chonsisi nthawi ina ili yonse ngati pali pofunikila kutelo  kuti ikhale pachilinganizo ndi malamulo komanso ndondomeko zonse zoyikidwa ndi awulamuliro komanso kusintha zina ndi zina za tsamba la betPawa, zimene zimapezeka pa betPawa komanso m’mene kampani imayendetsea buzinesi.


3.2 Kampani izadziwitsa ma kasitomala zakusintha kwakukulu kumene kungakhalepo kudzela pa zolengeza / zibaluwa pa tsamba la kampani. Kusintha kwa zinthu zina zin’gono zing’ono Kukhozanso kuchitika  kasitomala osauzididwa  , kotelo ndi udindo wa kasitomala kumaona ngati pali zina zomwe za sinthadwa  zoti mudziwe. Ngati pangakhale kusintha kwina kuli konse, kasitomala akuyenela kuchonga ndi kuvomeleza mgwirizanowu asadapitilire kugwilitsa ntchito tsamba la betPawa.


ZOMUYENELEZA KASITOMALA MALINGANA NDI MALAMULO

4.1 Potsegulitsa akaunti ya betPawa, mukuvomeleza ndi kutsimikizila kuti:


4.1.1 Munakwanitsa zaka 18 kapena kupitilira apo


4.1.2 Zina zili zonse zokhudzana ndi komanso ma lipoti onse ndi owona


4.1.3 Maganizo aubongo oyenela bwino komanso muli ndikuthekela kolowa mu mgwirizanowo


4.1.4 Simunaletsedwe kupanga zobeta pa masamba a intaneti kapenanso ma shop obeta


4.1.5 Kutsimikizila kuti ndalama zimene mukupanga deposit ku akaunti ya betPawa ndi zanu komanso kuti simukugwilitsila ntchito ndalama zochokela ku zaupandu komanso zosavomelezeka ndi boma


4.1.6 Simukupanga deposit ndalama kudzela munjira yosayenelela yoti sili mu dzina lanu olo siyanu


4.1.7 Simukupanga deposit ndalama kudzela mu amkhala pakati ena alionse kapena kulandira ndalama kudzela mu amkhala pakati kapenanso bizinesi


4.1.8  Mukunvetsetsa komanso kuvomeleza mgwirizanowu  kothelatu 

Monga mbali yotsegulitsa akaunti ku betPawa , muzafunikila kupeleka mayankho okhudzana ndi inu ngati munthu komanso ziphaso zovomelezeka kutithandizila kustimikizila umwini


4.2 Mukutsimikizila ndi kuvomeleza  kuti potsegula komanso kugwilitsila ntchito tsamba la betPawa mukapanga zonsezi mosakakamizidwa, mwakufuna kwanu komanso monvetstsa kuti zimatengela mwayi. Komanso kuti mukutenga ku beta nga msangulutso osati njira yokhazikika yopezela ndalama. Mukuvomeleza kuti zonsezi mukuchita mwa inu mwini komanso kuti kuchita zina zosiyana ndi mgwirizanowu ndikosaloledwa.


4.3 Povomeleza mgwirizanowu, mukovomeleza kuti mukhoza kutaya ndalama pobeta ndipo mukuvomela kuti muzavomeleza ngati zatachitika choncho. Malingana ndi chilinganizo chimenechi komanso kuvomela kwanu mukaluza, mukutsimikizila kuti simuzafuna kubwezeledwa ndalama ndi betPawa,akuluakulu  oyendetsa betPawa komanso ena onse ogwila ntchito ndi betPawa, ma agent , ma ofisala komanso amabungwe osiyanasiyana.


4.4 Potsegulitsa account komanso kugwilitsila ntchito tsamba la betPawa mukuyimilila, kuvomeleza komanso kutsimikizila kuti muzitsatila malamulo ndi ndondomeko zonse zimene zayikidwa moyenelela. Sitizazengedwa mlandu win uli onse ngati akaunti yanu ikugwilitsidwa ntchito mosayenela komanso mosemphana ndi malamulo. Polowa nafe mu/ Povomeleza  mgwirizanowu mukovomela kuti muzigwila nafe ntchito powonetstsa kuti malamumo ndi ndondomeko zimene zayikidwa zikutsatidwa.


4.5 Ndi udindo wanu kuwonetsetsa kuti mukutsatila malamulo ndi ndondomeko zimene zinayikidwa  ndi boma kuti ziziyendetsa zobeta pa masamba a intaneti komanso ma shop obetela. Sitizazengedwa mlandu m’malo mwanu ngati mwaphwanya lamulo lina liri lonse pogwilitsila ntchito akaunti ya betPawa komanso tsamba lathu.


4.6 Mukuvomelaza kuti muzatsatila mgwirizanowu nthawi zonse, ndipo kuti  pazakhala zilango ngati mwaphwanya zimene zalembedwa mugwirizanowu, zilangozo monga  kuyimitsa kugwilitsa nthicto kwa akaunti akaunti, kutsekedwa, kochotsedwa kwa ma bet amene mwayika komanso kulandidwa  kwa ndalama zoti mwawina.


KUTSEGULITSA NDI KUSAMALIRA AKAUNTI YANU

5.1 Ndalama zomwe zizatumizidwe ku bank zizatumizidwa kwa Kasitomala amene anatsegulitsa akaunti komanso amene wapempha kuti ndalama zitumizidwe. Ndipo dzina limen munthu adetsegulitsila akaunti ya Airtel money komanso Mpamba ikuyenela kukhala lofanana ndi dzina la akaunti yaku banki.


5.2Makasitimala ndi osaloledwa kugulitsa, kupeleka, kupatsila munthu olo makisitomala ena umwini wa akaunti yawo.  Ngati kampani itapeza kuti izi zachitika, kampani ili ndi mphanvu yotseka akauntiyi, kuchotsa ma beti ena ali onse amene anayikidwa komanso kusapeleka kapena kutenga ndalama zimene kasitomala anawina. Kuphatikiza apo Kamapani izatsatila ndondomeko zonse zoyenelela.


5.3 Mukalembetsa akaunti, ndi udindo  wanu kutsimikizira kuti china chili chonse chokudzana ndi zimene mwalemba komanso ziphaso ndi zonse  zimene mwapereka ndi zoyenelela komanso zilipo zokwanila. Kampani ili ndi ufulu wotseka akaunti iliyonse ngati zambiri kapena zikalata zomwe mwapereka zipezeka kuti ndi zabodza, zosakwanira, kapena zolakwika.


5.4 Akaunti iliyonse imagwirizana ndi nambala ya foni inayake, ndipo zochita zonse zokhudza akauntiyo zimagwirizana ndi nambala ya foni imeneyo. Ndalama sizingathe kusamutsidwa kuchokera ku akaunti ina kupita ku ina kapena kuchokera ku nambala ya foni ina kupita ku ina.


5.5 Mukhoza kulembetsa akaunti imodzi (1) yokha. Kampani ili ndi ufulu wotseka akaunti kapena maakaunti a kasitomala aliyense amene walembetsa maakaunti angapo m'dzina lawo, kapena m'maina osiyanasiyana, ngati ili ndi zifukwa zomveka zoganizira kuti maakaunti ambiriwa (ngakhale atakhala m'maina osiyanasiyana) adalembetsedwa ndi cholinga chonyenga kampani pofuna kubisa kuchuluka kwa zomwe wina kapena kudutstitsa mlingo wovomelezeka wa malire a kampani. Kampani ilinso ndi ufulu woletsa kapena kuyimitsa kulandira kapena kugwilitsila ntchito mu njira ina iliyonse ma account oterewa.


5.6 Mukalembetsa akaunti, muli ndi udindo wosunga chinsinsi cha zambiri za akaunti yanu ya paTsamba la kampani . Zochitika zilizonse zomwe zachitika mutaloŵa mu akaunti yanu zidzawerengedwa ngati zochita zanu. Kampani sidzakhala ndi udindo pa madandaulo alionse obwera chifukwa chakulephera kwanu kusunga kapena kuteteza zambiri za akaunti yanu, kuphatikizapo kugawana kapena kufalitsa zambiri zotere kwa wina popanda chilolezo. Kunena mwanvenvenve , kasitomala sayenera kugawana kapena kufalitsa zambiri za akaunti yawo ya pa kwa munthu wina aliyense pa zokhudza kubetcha kapena kusewera masewera. Ngati mukukayikira kuti dzina lanu kapena nambala yanu yachinsinsi ikugwiritsidwa ntchito ndi munthu wina, muyenera kuti dziwitsa nthawi yomweyo kudzela muma agent athu panjira zathu zolankhulilana.


5.7 Kasitomala ali ndi ufulu wopempha kuti akaunti yake itsekedwe mpaka kalekale kapena kuyimitsidwa kwakanthawi kochepa nthawi iliyonse popempha kudzela muma agent athu panjira zathu zolankhulilana.


5.8 Ngati pali kusintha kulikonse pa ziphaso zolembetsera, zainuyo  kapena zachuma  zokhudza akaunti yanu (monga zambiri za khadi lanu laku bank , dzina, kapena nambala ya foni), mukufunikanso kuti mutidziwitse nthawi yomweyo. Kulephera kutero kungachititse kuti zzchuma zokhudzana ndi akaunti yanu zisatheke. Pali zina zimene mukhoza kusintha nokha kudzela mu akaunti yanu koma zina ndizofunika mufikile ndi kulumikizana ndi  ma agent athu kuti mupemphe kusintha kofunikira. Kampani sidzalandira udindo uliwonse pa zochitika zoletsedwa chifukwa cha zambiri zolakwika ngati mwalephera kutidziwitsa za kusintha kulikonse kapena kupereka zambiri zolondola. Ngati njira yanu yolipirira yatayika, yabedwa, kapena yasinthidwa kukhala akaunti ya bizinesi, kapena ngati zambiri zanu zilizonse zasokonekera, muyenera kutidziwitsa nthawi yomweyo polumikizana ndi ma agent athu.


ZINTHU ZOSALOLEDWA KOMANSO ZACHINYENGO

6.1 Ngati mukukayikira kuti munthu wina akuchita zina mwa zochita zoletsedwa zomwe zafotokozedwa mu Ndime 6, mukuvomereza kuti mudachilimika ndikutidziwitsa pompo pompo polumikizana ndi  ma agent athu.  


6.2 Kutsata Malamulo Kuti Pakhale Zosangalatsa

Ndi udindo wathu kuonetsetsa kuti tsamba lathu komanso zonse zopezeka pa tsamba lathu zikubweletsa msangulutso, chitetezo komanso chimwemwe kwa ma kasitomala athu. Malingana ndi udindo umenewu, tinapatsidwa ufulu londoloza komanso kuunikila m’mene chilankhulo komanso  khalidwe losayenelela koma losavemelezeka. Ngati ziatpezeka kuti wina wagwilitsila ntchito chilankhulo kapena kahlidwe losavomelezeka, adzapatsidwa chilango choyenela monga kutsekedwa ka akaunti ya olakwayo mpaka kalekale/ Kuti isadzagwilenso ntchito. 


6.3 Tili ndi ufulu wowunika zochita zonse za makasitomala pa tsamba lathu ndi pa Ntchito zathu kuti tiwone ngati pali khalidwe lililonse loletsedwa ndi lamulo, zauchifwamba, kusakhulupirika, chinyengo, masewera osaloledwa, kuchita zoipa, zinthu zachinyengo, komanso njuga yopitilira muyezo. Zochita zonsezi ndi zoletsedwa ndipo zitha kupangitsa kuti akaunti yomwe yachita zolakwikazo ichotsedwe/ Itsekedwe nthawi yomweyo.


6.4 Zochita Zoletsedwa

Izi ndi zina mwa zochita zoletsedwa zokhudzana ndi kugwiritsa ntchito  tsamba lathu komanso zonse zopezeka ku kampani yathu:


6.4.1 Kutengelapo mwayi pogwiritsa ntchito molakwa  kuvuta kwa intaneti, kusokonekela kwa tsamba lathu, kusagwila bwinobwino kwa tsamba lathu, kuthawa kwa intaneti ndi zina zonse  mukagwilitside ntchito ka tsamba  lathu.


6.4.2 Kugwiritsa ntchito mtundu uliwonse wa luntha lochita kupanga(AI), malembo olembedwelatu ndi ena komanso zidole zopangidwa kuti zizikopela anthu.


6.4.3 Kuphwanya malamulo, kuyesa kuwononga, kapena kugwiritsa ntchito molakwika tsamba lathu , kuphatikizapo ma seva aliwonse, mapulogalamu, kapena zida zina zokhudzana ndi tsamba lathu komanso zonse zopezeka ku kampani yathu.


6.4.4 Kugwiritsa ntchito mapulogalamu kapena zida zodutsa zoletsedwa za malo a dziko kapena kubisa malo anu enieni, kuphatikizapo kugwiritsa ntchito zomwe zingachititse kuonetsa ngati muli mudziko lina(VPN).


6.4.5 Kuchita masewera oikana kuti team inayake iwine , chinyengo, kapena mgwirizano wobisa.


6.4.6 Kutenga nawo mbali, kuthandizira, kapena kulimbikitsa mtundu uliwonse wa zauchifwamba.


6.4.7 Mtundu uliwonse wa chinyengo kapena zochita zoletsedwa ndi lamulo pozembetsa ndalama kapena kugwilitsa ntchito ndalama mwachinyengo.


6.4.8 Kuchita zinthu zonyoza komanso zochotsera ndalama mobwerezabwereza.


6.4.9 Kuyesa kusokoneza Webusaitiyi ndi Ntchito zathu zilizonse kapena kunyenga njira zaukadaulo zomwe takhazikitsa kuti tiziteteza Webusaiti ndi Ntchito zathu.


6.4.10 Kugwiritsa ntchito khadi la ku banki  kapena njira ina iliyonse yolipirira yochokera ku ngongole ngati gwero la ndalama mu akaunti yanu.


6.4.11 Kutumiza ndalama ku akaunti yanu kugwilitsila ntchito Airtel money kapena Mpamba  njira yokuti sili mu dzina lanu gwiritsa ntchito njira yolipirira kaya mwachindunji, ngakhale mutakhala kuti mwapeza chilolezo kuchokera kwa eni ake a njira yolipirirayo.


6.4.12 Kugwiritsa ntchito njira yolipirira yobedwa, yochita kupanga nokha , kapena yosaloledwa ngati gwero la ndalama za akaunti yanu, kapena kuyika ndalama mu akaunti yanu zomwe zatengedwa kuchokera kuzinthu zoipa, zachifwamba, kapena zoletsedwa ndi lamulo.


6.4.13 Kuchita zachinyengo kuti mupate ma  bonasi kapena kuwina mipikisano pa tsamba lathu.


6.4.14 Kugwiritsa ntchito tsamba lathu komanso zonse zopezeka ku kampani yathu kuti mupezele phindu mwa inu nokha. 


6.4.15 Kuloleza  kapena kupereka mofuna/ kaya mwadala kapena mosadziwa, munthu wina kuti agwiritse ntchito akaunti yanu.


6.4.16 Kugwiritsa ntchito njira yolipirira yoyikira ndi kuchotsera ndalama yomwe yalemebetsedwa pansi pa dzina losiyana ndi dzina lomwe munalembetsa akaunti yanu.


6.4.17 Kuyika kapena kuchotsa ndalama kudzera mu njira yolipirira yomwe imagwirizana ndi akaunti ya kampani kapena bizinesi, kuphatikizapo mabizinesi omwe mungakhale wokhala ndi masheya okha.


6.4.18 Kukhala kapena kulengezedwa kuti mwasowa ndalama.


6.4.19 Kuchita chilichonse choopsya, chonyoza, kapena chokhumudwitsa kwa makasitomala athu, oyang'anira, ogwira ntchito, antchito a Gulu Lothandizira Makasitomala, kuphatikizapo mwayi wolankhulana pa Webusaitiyi.


6.4.20 Kupereka zambiri zabodza, zolakwika, zosakwanira, kapena zosokoneza kuti mulembetse akaunti yanu, kapena kupanga zosintha zilizonse pambuyo pake pa zambiri zoterezi zomwe ndi zabodza, zolakwika, zosakwanira, kapena zosokoneza; ndi/kapena


6.4.21 Kupereka zolemba zabodza, zolakwika, zosakwanira, kapena zosokoneza, kuphatikizapo kukwaniritsa zofunikira zathu zotsimikizira Umunthu kapena Zoletsa Kuchita Zandalama Zakuda (malinga ndi Ndime 19).


6.5 Kukusumilani ku bwalo la milandu 

Tili ndi ufulu  olondoloza ndi kutsatila ndondomeko zofunikila kuphatikizilapo kutengelani ndi kukakusumilani kubwa la milandu ngati tazindikila kuti mukupanga zinthu zosaloledwa pa tsamba lathukuphatikizapo kutseka maakaunti, kulembera ndalama, ndi kukutsegulirani  milandu. Zochita zilizonse zauchifwamba, zaupandu komanso zokayikitsa zizafikitsidwa kwa akuluakulu oyan’ganila za malamulo.


6.5 Zochitika Zamilandu: Tili ndi ufulu wochita chilichonse chofunikira ngati tikukayikira kuti pali Zinthu Zoletsedwa, kuphatikizapo kuletsa ma akaunti, kuzizira ndalama, ndi kuyambitsa milandu. Zochita zilizonse zaupandu kapena zokayikitsa zikhoza kudziwitsidwa kwa akuluakulu oyenera.


6.6 Zochita zachinyengo ndi kusamvana pa Malipiro:

Ngati tikukayikira  komanso tazindikila kuti pakuchitika zachinyengo, monga kugwiritsa ntchito njira zolipirira zomwe zabedwa kapena zinthu zina zilizonse zoletsedwa, tili ndi ufulu woyimitsa kapena kutseka  akaunti iliyonse, Kulanda komanso kukuwuzani kuti mubwenze ndalama zilizonse kapena ndalama zopambana zomwe zikugwirizana ndi zomwezo. Kuphatikiza apo, tili ndi ufulu wodziwitsa akuluakulu oyenera kapena mabungwe oyang'anira za malipiro aliwonse omwe akukayikira kuti ndi achinyengo kapena zochita zina zosaloledwa. Tikhoza kugwiritsanso ntchito mabungwe achitatu kuti abweze ndalama zilizonse zomwe zikuperewera chifukwa cha zochita zachinyengo.

Ngakhale zili choncho, sitidzakhala ndi mlandu uliwonse chifukwa cha kugwiritsa ntchito mosaloledwa ma mobile money wallets, makadi a aku bank , macard antundu  wina uliwonse,posatengela kuti eni ake a makadiwo anakanena ku polisi kuti makadi woa anabedwa kapena ayi.


6.7 Masewero Obela /Kusewela mwachinyengo : Kampani imayan’ganila nthawi ina iliyonse m’mene kasitomala akugwilitsila ntchito zonse zochitika pa tsamba lathu komanso m’mene akubetela m’mene inagfunile posadziwitsa ma kasitomala. Ngati zatsimikizika kuti mukuchita masewero osayenera komanso mukubeta mwachinyengo , Kampani ili ndi ufulu wosapeleka komanso kulanda ndalama ina iliyonse imene munthu wawina/wapeza munjira ya chinyengo komanso yosaloledwayi.


6.8 Malingana  ndi malamulo a ku Malawi, azamasewelo komanso onse audindo muzamaswelo za mtundu wina uli onse  ndiosaloledwa kuyika nawo ma bet ena ali onse a mipikisano imene amatenga nawo gawo mwa iwo okha kapena kudzela mwa anthu ena.  Kutenga gawo kudzela mwa ena kutha kukhala kepeleka upangiri wa mipikisano yochitika, m’mene matimu akhazikitsila ngodaya zawo zochitila bwino, Kuvulala kwa osewela ndi zina zambiri  zomwe zingakhudze kapena kukayikitsa zotsatira za bet/masewera zomwe ndizosadziwika kwa anthu ena onse. 


Ngati lamuloli laphwanyidwa, Kampani ili ndi mphanvu yotseka akaunti pompo pompo mpaka kalekale komanso kusapeleka ndalama ndi ma basela amene kasitomala wawina potsatila ndondomeko zosavomelezekazi. 


6.9  Pamene pazochitika pomwe ma beti angapo ali ndi kusankha kumodzi, ma beti oterowo akhoza kuganiziridwa ngati beti imodzi. Zikachitika izi, ma beti onse, kupatula beti yoyamba yomwe idayikidwa, akhoza kuonedwa kuti ndi opanda pake. Mwachitsanzo, izi zikhoza kugwira ntchito pazochitika pomwe kusankha kwina kumaphatikizidwa mobwerezabwereza mu ma beti angapo pamodzi ndi zosankha zina zotsika mtengo.


6.10 Pazochitika pomwe pali umboni wa ma beti angapo, aliwonse okhala ndi zosankha zofanana kapena zofanana kwambiri, atayikidwa ndi kapena m'malo mwa munthu mmodzi, gulu la anthu, kapena gulu la anthu, Kampaniyo ili ndi ufulu wochotsa ma beti oterowo.


6.11 Ngati mwakhala mukuchita nawo zochita za kubetcha ngati katswiri, kapena limodzi ndi Makasitomala ena ngati gawo la kalabu, gulu, kapena gulu lofanana, kapena mwayika ma beti m'njira yogwirizana ndi Makasitomala ena omwe akukhudza zosankha zofanana kapena zofanana kwambiri, Kampani ili ndi ufulu, kutengera kusankha kwake kokha, kuchepetsa ndalama zonse zomwe zingaperekedwe pamodzi ndi ma beti oterowo mpaka kufika pa malire a ndalama zomwe zingaperekedwe kwa Kasitomala mmodzi. Tsambali ndi akauntiyi ndi zongogwiritsa ntchito payekha komanso zosangalatsa zokha.


6.12 Kampani idzayesetsa kwambiri kuti chidziwitso chomwe chikuwonetsedwa pa tsambali chikhale cholondola, kuphatikizapo nthawi, zotsatira, ndi malo. Komabe, ngakhale kuti akuyesetsa, Kampaniyo sidzakhala ndi mlandu uliwonse chifukwa cha zolakwika zilizonse za chidziwitso choterocho.


6.13 Kampani ili ndi ufulu woletsa malipiro ndikunena kuti ma beti pa  amene chochitika china ndi opanda pake ngati pali umboni wosonyeza kuti ufulu wa chochitikawo wagwiritsidwa ntchito molakwika, kapena match-fixing kapena kubela kwachitika. Umboni wotero ukhoza kuphatikizapo koma osati kukula, kuchuluka, kapena mawonekedwe a ma beti omwe adayikidwa ndi Kampaniyo kudzera m'njira zathu zonse za kubetcha.


6.14 Makasitomala ndi oletsedwa kwambiri kuchita nawo zochita zilizonse zomwe zikuphwanya malamulo oyenera okhudzana ndi masewera obeta, kuphatikizapo zachinyengo, ndi kugwiritsa ntchito njira zosaloledwa zolipirira.


KUKANIZA KUTSEKA NDI KUYIMITSA MA AKAUNTI

7.1 Kamapani ili ndi ufulu komanso kuthekela kokaniza kasitomala kutsegula, kuyimitsa kapena kuchotselatu ndi kutseka akaunti nthawi ina ili yonse  pa chifukwa china chili chonse osamudziwitsa kasitomala ngati atafuna kutelo.


7.2 Mukuvomeleza kuti Kampani ili ndi ufulu opanga chiganizo payokha osakufotokozelani zifukwa zimene zingapangitse kuti musatsegulitse akaunti, akaunti yotsegulidwa kale ichotsedwe, iyimitsidwe kapena isagwilenso ntchito.   


7.3 Ngati Kampani yapanga chiganizo kuti akaunti yotsegulidwa kale ichotsedwe, isagwilenso ntchito kapena iyimitsidwe kaye, tizakhala ndi ufulu wo:


7.3.1 Ufulu wosapeleka ndalama zina zili zonse  zomwe mumayenela kulandira, monga zomwe munayika, zomwe zimayenela kubwenzedwa, ma basela/bonasi,ndalama zaulere/ zongopatsidwa, ngongole, ndalama zowinidwa ndi zina potsatila malamulo amen anayikdwa.


7.3.2 Kuyika ndondomeko zoyenelela kutsatidwa kuti mugwilitse ntchito komanso kulondoloza  akaunti komanso tsamba lathu ngati pangakhale pofunikila kutelo.


7.3.3 Polowa mgwirizanowu mukuvomeleza kut kampani ili ndi ufulu opeleka zambiri zokhudzana ndi inuyo kwa akuluakulu oyang’anila za malamulo ngati akaunti yanu yotsegulidwa kale yachotsedwa, yasiya kugwila ntchito kapena kuyimitsidwa kamba ka mchitidwe wozembetsa ndalama kapenanso mchitidwe wina wasaloledwa  wachinyengo.


7.4 Mukuyenela kufikila ma agent athu , ngati mungasankhe kuti akaunti iyimitsidwe kwa kanthawi. Munyengo imeneyi kuzakhala kosatheka kugwilitsila ntchito  komanso, kutulutsa ndalama zanu koma ndalama ili yonse yatsala izakhalabe ku akaunti yanu ya betPawa. Ngati mungapepephe kuti akaunti yanu iyambilenso kugwila ntchito, Izayambilanso kugwila ntchito kutengela ndondomeko komanso mgwirizano umene uzakhale ukutsatidwa nthawi imeneyo.


7.5 Kampani ili ndi ufulu woyimitsa akaunti yanu kuti isagwilenso  ntchito  kwakanthawi ngati ikukhulupilira kuti mwachita zimene zili zoletsedwa , zosayenela komanso zachinyengo. Pa nthawi  kampani ikuchita kafufukufuku wake  akaunti yanu sizagwila ntchito. Kuphatikizapo kampani izakhala ndi  ufulu komanso udindo okufunsani kuti mupeleke ziphaso ndi  zina zambiri  zothandizila kafukufuku ameneyi. Pomaliza pa kafukufukuyu ngati kapani Yakhutila ndizotsatilazo kuti panalibe zosayenela , akaunti izabwezeletsedwa nkuyambanso kugwila ntchito. Koma ngati zotsaila zasonyeza kuti munapanga mchitidwe wa wosayenela wina uli wonse, akaunti yanu izatsekedwa pompopompo. Ngati zapezeka kuti ndinu olakwa, zambiri zokhudzana ndi inu zizapelekedwa kwa akuluakulu oyang’anila komanso ena onse okhudzidwa . Chonde dziwani kuti panthawi imene akaunti yayimitsidwa,  kudzakhala kosatheka kugwilitsa ntchito ndalama zimene zingakhale mu akaunti yanu. Ndalama ina iliyonse imene ingakhale mu account mwanu idzasungidwa mpakana kafukufuku atatha.


7.6 Kampani  ili ndi ufulu woletsa kasitomala kugwilitsa ntchito akaunti mwa nthawi pang’ono kapena mpaka kalekale ngati pali kofunika kutelo potsatila lamulo komanso ndondomeko zimene zinayikidwa malingana ndi Chilolezo(lisensi) yoyendetsela kampani.


7.7 Kampani ili ndi ufulu ochotsa / kutsekelatu akaunti yanu  imene ili mu dzina lanu ndi nambala yanu ya chinsinsi ngati mwaphwanya malamulo kapena ndondomeko ina ili yonse pa tsamba lathu imene yayikidwa mu mgwirizanowu


7.8 Mukuvomeleza kuti Kampani sizakhala ndi undindo wina uli wonse wokudziwitsani zakutsekedwa kwa akaunti yanu isanapange chiganizo chimenchi.


7.9 Kampani ili ndi ufulu komanso mphanvu yoletsa kasitomala kugwilitsila ntchito tsamba lathu , ngati zili choncho kampani ili ndikuthekela kokaniza kasitomala kuyika kapena kuchotsa ndalama mu akaunti yanu. Kuchotsedwa kwa ndalama zotsalira mu akaunti yanu kudzaloledwa pokhapokha ngati munthu waphwanya malumulo komanso ndondomeko wa mgwirizanowu. Ngati akaunti yatsekedwa kamba koti munthu waphwanya kapena sadatsatile mgwirizanowu, kamoani ili ndi mphanvu yosapeleka ndalama zotsalira mu akaunti. Izi zizatsatidwanso ndi ma bet ena aliwonse amene Kasitomala wawina.


7.10 Muli ndi ufulu otseka akaunti yanu nthawi ina ili yonse mutafuna pofikila ma agent athu.


7.11 Pamena mwasankha kutseketsa akaunti yanu, ndalama ina iliyonse imene yatsala mu akaunti yanu idzabwenzedwa kwa inu kupatula pamene malamulo akutilola kuti tisapeleke kaye ndalama  za ma bet amene munayika amene sanaseweledwe pa nthawi imene mukutseketsa akaunti yanu. Ngati mukutseka akaunti nthawi yoti ma bet/ mipila ina sinaseweledwe, mukuyenela kuchotsa ndalamayo popanga cashout kapena kuvomeleza kuti simulandira ndalamayo. Ma bet onse oyikidwa sadzapitilira ngati mwatseka akaunti yanu.


7.12 Ngati mwakhala nthawi yaitali imene ili miyezi 12 kupita kutsogolo osagwilitsila ntchito akaunti yanu munjira yoyika kapena kuchotsa ndalama komanso kusayika ma bet, Kampani ili ndi mphanvu yokulipilitsani chindapusa kapena kutseka akauntiyo.


7.13 Ngati kuli koyenela kutelo mkatikati mwamasiku 30  pa miyeze 12 imene yafotokozeledwa mu ndime 7.12 m’mwambayi mutasiya kugwilitsa ntchito akaunti yanu, Kampani ili ndikuthekela kokutumizilani ndalama ina iliyonse yotsalira ku bank kapena thumba la ndalama ya phone imene mungafune.


7.12 Ndalama yobwenzedwayi, idatumizidwa ku foni nambala kapena banki  yomalizila imene munatsegulitsila akaunti  mogwilizana ndi akaunti yanu.


7.15 Ngati kuli kosatheka kutumiza ku nambala kapena banki imene munalembetsela komaliza, ndalama ina ili yonse yotsalira izasungidwa motsatila lamulo komanso ndondmeko imene inayikidwa ndi adindo oyan’ganila zobeta .


KUTUMIZA NDI KUCHOTSA NDALAMA

8.1 Kasitomala atha kutumiza ndi kuchotsa ndalama mu akaunti kugwilitsila ntchito ndonomeko zokhazika zimene zilipo padakali pano pa tsamba lathu. Kampani ili ndi ufulu otsimikizila umwini wa kasitomala nthawi ina ili yonse kasitomala akatumiza kapena kuchotsa ndalama.


8.2 Kamapani imagwilitsa ntchito amakhala pakati kuti muthe kutumiza komanso kuchotsa ndalama, pachifukwa chimenechi mukuyipatsa chilolezo kampani kugwila ntchito ndi amkhala pakatiwa kuti kutumiza ndi kuchotsa ndalama kuzitheka.


8.3 Kutumiza ndi kuchotsa ndalama kutha kukhala ndi misonkho yoyikidwa ndi amkhala pakatiwa. Ndichofunikila kuti kasitomala afufuze ndikudziwa misonkho yonse yomwe amkhala pakatiwa amayika komanso kutchaja.Chonde dziwani kuti kampani simayika misonkho ina ili yonse.


8.4  Malingana ndi m’mene kampani imagwilila ntchito, kasitomala azafunikila kutumiza komanso kusunga mlingo woyenela wa ndalama kuti athe kugwilitsila ntchito tsamba lathu ndi zonse zopezeka pa tsambalo. Mukatumiza ndalama muli ndi kuthekela koyika ma bet olingana ndi ndalama imene muli nayo mu akaunti yanu.


8.5 Chonde dziwani kuti ndikosatheka kuyika betpa ngongole, makina samagwila ntchito choncho.


8.6 Kampani yathu simagwila ntchito ngati banki komanso banki nkhonde kapena kubweleketsa ndalama, ndalama ina iliyonse yopezeka mu akunti yanu simakhala ndi chiongola dzanja chapamwamba. Dziwaninso kuti Kampani simapeleka ngongole komanso kubweleketsa ndalama.


8.7 Muli ndikuthekela kochotsa ndalama zimene munayika komanso zomwe mwawina ku akaunti yanu potsatili izi:


8.7.1 Ndalama zonse zimene zalipilidwa ndikutumizidwa ku akaunti yanu zikhale zoti zitha kuchotsedwa, zokuti sizikubwenzedwa kapena zokuti munati zisatumizdwenso.


8.7.2 pakuyenela kukhala kuti tatsimikizila umwini komanso kuti simukuchita mkhalidwe wokhudzana kuzembetsa ndalama kapena kupeza ndalama mwachinyengo ndipo takhutitsidwa. Ngati mwapemphedwa kupeleka zambiri zazotsmikizila umwini komanso kyendetsedwa ka ndalama, ndipo mukutenga nthawi kupeleka mayankho, dziwani kuti pazakhalanso kuchedwa kumbali yathu pa ndondomeko yochotsa ndalama


8.7.3 komanso kuti palibe panthawi imeneyo kafukufuku wina ali yense wokhudzana ndi akaunti yanu kapena ma bet ena ali onse amene mwayika.


8.8 Chonde dziwani kuti kampani simalola kutumiza kapena kuchotsa ndalama kugwilitsila ntchito chikalata cha ku banki(cheke)


8.9 Ndalama zonse zowinidwa sizingatumizidwe, kusinthitsidwa kapenanso kuwomboledwa pa mtengo wina kupatula umene wawinidwawo.


MALAMULO OYENDETSELA MADANDO / MILANDU KOMANSO KUSEMPHANA MAGANIZO

9.1 Madando ena ali onse akuyenela kupelekedwa pompopompo kudzela kwa ma agent athu.Kampani izayesetsa kuchita chothekela kuti madando onse ochokela pa mgwirizanawo aunikilidwa ndikukonzedwa mwa chinunu.


9.2 Ngati patakhala mlandu kapena kusemphana maganizo kwina kuli konse, Kasitomala ndi kampani ikuvomela kuti makina osungila zimene zimachitika ku kampani ndi amene adzagwilitsidwe ntchito ngati gwero lenileni lopezela  umboni lokonzela dandaulo ndi kupeleka chigamulo moyenela.


9.3 Kampani ndi kasitomala akuvomela kuti ngati pangakhale kusempana maganizo pakati pa awiriwa, choyambilira kuchita chidzakhala zokabilana pakati pa mbali zonse. Kasitomala akuyenela kupeleka dandaulo lake kudzela kwa ma agent athu amene adzakudziwitseni kuti alandira mkatikati mwa masiku atatu. Kampani izaunikila dandaulolo ndikupeleka chilinganizo  mkatikati mwamasiku 5 kuchokela tsiku limene mwadziwitsidwa kuti dandaulo lafika. Ngati kasitomala sanakhutitsidwe ndi chilanganizo chime chapelekedwa , ali ndi ufulu wokandandaulanso kwina malaingana ndi ndondomeko yokhazikika yopelekela madando imene anagyipeze polakhula ndi ma agent athu.


9.4 Ngati pangakhale kuti  dandaulo lopelekedwalo silinapeze chilinganizo ku bungwe loyang’anila za madando mkatikati mwamasiku khumi ndi anayi, dandaulo litha kufikitsidwa kwa:


9.4.1 Adindo oyan’ganila za ma kampani obeta


9.4.2 Mabwalo a milandu a mdziko la Malawi amene ali ndi mphanvu zapadela zokunva komanso kupeleka chilinganizo chokhudzana ndi mgwirizanowu.


NDONDOMEKO YOLANDIRA NDIKUVOMELEZA BET

10.1 Ndi udindo wa Kasitomala aliyense kuonetsetsa ndi kutsimikizila kuti zomwe wayika pa tikita ya bet komanso ndalama yobetela ndizolondola asanayike bet. Chonde dziwani kuti ndikosatheka kusintha kapena kochotsa bet itayikidwa kale.


10.2 Bet imakhala yovomeleza pamene mwayika tikiti ndipo kampani yapeleka nambala ya tikitiyo yotchedwa betslip ID. Kampani ili ndi ufulu ndi mphanvu yokana, kovumela kapena kuvomela mbali ina ya  bet imene mwayika


10.3 Ngati kamampani yakanilatu kapena yakana mbali ina ya bet imene mwayika, ndalama imene yachotsedwayo izabwnzedwa ku akaunti ya kasitomala


10.4  Mukalandila chitsimikizo kuti bet yanu yavomeledwa, ndalama imene mwabetela izachotseledwa pa ndalama imene muli nayo mu akaunti yanu.


MALIRE A MLINGO WA NDALAMA YOBETELA

Kampani uli ndi ufulu wosintha mlingo wandalama imene mungabetele komanso imene mungawina kutiikhale yochuluka kapena yochepela motele. Ngati pangakhale kusintha kuli kunso, kusinthau kudzitikidwa pa tsamba lathu ndipo ndi udindo wa kasitomala kuwerenga ndi kuwunikilanso kusinthaku nthawi iliyonse mukalowa mu akaunti yanu.


MAVUTO OKHUDZANA NDI MAKINA

12.1 Nthawi zina pamatha kukhala vuto lotsimikizila bet kapena kuyika ndalama Kamba ka kusagwila ntchito bwino kwa makina 


12.2  Pamusipa tafotokozela nthawi imene zimenezi zikhoza  kuchitika 


12.2.1 Pamene mitengo ya ma odds imenene Kampani yapeleka/yawonetsa ili yosiyana ndi imene ilipo pa misika yosiyanasiyana


12.2.2  Pamene bet imene pali misika yosiyanasiyana yavomelezeka chifukwa chakusagwila bwino ntchito  kwa makina kapena kulakwitsa kwa munthu


12.2.3 Pomwe pali kulakwika kamba koti zotsatila zimene zinayikidwa pochonga bet kukawelengedwe ka ndalama zimene zawinidwa komanso kuyikidwa mu akaunti ya kasitomala.


12.2.4  Pomwe kutumiza kapena kuchotsa ndalama sikunapangidwe molondola


12.3 Zikachitika zomwe tafokozela pamwambapa, kamapni ili ndi mphanvu yokonza zomwe zalakwika potumiza ndi kuchotsa ndalama, kuchotsa ma bet onse amene analakwika, kuchonganso bet kugwilitila ma oddas komanso mtengo woyenela umene unalipo nthawi imene bet imayikidwa


12.4 Ngati pali kulakwika kapena kukanika kugwila ntchito kwa makina moyenelela pa nthawi imene bet imayikidwa yapangitsa kuti pakhale ma odds koma mtengo olakwika pa bet, bet yonse kapena gawo lina la bet silizawelengeledwa


12.5 Ngati tsamba lathu  kapena makina sakugwila ntchito moyenelela ,ma bet onse sadzawelengeledwa. Kampani ili ndili ufulu wosawelengela /kupeleka ndalama zowinidwa pamene makina komputa kapena oyendetsela komputayo sizikugwila ntchito bwinobwino kapena zasiya kugwila ntchito. Kampani sizazengedwa mlandu pa kuluza kumene kuzachitike mu nthawi imene makina komanso tsamba lathu silikugwila ntchito


12.6  Ngati mwachotsa ndalama pa nthawi imeneyi, mukuvomeleza kuti muzabwenza ndalamazi ngati kampani yafuna kuti mubwenze.  Ngati akaunti yanu yabwela kuti mulibe  ndalama iliyonse zitachika zotelozi, ndi udindo wanu kuwonjezela ndalama poyika ndalama ina kuti mukhale ndi ndalama. Mutalephela kutelo akaunti izayimitsidwa kapena kutsekedwa, ndipo kampani ili ndi mphavu yokuwuzani kuti muwonjzelepo ndalama yapamwamba.


12.7 Makasitomala amene adzapezeke kuti akugwilitsa ntchito kusagwila bwino kapena kusokonekela  kwa tsamba kapena makina athu mokomela iwowo kuti apeze phindu lirilonse mwachinyengo, ma akaunti awo adzatsekedwa, ndipo ndalama zimene ayika kapena kuchotsa sizizpelekedwa.


12.8 Ngati mwazindikila kapena mukukayikila kuti tsamba kapena makina athu sakugwila ntchito bwinobwino kapena pali vuto, mukuvomeleza kuti muzasiya ompmpo kugwilitsa ntchito/ kusiya kuchita zomwe mumapanga ndikulumikizana ndi ma agenti athu kuwadziwitsa za vutoli.


KUTETEZA ZINA NDI ZINA ZOKHUDZANA KAMPANI

13.1 Zizindkilo , mayina, mbendela ya kampani, zithunzi , zonvera ndi zionela, komanso zolemba zosiyanasiyana ndi zina zonse zimene Kampani yathi imagwilitsila ntchito pa tsamba lathu kapenso zochitika pa tsamba lathu ndizotetezeka ndi lamulo(copyright) ndipo zizapitilira kukhala kautndu wa kampani , eni ake a kampani komanso adindo opeleka ziphaso zoyendetsela kampani. Kotelo ndikosaoledwa kugwilitsa ntchito katundu ameneyi munjira yosintha, kumupanganso kapena kumugawa m’malo mwa kampani popanda chilolezo chilombedwa komanso chotsinikizika ndi Kampani komanso adindo opeleka ziphaso zoyendetsela kampani.


13.2  Mukulonjeza ndi kuvomela kuti muzagwilitsila ntchito katundu amene wachulidwa mu ndime 13.1 yu mwa inu nokha osagulitsa kapena kupangila ndalama ina iliyonse kamba kuti zimenezi ndizosaloledwa konse. Mukuvomelanso kuti simuzathandizila mchitidwe anthu ena apadela kukopela,  kupanganso zinthu zofanana ndi izi , kutumiza kwina, Kutulutsanso ngati zomwezi,kuwonetsa kugulu ,kugulitsa mwachinyengo, kusintha zithunzi kapenanso kupanga zangati zomwe pobela machitidwe a kampani ndi zonse zikhudzana ndi Kampani. Kuphatikiza apo, mukuvomelanso kuti simuzagwilitsila ntchito tsamba lathu pa zachitukuko, kusala ena , kugwilitsa ntchito ma makina opangidwa ndi anthu komanso nzerza makono komanso zina zikhudzana ndi luso lamakono la makina akomputa.


KUGWILITSILA NTCHITO TSAMBA LATHU MOTSATILA LAMULO

14.1 Kugwilitsa ntchito kwa tsamba lathu ndi zina zonse zokhudzana ndi Kampani yathu kutha kukhala koletsedwa kapena kosaloledwa mu mayiko ena monga dziko la America komanso mayiko ena azungu amene ali mu bungwe la European Union.  Kampani ilibe chitsimikizilo kuti tsamba lathu komanso zopezeka pa tsamba lathu ndizovomelezeka kapeza zopezekelatu ku mayiko ena.


14.2 Ndi udindo wa kasitomala aliyense kufufuza ngati malamulo a dziko limene ali   ndiowalola kugwilitsila ntchito tsamba lathu komanso zonse zopezaka pa tsambali mu dziko limene ali pa nthawi imeneyo.


14.3 Tsamba lathu lilibe mawu amene amapeleka  mwayi wopempha kapena   kuyitanila kugwilitsa ntchito tsamba lathu ndi zina zonse zopezekapo  monga kubeta  komanso  zina zochitika pa tsambali kumayiko amene amaletsa kapena salola zobeta.


ZOMWE KAMPANI INGAloLONJEZE KUKWANILITSA KOMANSO KUSAKWANILITSA

15.1 Kampani singalonjeze kuti tsamba lathu lidzagwila ntchito bwinobwino nthawi zonse popanda zovuta komanso zina zonse zopezeka pa tsambali kotelo kampani sizazengedwa mlandu olo kutenga undindo wina uli onse ngati kasitomala wakumana ndi vuto lotaya, kusachita bwino, kusapeza phindu kapena zovuta zina zimene wakumana nazo ngati tsamba lathu silikugwila bwinobwino pa nthawi yokhazikika kapena pa vuto lokugwa mwadzidzidzi lokuti Kampani ilibe mphamvu ina iliyonse malingana ndi mgwirizanowu. Kampani ili ndi ufulu woyimitsa, kuletsa komanso kuchotsa gawo kapena mbali ina ya gawo la tsamba lathu komanso zopezeka pa tsamba lathu kuphatikizapo kulankhulana ndi ma agenti athu ngati vuto lakhudza kayendetsedwe komanso nkhani za malonda.


15.2 Vuto lokugwa mwadzidzidzi limene kampani ilibe mphanvu yochitapo kanthu litha kukhala monga ngozi, moto, nkhondo, Kusowa kwa mtendere mudziko, mliri wokhudza dziko komanso mayiko ena, kukhala motalikirana malingana ndi lamulo lomwe layikidwa ndi boma, kuwonengeka kwa  makampani a njira zolumikizilana, Kuphulika kwa zinthu, Chindindindi, Kusefukila kwa madzi, Namondwe/Chiperoni, Kunyanyala ntchito kwa anthu, Kuwukila ndi zina zonse zomwe kampani ilibe mphanvu yoti itha kuchitapo kanthu zimene sinakatha kudziwa kuti zichitika, inakatha kuletsa zisanachitike komanso kuchitapo kanthu kuletsetsa kuti zisachitike.


15.3 Kampani sizazengedwa mlandu wina uli onse ngati pali kuwonongeka kwa chinthu china chili chonse koma kwabwela kamba kgwilitsila ntchito tsamba lathu ndi zina zopezeka pa tsambali kuphatikizapo zopelekedwa ndi anthu adela. Kampani sizakhalans ndi udindo kapena kuzengedwa mlandu ngati  intaneti komanso katundu wa magetsi wa kasitomala waonongeka kapena sakugwila ntchito moyenelela panthawi imene kasitomala akugwilitsila ntchito tsamba lathu.


15.4 Kampani sikulonjeza china chilichonse pa nkhani yokhudzana ndi upangiri womwe umayikidwa pa tsamba lathu moyan’ganila kuti upangiri wayikidwa nthawi yanji, ndiolondola, ndiokwanira komanso kuti pali zina zimene zachotsedwa.  Kampani sizasengedwa mlandu wina uli onse pa nkhani imeneyi.


15.5 Kumbukilani kuti ma upangiri onse ochokela kwa amkhala pakati umapelekedwa kuti ukuthandizileni kudziwa zina ndi zina komanso kugwilitsila ntchito tsamba lathu. Zonse zopezeka pamenepo zimakhala za amkhala pakatiwo osati maganizo kapena upangiri ovomelezeka  a kampani yathu. Kampani simakhala ndi mphanvu ina ili yonse kapena kuyan’ganila zimene zimayikidwa pa masamba amakampani amenewo  Kotelo kampani sizazengedwa mlandu wina uli onse ngati mwakumana ndi vuto kapena mwataya katundu olo simunachite bwino kamba ka upangiri ochokela pamasamba amenewa.


15.6 Ndi udindo wa kasitomala  kuwonetsetsa kuti mukutsatila ndondomeko zonse zozitetezela kwa zoyipa zimene zimachitika pa intaneti mukamagwilitsila ntchito  masamba ena oti si a kampani. Mukuyenela kupeza ma pologalamu othana ndi tizilombo tomwe timatha kuwononga makina a komputa mukamagwilitsila maluso amakono .  Kampani ilibe kuthekela kulonjeza kuti  masamba ochokela kwa anthu ena sangakuyikeni pa chiopyezo chiwonongeledwa katundu amene mukugwilitsila ntchito. Kampani sizazengedwa malndu wina uli onse ngati makina anu a komputa awonongeka kamba kogwilitsila ntchito masamba ena osadziteteza.


MISONKHO

Ndi udindo wanu kupeleka misonkho ina iliyonse imene mukuyenela kupeleka pa  mphoto komanso ndalama zina zili zonse zimene mwawina pogwilitsila nthicto tsamba lathu komanso zina zonse zochitika pa tsamba lathu. Kuphatikiza apo, pali misonkho ina imene kampani izapeleke m’malo mwanu potsatila malamulo amene anakhazikitsidwa okhudza misonkho. Misonkho yonse yofunika kupelekedwa ku boma, idzachotsedwa pa ndalama imene mwawina isanayikidwe mu akaunti mwanu ngati kuli kofunika kutelo. Mukuvomeleza kuti misonkho izachotsedwa pa  ndalama zomwe mungawine, ndipo ndalama zimene zizaykidwe mu akaunti mwanu ndizitsala msonkho utachotsedwa.


KUBETA MUSANAKWANITSE ZAKA ZOVOMELEZEKA

17.1 Kapani ili ndi ufulu otsimikizila zaka zakubadwa za kasitomala aliyense. Ilinso ndi ufulu woymitsa kaye akaunti ya kasitomala ngati ili ndi chifukwa chokhulupilira kuti kasimtomala sadakwanitse zaka zovomelezeka ndi boma kuti akhoza kumabeta.


17.2 Kampani izatseka akaunti ya kasitomala amene wadziwika kuti sanakwanitse zaka zovomelezeka kuti azibeta ,ndipo idzalanda kapena kusapeleka ndalama zonse zimene kasitomalayu anawina. Kubeta munthu asanakwanitse zaka zovomelezeka ndi mlandu ndipo olakwayo azapatsidwa chilango chofanana ndi mlanduwu.


KUBETA MOSAMALA KOMANSO MOTETEZEKA

18.1 Msanamila wathu pa zobeta ndikuti muzitha kupeza msangulutso , ngakhale zili choncho timdziwa kuti kubet kutha kubweletsa mavuto komanso chiopyezo pa moyo wa anthu ena. Pozindikila zimenezi, timayesetsa kulimbikitsa ma kasitomala athu kuti azibeta mosamala  pogwilitsila ntchito upangiri komanso ndondomeko zosiyanasiyana zimene tinayika pa tsamba lathu zomwe zimathandizila kugwilitsila ntchito akaunti yanu moyenelera. 


18.2 Timakulondelelani pa tsamba lathu pamene pali ndondomeko yofotokozela m’mene mungabetele mosamala komanso motetezeka.


KUTSIMIKIZILA UMWINI /MBALI YOONA ZOZEMBETSA NDALAMA/KUGWILITSILA NTCHITO  NDALAMA MWACHINYENGO

19.1 Mukolonjeza kuti zonse zomwe mwapeleka zokhudzana ndi inu potsegula kapena kupelekanso upangiri wina wokhudzana ndi inu ndiwoona komanso olondola.   Pamwamba pake mukutsimikizilanso kuti ndinu mwini wake wa ndalama zimene muziyika mu akaunti yanu pa nthawi ina ili yonse.


19.2 Mukuyipatsa Kampani komanso ena onse ogwila ntchito ndi kampani kuphatikizapo adindo oyang’anila zobeta  mphanvu  komanso ufulu wotsimikizila umwini komanso kulondola kwa zonse zimene mwapeleka mwa nthawi ndi nthawi ngati kuli kofunikila kutelo.


19.3 Mukuvomeleza kuti kwa nthawi ndi nthawi pamane takupemphani kupeleke zoonjezela zina ziri zonse pa zomwe mudapelekapo kale, mudzatipatsa zofunikila zonse kuphatikizapo za kuyika ndalama mu akaunti yanu.


19.4 Ngati kuli kofunikila kutelo pa nthawi zina, muzayembekezeka kupeleka zambiri zokhudza inu zotithandizila kutzimikizila umwini monga , chiphaso choyendela, chaunzika, kalata yosonyeza kumene mumakhala, ma bilu amene mwalipira kapenanso zina zokhudzana ndi za chuma. Kampani ili ndi mphanvu zoyimitsa  kapena kuchepetsa zimene mungapange mu akaunti yanu mpaka mutapeleka nzonse zimene mwapemphedwa kuti mupeleke.  


19.5  Ngati kampani ili ndi chifukwa chokuti ikhulupilire kuti mudapeleka zambiri za inu zabodza mwadala, kampani izakhala ndi mphanvu yosunga kaye ndalama ina iliyonse imene mwayika kapena kuwina mu akaunti yanu.


MGWIRIZANO WOKHUDZA MA BASELA/ BONANSI KOMANSO MIPIKISANO 

20.1 Nthawi ndi nthawi pa tsamba lathu pazikhala ma bonasi/basela komanso mipikisano yosiyanasiyana imene izitsatila mgwirizano komanso ndondomeko zomwe zayikidwa pa nthawi imeneyo.


20.2 Mipikisano imapezeka malingana ndi chiganizo chathu pa nthawi imene tayiyikiza ndipo chiganizo choti mukhale ovomelezeka kuchita nawo mpikisano chitha kusinthidwa pa nthawi ina iliyonse pa akaunti ina ili yonse.


20.3  Tili ndi mphanvu komanso ufulu opanga chiganizo kuti musatenege nawo gawo pa mipikisano kapena kulandira nawo ma bonasi/basela kapena mphoto zina zonse zochokela kwa kampani.


20.4 Tilinso ndi mphanvu yolkuletsani kutenga nawo gawo mu kupanag mipikisano kapena kulandila ma bonasi/basela, kuphatikizapo zomwe zinayamba kale, ngati la mulo kapena adindo oya’ganila  awona kuti ndikuyenela kutelo. Izinso ndikuphatikizilapo ngati zifukwa zakenso zikukhudaz kubeta mosamala.


20.5 Kampani ili ndi mphavu yochotsa mpikisano wina uli wonse pa tsamba lathu  nthawi ina iliyonse isadadziwitse ma kasitomala komanso osapeleka chifukwa china chili chonse.


KULENGEZA ZAKAPELEKEDWE KA MPHOTO

21.1 Pogwilitsila komanso kuwina kapena kulandira mphoto/ndalama, mukupeleka chiloloze komanso kutipatsa mphanvu ngati kampani  kuti titha kukufikilani ndi kulumikizana nanu, kuti titha kutsatsa malonda komanso kulengeza zambiri za m’mene mwawinila popanda kulandira chindapusa chili chonse kupatula pamene malamulo saloleza kutelo. Chonde dziwani kuti dzina lanu lidzagwilitsidwa ntchito pokhapokha pamene mwapeleka chikalata chopeleka chiloloze kuti titha kuligwilitsila ntchito.


21.2  Kampani ili ndi mphanvu yowulutsa komanso kuyitinila malonda kugwilitsa ntchito mlingo wina uli wonse umene kasitomala wawina pa tsamba lathu. Mu nthawi imeneyi, kasitomala owinayo atha kupemphedwa kuti ajambulidwe zithunzi komanso kanema amene atha kugwilitsa/kuzagwilitsidwa ntchito ndi kampani potsatsa malonda komanso kukopa makasitomala kusatengela nthawi komanso malo amene makasitomala a kampani angapezeke. Ndi ufulu wanu kukona kuwoneka nawo mu zithunzi kapena kanema ngati mutafuna kutelo. Ngati kungakhale kufunikila olo mutapempha ngati mwafuna, dzina lanu lizabisidwa ngati nkhani yanu ingazagwilitsidwe potsatsa malonda komanso pokopa makasitomala.


KUPEZA THANDIZO NDI AKAUNTI YANU

Kuti mupeze thandizo lina liri lonse lokhudza ndi akaunti yanu, monga kusintha nambala yanu yachinsisi,kuwona zomwe ma betela ndi zina zambiri, mutha kutsatila tsamba latu lopezela thandizo.


MALAMULO OBETELA

Kuti mupeze upangiri/zambiri  za malamulo a misika yathu,kuphatikiza za kuyimitsidwa kwa mipila , misika imene tili nayo, masewela athu a casino kuphatikizapo omwe akuchitika pompopompo komanso malamulo a masewela oyendetsedwa ndi makina a komputa pa tsamba lathu.


M’MENE TIMATETEZELA ZAMBIRI ZAMA KASITOMALA ATHU

Kuti mudziwe zambiri za’mmena kampani imapezela, kuwunikila , kusunga komanso kugwilitsila ntchito zonsezokhudzana ndi makasitomala wlengani zambiri pa tsamba lathu lomwe tinafotokozela m’mene timatetezela zomwe makatiomala amagawana nafe. 

M’mene timagwilitsila ntchito UPANGIRI WA ZOMWE MWAGAWANA NAFE


ZOMWE ZIZATSATILIDWEBE NGATI MBALI INA YA MGWIRIZANO SINGAGWILE NTCHITO MALAINGANA NDI CHIGAMULO CHA BWALO LA MAILANDU

26.1 Ngati kampani yapanga chiganizo choti mbali ina ya mgwirizanowu kapena ndondomeko zina zomwe zayikidwa mugwirizanowu  pa tsamba lathu  zisagwilitsidwe ntchito, dziwani kuti chiganizochi sichidzakhudza mbali zina zamgwirizanowu zomwe zingagwilebe ntchito komanso kugwilitsidwa ntchito , zizatsatilidwa ndithu momwe ziliri.


26.2 Chimodzomodzinso ngati bwali lamilandu kapena adindo ena ali onse apeleka chilinganizo choti mbali ina ya mgwirizanowu kapena ndondomeko zina zomwe zayikidwa mugwirizanowu  pa tsamba lathu  zisagwilitsidwe ntchito,dziwani kuti chiganizochi sichidzakhudza mbali zina zamgwirizanowu zomwe zingagwilebe ntchito komanso kugwilitsidwa ntchito , zizatsatilidwa ndithu momwe ziliri.


26.3 Zikachitika chonchi, mbali ina ya mgwirizanowu kapena ndondomeko imene yayikidwa kuti isagwile ntchitoyo, izisinthidwa potsatila lamulo loyenela molingana ndi chimene kampani imafuna kukwaniritsa pachiyambi.


UDINDO WANU

Mgwirizanowo ndi wa inu nokha ndipo simungapatse kapena kupeleka kwa munthu wina popanda chikalata chovomelezeka kuchokela kwa inu. Kampani ili ndi mphanvu komanso ufulu wogawa, kusamutsa, kapena kupatsa ena  maufulu komanso undindo womwe ili nayo kwa anthu ena apambali, ngati inuyo mwadziwitsidwa ngati pali kugawawidwa, kusamutsidwa kapenanso kupatsatsidwa kwa mgwirizanowu kwa ena . Ndipo mukuyenela kupatsidwa nthawi yoyenela kupanga chiganizo kuti mukhalabe mu mgwirizanowu ndi ena apambali kapena mufuna kuthe tsa mgwirizanowu.


Back to top
Not logged in-Join NoworLogin